< 2 Akorinto 3 >

1 Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena?
آیا باز به سفارش خود شروع می‌کنیم؟ وآیا مثل بعضی احتیاج به سفارش نامه جات به شما یا از شما داشته باشیم؟۱
2 Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense.
شما رساله ماهستید، نوشته شده در دلهای ما، معروف وخوانده شده جمیع آدمیان.۲
3 Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.
چونکه ظاهرشده‌اید که رساله مسیح می‌باشید، خدمت کرده شده از ما و نوشته شده نه به مرکب بلکه به روح خدای حی، نه بر الواح سنگ، بلکه بر الواح گوشتی دل.۳
4 Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu.
اما بوسیله مسیح چنین اعتماد به خدا داریم.۴
5 Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu.
نه آنکه کافی باشیم که چیزی را به خود تفکر کنیم که گویا از ما باشد، بلکه کفایت مااز خداست.۵
6 Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.
که او ما را هم کفایت داد تا عهدجدید را خادم شویم، نه حرف را بلکه روح رازیرا که حرف می‌کشد لیکن روح زنده می‌کند.۶
7 Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala,
اما اگر خدمت موت که در حرف بود و برسنگها تراشیده شده با جلال می‌بود، بحدی که بنی‌اسرائیل نمی توانستند صورت موسی را نظاره کنند به‌سبب جلال چهره او که فانی بود،۷
8 kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa?
چگونه خدمت روح بیشتر با جلال نخواهد بود؟۸
9 Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo!
زیراهرگاه خدمت قصاص با جلال باشد، چند مرتبه زیادتر خدمت عدالت در جلال خواهد افزود.۹
10 Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo.
زیرا که آنچه جلال داده شده بود نیز بدین نسبت جلالی نداشت به‌سبب این جلال فایق.۱۰
11 Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!
زیرا اگر آن فانی با جلال بودی، هرآینه این باقی از طریق اولی در جلال خواهد بود.۱۱
12 Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri.
پس چون چنین امید داریم، با کمال دلیری سخن می‌گوییم.۱۲
13 Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala.
و نه مانند موسی که نقابی برچهره خود کشید تا بنی‌اسرائیل، تمام شدن این فانی را نظر نکنند،۱۳
14 Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha.
بلکه ذهن ایشان غلیظ شدزیرا که تا امروز همان نقاب در خواندن عهد عتیق باقی است و کشف نشده است، زیرا که فقط درمسیح باطل می‌گردد.۱۴
15 Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo.
بلکه تا امروز وقتی که موسی را می‌خوانند، نقاب بر دل ایشان برقرارمی ماند.۱۵
16 Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.”
لیکن هرگاه به سوی خداوند رجوع کند، نقاب برداشته می‌شود.۱۶
17 Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu.
اما خداوند روح است و جایی که روح خداوند است، آنجا آزادی است.۱۷
18 Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.
لیکن همه ما چون با چهره بی‌نقاب جلال خداوند را در آینه می‌نگریم، از جلال تاجلال به همان صورت متبدل می‌شویم، چنانکه از خداوند که روح است.۱۸

< 2 Akorinto 3 >