< 2 Mbiri 1 >
1 Solomoni mwana wa Davide anakhazikika molimbika mu ufumu wake, pakuti Yehova Mulungu wake anali naye ndipo anamukweza kwambiri.
2 Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja.
3 Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja.
4 Davide anabweretsa Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriyati Yearimu, ndi kulikhazika kumalo kumene analikonzera popeza analimangira tenti mu Yerusalemu.
5 Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko.
6 Solomoni anapita pamene panali guwa lansembe lamkuwa pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano ndipo anapereka nsembe zopsereza 1,000.
7 Usiku umenewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni ndipo anati kwa iye, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
8 Solomoni anayankha Mulungu kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Davide abambo anga ndipo mwayika ine kukhala mfumu mʼmalo mwake.
9 Tsopano Inu Yehova Mulungu, lolani kuti lonjezo lanu kwa abambo anga Davide likwaniritsidwe, pakuti mwandiyika kukhala mfumu ya anthu anu amene ndi ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi.
10 Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
11 Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo,
12 Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.”
13 Kotero Solomoni anabwerera ku Yerusalemu kuchoka kumalo opembedzerako a ku Gibiyoni, ku tenti ya msonkhano ndipo analamulira Israeli.
14 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu.
15 Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa.
16 Solomoni amagula akavalo ku Igupto ndi Kuwe pakuti anthu amalonda a mfumu amakawagula ku Kuwe.
17 Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu.