< 2 Akorinto 10 >

1 Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu!
Ipse autem ego Paulus obsecro vos per mansuetudinem, et modestiam Christi, qui in facie quidem humilis sum inter vos, absens autem confido in vos.
2 Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzachite kuyankhula mwamphamvu monga mmene ndimayembekezera kudzachita kwa anthu ena amene amaganiza kuti machitidwe athu ndi ofanana ndi anthu a dziko lapansi.
Rogo autem vos ne præsens audeam per eam confidentiam, qua existimor audere in quosdam, qui arbitrantur nos tamquam secundum carnem ambulemus.
3 Ngakhale ife timakhala mʼdziko lapansi, sitimenya nkhondo monga mmene dziko lapansi limachitira.
In carne enim ambulantes, non secundum carnem militamus.
4 Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga.
Nam arma militiæ nostræ non carnalia sunt, sed potentia Deo ad destructionem munitionum, consilia destruentes,
5 Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
et omnem altitudinem extollentem se adversus scientiam Dei, et in captivitatem redigentes omnem intellectum in obsequium Christi,
6 Ndipo ife tidzakhala okonzeka kulanga aliyense wosamvera ngati inuyo mutakhala omvera kwenikweni.
et in promptu habentes ulcisci omnem inobedientiam, cum impleta fuerit vestra obedientia.
7 Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye.
Quæ secundum faciem sunt, videte. Si quis confidit sibi Christi se esse, hoc cogitet iterum apud se: quia sicut ipse Christi est, ita et nos.
8 Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi.
Nam, etsi amplius aliquid gloriatus fuero de potestate nostra, quam dedit nobis Dominus in ædificationem, et non in destructionem vestram: non erubescam.
9 Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga.
Ut autem non existimer tamquam terrere vos per epistolas:
10 Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.”
quoniam quidem epistolæ, inquiunt, graves sunt et fortes: præsentia autem corporis infirma, et sermo contemptibilis:
11 Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko.
hoc cogitet qui eiusmodi est, quia quales sumus verbo per epistolas absentes, tales et præsentes in facto.
12 Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru.
Non enim audemus inserere, aut comparare nos quibusdam, qui seipsos commendant: sed ipsi in nobis nosmetipsos metientes, et comparantes nosmetipsos nobis.
13 Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu.
Nos autem non in immensum gloriabimur, sed secundum mensuram regulæ, qua mensus est nobis Deus, mensuram pertingendi usque ad vos.
14 Pakuti sitikudzitama modutsa malire ngati kuti sitinafike kwa inu, popeza tinali oyamba kufika kwa inu ndi Uthenga Wabwino wa Khristu.
Non enim quasi non pertingentes ad vos, superextendimus nos: usque ad vos enim pervenimus in Evangelio Christi.
15 Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri,
non in immensum gloriantes in alienis laboribus: spem autem habentes crescentis fidei vestræ, in vobis magnificari secundum regulam nostram in abundantiam,
16 kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina.
etiam in illa, quæ ultra vos sunt, evangelizare, non in aliena regula in iis quæ præparata sunt gloriari.
17 Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
Qui autem gloriatur, in Domino glorietur.
18 Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.
Non enim qui seipsum commendat, ille probatus est: sed quem Deus commendat.

< 2 Akorinto 10 >