< 2 Akorinto 2 >

1 Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko.
εκρινα δε εμαυτω τουτο το μη παλιν ελθειν εν λυπη προς υμας
2 Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni?
ει γαρ εγω λυπω υμας και τις εστιν ο ευφραινων με ει μη ο λυπουμενος εξ εμου
3 Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe.
και εγραψα υμιν τουτο αυτο ινα μη ελθων λυπην εχω αφ ων εδει με χαιρειν πεποιθως επι παντας υμας οτι η εμη χαρα παντων υμων εστιν
4 Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.
εκ γαρ πολλης θλιψεως και συνοχης καρδιας εγραψα υμιν δια πολλων δακρυων ουχ ινα λυπηθητε αλλα την αγαπην ινα γνωτε ην εχω περισσοτερως εις υμας
5 Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera.
ει δε τις λελυπηκεν ουκ εμε λελυπηκεν αλλ απο μερους ινα μη επιβαρω παντας υμας
6 Chilango chimene ambiri a inu mwamupatsa munthu ameneyu nʼchokwanira.
ικανον τω τοιουτω η επιτιμια αυτη η υπο των πλειονων
7 Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima.
ωστε τουναντιον μαλλον υμας χαρισασθαι και παρακαλεσαι μηπως τη περισσοτερα λυπη καταποθη ο τοιουτος
8 Choncho ndikukupemphani kuti mutsimikizire chikondi chanu pa iye.
διο παρακαλω υμας κυρωσαι εις αυτον αγαπην
9 Cholinga china chimene ndinakulemberani kalata ija chinali chofuna kukuonani ngati mudzandimvera pa zonse.
εις τουτο γαρ και εγραψα ινα γνω την δοκιμην υμων ει εις παντα υπηκοοι εστε
10 Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu,
ω δε τι χαριζεσθε και εγω και γαρ εγω ει τι κεχαρισμαι ω κεχαρισμαι δι υμας εν προσωπω χριστου
11 kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.
ινα μη πλεονεκτηθωμεν υπο του σατανα ου γαρ αυτου τα νοηματα αγνοουμεν
12 Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo,
ελθων δε εις την τρωαδα εις το ευαγγελιον του χριστου και θυρας μοι ανεωγμενης εν κυριω
13 ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.
ουκ εσχηκα ανεσιν τω πνευματι μου τω μη ευρειν με τιτον τον αδελφον μου αλλα αποταξαμενος αυτοις εξηλθον εις μακεδονιαν
14 Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.
τω δε θεω χαρις τω παντοτε θριαμβευοντι ημας εν τω χριστω και την οσμην της γνωσεως αυτου φανερουντι δι ημων εν παντι τοπω
15 Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka.
οτι χριστου ευωδια εσμεν τω θεω εν τοις σωζομενοις και εν τοις απολλυμενοις
16 Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi?
οις μεν οσμη θανατου εις θανατον οις δε οσμη ζωης εις ζωην και προς ταυτα τις ικανος
17 Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.
ου γαρ εσμεν ως οι πολλοι καπηλευοντες τον λογον του θεου αλλ ως εξ ειλικρινειας αλλ ως εκ θεου κατενωπιον του θεου εν χριστω λαλουμεν

< 2 Akorinto 2 >