< 2 Akorinto 12 >
1 Ndiyenera kupitiriza kudzitamandira. Ngakhale palibe choti ndipindule, ndipitiriza kufotokoza za masomphenya ndi mavumbulutso ochokera kwa Ambuye.
Καυχᾶσθαι (δεῖ, *N(K)O*) οὐ (συμφέρον μέν, *N(K)O*) ἐλεύσομαι (δὲ *N(k)O*) εἰς ὀπτασίας καὶ ἀποκαλύψεις κυρίου.
2 Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.
Οἶδα ἄνθρωπον ἐν Χριστῷ πρὸ ἐτῶν δεκατεσσάρων, εἴτε ἐν σώματι οὐκ οἶδα, εἴτε ἐκτὸς τοῦ σώματος οὐκ οἶδα, ὁ θεὸς οἶδεν, ἁρπαγέντα τὸν τοιοῦτον ἕως τρίτου οὐρανοῦ.
3 Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.
καὶ οἶδα τὸν τοιοῦτον ἄνθρωπον, εἴτε ἐν σώματι εἴτε (χωρὶς *N(k)O*) τοῦ σώματος, οὐκ οἶδα, ὁ θεὸς οἶδεν,
4 Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena.
ὅτι ἡρπάγη εἰς τὸν παράδεισον καὶ ἤκουσεν ἄρρητα ῥήματα ἃ οὐκ ἐξὸν ἀνθρώπῳ λαλῆσαι.
5 Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga.
ὑπὲρ τοῦ τοιούτου καυχήσομαι, ὑπὲρ δὲ ἐμαυτοῦ οὐ καυχήσομαι εἰ μὴ ἐν ταῖς ἀσθενείαις (μου· *K*)
6 Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula,
ἐὰν γὰρ θελήσω καυχήσασθαι, οὐκ ἔσομαι ἄφρων· ἀλήθειαν γὰρ ἐρῶ· φείδομαι δὲ μή τις εἰς ἐμὲ λογίσηται ὑπὲρ ὃ βλέπει με, ἢ ἀκούει τι ἐξ ἐμοῦ
7 kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza.
καὶ τῇ ὑπερβολῇ τῶν ἀποκαλύψεων. (Διὸ *NO*) ἵνα μὴ ὑπεραίρωμαι, ἐδόθη μοι σκόλοψ τῇ σαρκί, ἄγγελος σατανᾶ ἵνα με κολαφίζῃ ἵνα μὴ ὑπεραίρωμαι.
8 Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere.
ὑπὲρ τούτου τρὶς τὸν κύριον παρεκάλεσα ἵνα ἀποστῇ ἀπ᾽ ἐμοῦ.
9 Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
καὶ εἴρηκέν μοι· ἀρκεῖ σοι ἡ χάρις μου· ἡ γὰρ δύναμις (μου *K*) ἐν ἀσθενείᾳ (τελεῖται. *N(k)O*) ἥδιστα οὖν μᾶλλον καυχήσομαι ἐν ταῖς ἀσθενείαις μου, ἵνα ἐπισκηνώσῃ ἐπ᾽ ἐμὲ ἡ δύναμις τοῦ Χριστοῦ.
10 Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.
διὸ εὐδοκῶ ἐν ἀσθενείαις, ἐν ὕβρεσιν, ἐν ἀνάγκαις, ἐν διωγμοῖς (καὶ *N(k)O*) στενοχωρίαις, ὑπὲρ Χριστοῦ· ὅταν γὰρ ἀσθενῶ τότε δυνατός εἰμι.
11 Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja.
Γέγονα ἄφρων (καυχώμενος· *K*) ὑμεῖς με ἠναγκάσατε. ἐγὼ γὰρ ὤφειλον ὑφ᾽ ὑμῶν συνίστασθαι· οὐδὲν γὰρ ὑστέρησα τῶν ὑπερλίαν ὑπερλίαν ἀποστόλων, εἰ καὶ οὐδέν εἰμι.
12 Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu.
τὰ μὲν σημεῖα τοῦ ἀποστόλου κατειργάσθη ἐν ὑμῖν ἐν πάσῃ ὑπομονῇ, (ἐν *k*) σημείοις (τε *no*) καὶ τέρασιν καὶ δυνάμεσιν.
13 Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!
τί γάρ ἐστιν ὃ ἡσσώθητε ὑπὲρ τὰς λοιπὰς ἐκκλησίας, εἰ μὴ ὅτι αὐτὸς ἐγὼ οὐ κατενάρκησα ὑμῶν; χαρίσασθέ μοι τὴν ἀδικίαν ταύτην.
14 Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana.
Ἰδοὺ τρίτον (τοῦτο *no*) ἑτοίμως ἔχω ἐλθεῖν πρὸς ὑμᾶς καὶ οὐ καταναρκήσω (ὑμῶν· *k*) οὐ γὰρ ζητῶ τὰ ὑμῶν ἀλλ᾽ ὑμᾶς. οὐ γὰρ ὀφείλει τὰ τέκνα τοῖς γονεῦσιν θησαυρίζειν ἀλλ᾽ οἱ γονεῖς τοῖς τέκνοις·
15 Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono?
ἐγὼ δὲ ἥδιστα δαπανήσω καὶ ἐκδαπανηθήσομαι ὑπὲρ τῶν ψυχῶν ὑμῶν, εἰ (καὶ *k*) περισσοτέρως ὑμᾶς (ἀγαπῶν *NK(o)*) (ἧσσον *N(k)O*) ἀγαπῶμαι.
16 Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani.
ἔστω δέ, ἐγὼ οὐ κατεβάρησα ὑμᾶς· ἀλλ᾽ ὑπάρχων πανοῦργος δόλῳ ὑμᾶς ἔλαβον.
17 Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu?
μή τινα ὧν ἀπέσταλκα πρὸς ὑμᾶς, δι᾽ αὐτοῦ ἐπλεονέκτησα ὑμᾶς;
18 Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?
παρεκάλεσα Τίτον καὶ συναπέστειλα τὸν ἀδελφόν· μήτι ἐπλεονέκτησεν ὑμᾶς Τίτος; οὐ τῷ αὐτῷ πνεύματι περιεπατήσαμεν; οὐ τοῖς αὐτοῖς ἴχνεσιν;
19 Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani.
(Πάλαι *N(K)O*) δοκεῖτε ὅτι ὑμῖν ἀπολογούμεθα. (κατέναντι *N(k)O*) (τοῦ *k*) θεοῦ ἐν Χριστῷ λαλοῦμεν. τὰ δὲ πάντα, ἀγαπητοί, ὑπὲρ τῆς ὑμῶν οἰκοδομῆς.
20 Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo.
φοβοῦμαι γὰρ μή πως ἐλθὼν οὐχ οἵους θέλω εὕρω ὑμᾶς, κἀγὼ κἀγὼ εὑρεθῶ ὑμῖν οἷον οὐ θέλετε, μή πως (ἔρις, ζῆλος, *N(k)O*) θυμοί, ἐριθείαι, καταλαλιαί, ψιθυρισμοί, φυσιώσεις, ἀκαταστασίαι,
21 Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.
μὴ πάλιν (ἐλθόντος *N(k)O*) (μου *no*) (ταπεινώσῃ *NK(o)*) με ὁ θεός μου πρὸς ὑμᾶς, καὶ πενθήσω πολλοὺς τῶν προημαρτηκότων καὶ μὴ μετανοησάντων ἐπὶ τῇ ἀκαθαρσίᾳ καὶ πορνείᾳ καὶ ἀσελγείᾳ ᾗ ἔπραξαν.