< 2 Akorinto 11 >
1 Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani!
Would that ye could bear with me in a little foolishness: nay indeed bear with me.
2 Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro.
For I am jealous over you with a godly jealousy: for I espoused you to one husband, that I might present you [as] a pure virgin to Christ.
3 Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu.
But I fear, lest by any means, as the serpent beguiled Eve in his craftiness, your minds should be corrupted from the simplicity and the purity that is toward Christ.
4 Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.
For if he that cometh preacheth another Jesus, whom we did not preach, or [if] ye receive a different spirit, which ye did not receive, or a different gospel, which ye did not accept, ye do well to bear with [him].
5 Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.”
For I reckon that I am not a whit behind the very chiefest apostles.
6 Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino.
But though [I be] rude in speech, yet [am I] not in knowledge; nay, in everything we have made [it] manifest among all men to you-ward.
7 Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?
Or did I commit a sin in abasing myself that ye might be exalted, because I preached to you the gospel of God for nought?
8 Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni.
I robbed other churches, taking wages [of them] that I might minister unto you;
9 Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero.
and when I was present with you and was in want, I was not a burden on any man; for the brethren, when they came from Macedonia, supplied the measure of my want; and in everything I kept myself from being burdensome unto you, and [so] will I keep [myself].
10 Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya.
As the truth of Christ is in me, no man shall stop me of this glorying in the regions of Achaia.
11 Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!
Wherefore? because I love you not? God knoweth.
12 Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira.
But what I do, that I will do, that I may cut off occasion from them which desire an occasion; that wherein they glory, they may be found even as we.
13 Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu.
For such men are false apostles, deceitful workers, fashioning themselves into apostles of Christ.
14 Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu.
And no marvel; for even Satan fashioneth himself into an angel of light.
15 Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.
It is no great thing therefore if his ministers also fashion themselves as ministers of righteousness; whose end shall be according to their works.
16 Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono.
I say again, Let no man think me foolish; but if [ye do], yet as foolish receive me, that I also may glory a little.
17 Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru.
That which I speak, I speak not after the Lord, but as in foolishness, in this confidence of glorying.
18 Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso.
Seeing that many glory after the flesh, I will glory also.
19 Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru!
For ye bear with the foolish gladly, being wise [yourselves].
20 Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi.
For ye bear with a man, if he bringeth you into bondage, if he devoureth you, if he taketh you [captive], if he exalteth himself, if he smiteth you on the face.
21 Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi. Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso.
I speak by way of disparagement, as though we had been weak. Yet whereinsoever any is bold (I speak in foolishness), I am bold also.
22 Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu.
Are they Hebrews? so am I. Are they Israelites? so am I. Are they the seed of Abraham? so am I.
23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa.
Are they ministers of Christ? (I speak as one beside himself) I more; in labours more abundantly, in prisons more abundantly, in stripes above measure, in deaths oft.
24 Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi.
Of the Jews five times received I forty [stripes] save one.
25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja.
Thrice was I beaten with rods, once was I stoned, thrice I suffered shipwreck, a night and a day have I been in the deep;
26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga.
[in] journeyings often, [in] perils of rivers, [in] perils of robbers, [in] perils from [my] countrymen, [in] perils from the Gentiles, [in] perils in the city, [in] perils in the wilderness, [in] perils in the sea, [in] perils among false brethren;
27 Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala.
[in] labour and travail, in watchings often, in hunger and thirst, in fastings often, in cold and nakedness.
28 Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse.
Beside those things that are without, there is that which presseth upon me daily, anxiety for all the churches.
29 Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?
Who is weak, and I am not weak? who is made to stumble, and I burn not?
30 Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga.
If I must needs glory, I will glory of the things that concern my weakness.
31 Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. (aiōn )
The God and Father of the Lord Jesus, he who is blessed for evermore, knoweth that I lie not. (aiōn )
32 Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire.
In Damascus the governor under Aretas the king guarded the city of the Damascenes, in order to take me:
33 Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.
and through a window was I let down in a basket by the wall, and escaped his hands.