< 2 Akorinto 9 >

1 Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu.
περι μεν γαρ της διακονιας της εις τους αγιους περισσον μοι εστιν το γραφειν υμιν
2 Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu.
οιδα γαρ την προθυμιαν υμων ην υπερ υμων καυχωμαι μακεδοσιν οτι αχαια παρεσκευασται απο περυσι και ο εξ υμων ζηλος ηρεθισεν τους πλειονας
3 Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera.
επεμψα δε τους αδελφους ινα μη το καυχημα ημων το υπερ υμων κενωθη εν τω μερει τουτω ινα καθως ελεγον παρεσκευασμενοι ητε
4 Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo.
μηπως εαν ελθωσιν συν εμοι μακεδονες και ευρωσιν υμας απαρασκευαστους καταισχυνθωμεν ημεις ινα μη λεγωμεν υμεις εν τη υποστασει ταυτη της καυχησεως
5 Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
αναγκαιον ουν ηγησαμην παρακαλεσαι τους αδελφους ινα προελθωσιν εις υμας και προκαταρτισωσιν την προκατηγγελμενην ευλογιαν υμων ταυτην ετοιμην ειναι ουτως ως ευλογιαν και μη ως πλεονεξιαν
6 Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.
τουτο δε ο σπειρων φειδομενως φειδομενως και θερισει και ο σπειρων επ ευλογιαις επ ευλογιαις και θερισει
7 Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.
εκαστος καθως προαιρειται τη καρδια μη εκ λυπης η εξ αναγκης ιλαρον γαρ δοτην αγαπα ο θεος
8 Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino.
δυνατος δε ο θεος πασαν χαριν περισσευσαι εις υμας ινα εν παντι παντοτε πασαν αυταρκειαν εχοντες περισσευητε εις παν εργον αγαθον
9 Paja analemba kuti, “Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka, chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.” (aiōn g165)
καθως γεγραπται εσκορπισεν εδωκεν τοις πενησιν η δικαιοσυνη αυτου μενει εις τον αιωνα (aiōn g165)
10 Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu.
ο δε επιχορηγων σπερμα τω σπειροντι και αρτον εις βρωσιν χορηγησαι και πληθυναι τον σπορον υμων και αυξησαι τα γενηματα της δικαιοσυνης υμων
11 Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.
εν παντι πλουτιζομενοι εις πασαν απλοτητα ητις κατεργαζεται δι ημων ευχαριστιαν τω θεω
12 Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu.
οτι η διακονια της λειτουργιας ταυτης ου μονον εστιν προσαναπληρουσα τα υστερηματα των αγιων αλλα και περισσευουσα δια πολλων ευχαριστιων τω θεω
13 Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense.
δια της δοκιμης της διακονιας ταυτης δοξαζοντες τον θεον επι τη υποταγη της ομολογιας υμων εις το ευαγγελιον του χριστου και απλοτητι της κοινωνιας εις αυτους και εις παντας
14 Ndipo iwowo adzakupemphererani mwachikondi chifukwa cha chisomo choposa chimene Ambuye wakupatsani.
και αυτων δεησει υπερ υμων επιποθουντων υμας δια την υπερβαλλουσαν χαριν του θεου εφ υμιν
15 Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!
χαρις δε τω θεω επι τη ανεκδιηγητω αυτου δωρεα

< 2 Akorinto 9 >