< 2 Akorinto 4 >

1 Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima.
Derfor, da vi have denne Tjeneste efter den Barmhjertighed, som er bleven os til Del, så tabe vi ikke Modet;
2 Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake.
men vi have frasagt os de skammelige Smugveje, så vi ikke vandre i Træskhed, ej heller forfalske Guds Ord, men ved Sandhedens Åbenbarelse anbefale os til alle Menneskers Samvittighed for Guds Åsyn.
3 Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika.
Men om også vort Evangelium er tildækket, da er det tildækket iblandt dem, som fortabes,
4 Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. (aiōn g165)
dem, i hvem denne Verdens Gud har forblindet de vantros Tanker, for at Lyset ikke skulde skinne fra Evangeliet om Kristi Herlighed, han, som er Guds Billede. (aiōn g165)
5 Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu.
Thi ikke os selv prædike vi, men Kristus Jesus som Herre, os derimod som eders Tjenere for Jesu Skyld.
6 Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
Thi Gud, som sagde: "Af Mørke skal Lys skinne frem", han har ladet det skinne i vore Hjerter for, at bringe Kundskaben om Guds Herlighed på Kristi Åsyn for Lyset.
7 Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife.
Men denne Skat have vi i Lerkar, for at den overvættes Kraft må være Guds, og ikke fra os,
8 Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima;
vi, som trænges på alle Måder, men ikke stænges inde, ere tvivlrådige, men ikke fortvivlede,
9 tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka.
forfulgte, men ikke forladte, nedslagne, men ikke ihjelslagne,
10 Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu.
altid bærende Jesu Dødelse om i Legemet, for at også Jesu Liv må åbenbares i vort Legeme.
11 Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa.
Thi altid overgives vi, som leve, til Død for Jesu Skyld, for at også Jesu Liv må åbenbares i vort dødelige Kød.
12 Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.
Således er Døden virksom i os, men Livet i eder!
13 Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula,
Men efterdi vi have den samme Troens Ånd, som der er skrevet: "Jeg troede, derfor talte jeg," så tro også vi, og derfor tale vi også,
14 chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake.
idet vi vide, at han, som oprejste den Herre Jesus, skal også oprejse os med Jesus og fremstille os tillige med eder.
15 Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
Thi det sker alt sammen for eders Skyld, for at Nåden må vokse ved at nå til flere, og til Guds Ære forøge Taksigelsen.
16 Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku.
Derfor tabe vi ikke Modet; men om også vort udvortes Menneske fortæres, fornyes dog vort indvortes Dag for Dag.
17 Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. (aiōnios g166)
Thi vor Trængsel, som er stakket og let, virker for os over al Måde og Mål en evig Vægt af Herlighed, (aiōnios g166)
18 Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya. (aiōnios g166)
idet vi ikke se på de synlige Ting, men på de usynlige; thi de synlige ere timelige, men de usynlige ere evige. (aiōnios g166)

< 2 Akorinto 4 >