< 2 Akorinto 7 >

1 Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
ᎯᎠᏃ ᎾᏍᎩ ᏥᏄᏍᏗ ᎡᎩᏚᎢᏍᏓᏁᎸᎯ ᏥᎩ, ᎢᏨᎨᏳᎢ, ᎢᏓᏓᏅᎦᎸ ᎢᏗᎲᎾ ᏄᏓᎴᏒ ᎦᏓᎭ ᎨᏒ ᎢᎩᏇᏓᎸ, ᎠᎴ ᎢᎦᏓᏅᏙᎩᎯ, ᎢᏗᏍᏆᏗᏍᎨᏍᏗ ᏚᏳᎪᏛ ᎨᏒᎢ, ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎡᏗᎾᏰᏍᎬᎢ.
2 Mutipatse malo mʼmitima mwanu. Ife sitinalakwire munthu aliyense, kapena kuyipitsa munthu aliyense, kapena kumuchenjerera munthu aliyense.
ᏗᏍᎩᏯᏓᏂᎸᎩ; ᎥᏝ ᎩᎶ ᎤᏣᏘᏂ ᏱᏃᏨᏁᎸ, ᎥᏝ ᎩᎶ ᎠᏍᎦᎾ ᏱᏃᏨᏁᎸ, ᎥᏝ ᎩᎶ ᏲᏥᎶᏄᎡᎸ.
3 Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
ᎯᎠ ᎾᏍᎩ ᏥᏂᏥᏪᎭ ᎥᏝ ᏗᏨᏳᎪᏓᏁᏗᏱ ᏯᎩᏰᎸᎭ; ᎦᏳᎳᏰᏃ ᎯᎠ ᏥᏂᎠᎩᏪᏒ, ᏦᎩᎾᏫᏱ ᎢᏥᏯᎠ, ᎣᎦᏛᏅᎢᏍᏗᏉ ᎢᏧᎳᎭ ᏗᎩᏂᏲᎱᎯᏍᏗᏱ, ᎠᎴ ᎢᏧᎳᎭ ᎢᎦᏕᏗᏱ.
4 Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.
ᎤᏣᏘ ᎢᏨᏲᎢᏳᎭ; ᎤᏣᏘ ᎢᏨᎸᏉᏗᏍᎪᎢ; ᎠᎩᎧᎵᏨᎯ ᎤᎦᎵᏍᏗ ᎨᏒᎢ; ᎤᏣᏔᏅᎯ ᎤᎵᎮᎵᏍᏗ ᎠᏆᏓᏅᏔᏩᏕᎪ ᏂᎦᎥ ᎣᏥᎩᎵᏲᏥᏙᎲᎢ.
5 Pakuti titafika ku Makedoniya, sitinapume nʼkomwe, koma tinavutitsidwa mbali zonse. Kunja kunali mikangano, ndipo mʼmitima mwathu munali mantha.
ᎹᏏᏙᏂᏰᏃ ᏬᎩᎷᏨ, ᎥᏝ ᎣᎩᏇᏓᎸ ᎬᏩᏣᏪᏐᎸᏍᏙᏗ ᏱᎨᏎᎢ, ᎬᏩᏚᎾᏛᏍᎩᏂ ᎣᎦᏕᏯᏙᏗᎬᎩ; ᏙᏱᏗᏢ ᎠᎵᏛ ᎨᏒᎢ, ᎭᏫᏂᏃ ᎢᏗᏢ ᎣᏥᎾᏰᏍᎬᎢ.
6 Koma Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza mtima ndi kufika kwa Tito,
ᎤᏁᎳᏅᎯᏍᎩᏂᏃᏅ ᏗᎦᎵᏍᏓᏗᏍᎩ ᎤᏪᎵᎯᏍᏗ ᎤᎾᏓᏅᏔᏩᏕᎩ, ᎣᎩᎦᎵᏍᏓᏗᏍᏔᏅᎩ ᏓᏓᏏ ᎤᎷᏨᎢ;
7 sikubwera kwake kokhako, komanso mawu achilimbikitso amene analandira kuchokera kwa inu. Iye anatiwuza kuti mukufuna kundiona, zachisoni chanu chachikulu, ndi kudzipereka kwanu kwa ine, motero chimwemwe changa chinachuluka kuposa kale.
ᎥᏝᏍᎩᏂᏃᏅ ᎤᎷᏨᏉ ᎤᏩᏒ, ᎤᎦᎵᏍᏗᏍᎩᏂ ᎾᏍᏉ ᎤᏓᏅᏓᏛᎢ ᏂᎯ ᎨᏒ ᎢᏳᏍᏗ, ᎣᎩᏃᏁᎸ ᏂᎯ ᎤᏣᏘ ᎢᏣᏚᎵᏍᎬᎢ, ᎤᏲ ᎢᏥᏰᎸᏒᎯ, ᎤᏣᏘ ᏍᎩᎨᏳᎢᏳ ᎨᏒᎢ; ᎾᏍᎩ ᎢᏳᏍᏗ ᎤᏟ ᎢᎦᎢ ᎠᏆᎵᎮᎵᏨᎩ.
8 Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa.
ᎤᏙᎯᏳᎯᏍᎩᏂᏃᏅ ᎤᏲ ᎢᏨᏯᏓᏅᏓᏗᏍᏔᏅᎩ ᎪᏪᎵ ᏫᏨᏅᏁᎸᎢ, ᎥᏝ ᎤᏲ ᏯᎩᏰᎸᎭ, ᎤᏲᏍᎩᏂᏃᏅ ᎠᎩᏰᎸᏒᎩ; ᎢᏥᎪᏩᏘᏰᏃ ᎾᏍᎩ ᎪᏪᎵ ᎤᏲ ᎢᏣᏓᏅᏓᏗᏍᏔᏅᎢ, ᎠᏎᏃ ᏞᎦᏉ.
9 Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse.
ᎪᎯᏃ ᏥᎩ ᎦᎵᎡᎵᎦ, ᎥᏝ ᎠᏗᎾ ᎤᏲ ᎢᏣᏓᏅᏓᏛ ᏱᏅᏗᎦᎵᏍᏙᏗᎭ, ᏅᏗᎦᎵᏍᏙᏗᎭᏍᎩᏂ ᏗᎨᏥᏁᏟᏴᏍᏗ ᏕᏣᏓ ᏅᏛ ᎢᏴᏛ ᎤᏲ ᎢᏣᏓᏅᏓᏛᎢ; ᎤᏲᏰᏃ ᎢᏣᏓᏅᏓᏛᎩ ᎾᏍᎩᏯ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᏗᎬᏩᏓᏂᎸᎢᏍᏗ ᏥᎩ, ᎾᏍᎩ ᏅᏓᏳᎵᏍᏙᏗᏱ ᎪᎱᏍᏗ ᎡᏍᎦ ᎢᏨᏴᏁᏗᏱ ᏂᎨᏒᎾ.
10 Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa.
ᎤᏲᏰᏃ ᎠᏓᏅᏓᏗᏍᏗ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᏗᎬᏩᏓᏂᎸᎢᏍᏗ ᎨᏒ ᎦᏁᏟᏴᏍᏗ ᎨᏒ ᎣᏓᏅᏛ ᏩᎵᏰᎢᎶᎯᎭ ᎥᏓᏗᏍᏕᎸᏗᏱ ᏫᎦᎷᎩ, ᎾᏍᎩ ᎤᏲ ᎠᏰᎸᏗ ᏂᎨᏒᎾ; ᎡᎶᎯᏍᏗᏂ ᎡᎯ ᎤᏲ ᎠᏓᏅᏓᏗᏍᏗ ᎨᏒ ᎠᏲᎱᎯᏍᏗ ᎨᏒ ᏩᎵᏰᎢᎶᎯᎭ.
11 Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.
ᎬᏂᏳᏉᏰᏃ ᎯᎠ ᎾᏍᎩ ᎤᏲ ᏥᏣᏓᏅᏓᏛᎩ ᎾᏍᎩ ᏗᎬᏩᏓᏂᎸᎢᏍᏗ ᎨᏒ ᎤᏁᎳᏅᎯ, ᏂᎦᎥ ᎢᏣᎵᏂᎬᏁᏗ ᎨᏒ ᏭᎵᏰᎢᎶᎸ; ᏂᎦᎥ ᏗᏣᏢᏫᏍᏙᏗ ᎢᏥᏲᎲᎢ, ᎥᎥ ᏂᎦᎥ ᎢᏥᏂᏆᏘᎲᎢ, ᎥᎥ, ᏂᎦᎥ ᎢᏥᎾᏰᏍᎬᎢ, ᎥᎥ, ᏂᎦᎥ ᎤᏣᏘ ᎢᏣᏑᎵᏍᎬᎢ, ᎥᎥᎢ, ᏂᎦᎥ ᎤᎵᏂᎩᏛ ᎢᏣᏓᏅᏛᎢ, ᎥᎥ, ᏂᎦᎥ ᎠᏓᏍᏛᏗᏍᏙᏗ ᎨᏒᎢ! ᏂᎦᎥ ᏧᏓᎴᏅᏛ ᎬᏂᎨᏒ ᏂᏨᏁᎸ ᏂᏥᏍᎦᏅᎾ ᎨᏒ ᎯᎠ ᎾᏍᎩ ᎧᏃᎮᏗ ᏥᎩ.
12 Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu.
ᎾᏍᎩ ᏥᏄᏍᏗ ᎤᏙᎯᏳᎯᏍᎩᏂᏃᏅ ᏫᏨᏲᏪᎳᏁᎸᎩ, ᎠᏎᏃ ᎥᏝ ᎤᏣᏘᏂ ᎢᏳᏛᏁᎸᎯ ᏳᎬᏩᎴᎢ, ᎥᏝ ᎠᎴ Ꮎ ᎤᏣᏘᏂ ᎢᏯᎦᏛᏁᎸᎯ ᏳᎬᏩᎴᎢ; ᎠᏍᎩᏂ ᎢᏨᏍᏆᏂᎪᏗᏳ ᎨᏒ ᎤᏁᎳᏅᎯ ᎠᎦᏔᎲ ᎬᏂᎨᏒ ᎢᏣᎵᏍᏓᏁᏗᏱ.
13 Zimenezi zatilimbikitsa kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbikitsazo, tinakondwa kwambiri poona chisangalalo cha Tito, chifukwa nonsenu munamuthandiza kukhazikitsa mtima wake pansi.
ᎾᏍᎩ ᎢᏳᏍᏗ ᏂᎯ ᎤᎦᎵᏍᏗ ᎢᏣᏓᏅᏛ ᎠᏴ ᎣᎩᎦᎵᏍᏓᏛᎩ; ᎥᎥ, ᎠᎴ ᎤᏟ ᎢᎦᎢ ᎣᎦᎵᎮᎵᏍᏗ ᏄᎵᏍᏔᏅᎩ, ᏓᏓᏏ ᎠᎵᎮᎵᎬ ᎢᏳᏍᏗ, ᏅᏓᎦᎵᏍᏙᏗᏍᎬᎩ ᎾᏍᎩ ᎤᏓᏅᏙ ᏂᏥᎥ ᎡᏥᎦᎵᏍᏓᏕᎸᎢ.
14 Ndinamuwuza kuti ndimakunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi. Koma monga zonse zimene tinakuwuzani zinali zoona, tsono zomwe ndinawuza Tito zokunyadirani zinali zoona.
ᎢᏳᏰᏃ ᏥᏯᏢᏈᏎᎸᎯ ᎨᏎᏍᏗ, ᏂᎯ ᎢᏨᏁᎢᏍᏗᏍᎬᎢ, ᎥᏝ ᏱᎦᏕᎣᏍᎦ; ᏂᎦᏗᏳᏍᎩᏂ ᏧᏓᎴᏅᏛ ᎢᏨᏬᏁᏔᏅᎢ ᎤᏙᎯᏳᎯᏯ ᏥᎩ, ᎾᏍᎩᏯᏉ ᎣᎦᏢᏆᏒᎢ, ᎾᏍᎩ ᏓᏓᏏ ᎣᏣᏢᏆᏎᎸᎢ, ᎤᏙᎯᏳᎯᏯ ᏄᎵᏍᏔᏅ.
15 Ndipo chikondi chake pa inu nʼchachikulu kwambiri akakumbukira kuti nonse munali omvera, munamulandira ndi mantha ndi kunjenjemera.
ᎠᎴ ᎤᎾᏫᏱ ᎢᏥᎨᏳᎯᏳ ᎨᏒ ᎤᏣᏘ ᎤᏁᏉᏨ, ᎤᏅᏓᏛ ᎢᏦᎯᏳᎯᏳ ᎨᏒ ᏂᏥᎥᎢ, ᎾᏍᎩ ᎢᏥᎾᏰᏍᎩ ᎠᎴ ᏗᏥᎾᏫᏍᎩ ᏕᏣᏓᏂᎸᏨᎢ.
16 Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.
ᎾᏍᎩ ᎢᏳᏍᏗ ᎦᎵᎡᎵᎦ, ᎨᏨᏲᎢᏳᏗ ᎨᏒ ᏄᏓᎴᏒ ᎪᎱᏍᏗ ᎤᎬᏩᎵ.

< 2 Akorinto 7 >