< 2 Akorinto 4 >
1 Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima.
Therefore, having this ministry through the mercy we received, we are not faint-hearted;
2 Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake.
but have renounced the hidden things of shame, not walking in craftiness, nor adulterating the word of God, but by the manifestation of the truth commending ourselves to every man's conscience in the sight of God.
3 Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika.
But if our gospel is veiled, it is veiled to them that perish,
4 Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. (aiōn )
in whom the God of this world blinded the understandings of the unbelieving, so that they cannot behold the light of the gospel of the glory of Christ, who is the image of God. (aiōn )
5 Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu.
For we preach not ourselves, but Christ Jesus as Lord, and ourselves your bond-servants for Jesus' sake.
6 Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
For it is God, who commanded light to shine out of darkness, that shined in our hearts, to give the light of the knowledge of the glory of God in the face of Christ.
7 Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.
But we have this treasure in earthen vessels, that the exceeding greatness of the power may be of God, and not of us;
8 Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima;
being troubled on every side, yet not distressed; perplexed, but not in despair;
9 tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.
persecuted, but not forsaken; cast down, but not destroyed;
10 Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu.
always bearing about in the body the dying of Jesus, that the life also of Jesus may be manifested in our body.
11 Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa.
For we who live are continually delivered up to death for Jesus' sake, that the life also of Jesus may be manifested in our mortal flesh.
12 Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.
So then death worketh in us, but life in you.
13 Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula,
But having the same spirit of faith, according to that which is written, “I believed, and therefore I spoke,” we also believe, and therefore speak;
14 chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake.
knowing that he who raised up the Lord Jesus will raise up us also with Jesus, and will present us with you.
15 Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
For all things are for your sakes, that the grace abounding by means of the greater number may cause thanksgiving to abound to the glory of God.
16 Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
For which cause we are not faint-hearted; but though our outward man is perishing, yet the inward man is renewed day by day.
17 Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. (aiōnios )
For our light affliction, which is but for a moment, worketh out for us, in a higher and still higher degree, an everlasting weight of glory; (aiōnios )
18 Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya. (aiōnios )
while we look not at the things which are seen, but at the things which are not seen; for the things which are seen are but for a time; but the things which are not seen are ever lasting. (aiōnios )