< 2 Mbiri 8 >

1 Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu ndi nyumba yake yaufumu,
Expletis autem viginti annis postquam ædificavit Salomon domum Domini et domum suam:
2 Solomoni anamanganso midzi imene anapatsidwa ndi Hiramu, ndipo anakhazikamo Aisraeli.
civitates, quas dederat Hiram Salomoni, ædificavit, et habitare ibi fecit filios Israel.
3 Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba.
Abiit quoque in Emath Suba, et obtinuit eam.
4 Iye anamanganso Tadimori ku chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anayimanga ku Hamati.
Et ædificavit Palmiram in deserto, et alias civitates munitissimas ædificavit in Emath.
5 Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira,
Extruxitque Bethoron superiorem, et Bethoron inferiorem, civitates muratas habentes portas et vectes et seras:
6 pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
Balaath etiam et omnes urbes firmissimas, quæ fuerunt Salomonis, cunctasque urbes quadrigarum, et urbes equitum. omnia quæcumque voluit Salomon atque disposuit, ædificavit in Ierusalem et in Libano, et in universa terra potestatis suæ.
7 Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli).
Omnem populum, qui derelictus fuerat de Hethæis, et Amorrhæis, et Pherezæis, et Hevæis, et Iebusæis, qui non erant de stirpe Israel,
8 Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino.
de filiis eorum: et de posteris, quos non interfecerant filii Israel, subiugavit Salomon in tributarios, usque in diem hanc.
9 Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake.
Porro de filiis Israel non posuit ut servirent operibus regis: ipsi enim erant viri bellatores, et duces primi, et principes quadrigarum et equitum eius.
10 Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za mfumu Solomoni. Onse amene ankayangʼanira anthu analipo 250.
Omnes autem principes exercitus regis Salomonis fuerunt ducenti quinquaginta, qui erudiebant populum.
11 Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”
Filiam vero Pharaonis transtulit de Civitate David in domum, quam ædificaverat ei. Dixit enim rex: Non habitabit uxor mea in domo David regis Israel, eo quod sanctificata sit: quia ingressa est in eam arca Domini.
12 Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera,
Tunc obtulit Salomon holocausta Domino super altare Domini, quod extruxerat ante porticum,
13 monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa.
ut per singulos dies offerretur in eo iuxta præceptum Moysi in sabbatis et in calendis, et in festis diebus, ter per annum, id est, in sollemnitate azymorum, et in sollemnitatem hebdomadarum, et in sollemnitate tabernaculorum.
14 Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula.
Et constituit iuxta dispositionem David patris sui officia Sacerdotum in ministeriis suis: et Levitas in ordine suo, ut laudarent, et ministrarent coram Sacerdotibus iuxta ritum uniuscuiusque diei: et ianitores in divisionibus suis per portam et portam: sic enim præceperat David homo Dei.
15 Anthu sanapatukepo pa zimene mfumu inalamula ansembe kapena Alevi pa china chilichonse, kuphatikiza za chuma.
Nec prætergressi sunt de mandatis regis tam Sacerdotes, quam Levitæ ex omnibus, quæ præceperat, et in custodiis thesaurorum.
16 Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa.
Omnes impensas præparatas habuit Salomon ex eo die, quo fundavit domum Domini usque in diem, quo perfecit eam.
17 Kenaka Solomoni anapita ku Ezioni-Geberi ndi Eloti, mʼmbali mwa nyanja ku Edomu.
Tunc abiit Salomon in Asiongaber, et in Ailath ad oram Maris rubri, quæ est in Terra Edom.
18 Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.
Misit autem ei Hiram per manus servorum suorum naves, et nautas gnaros maris, et abierunt cum servis Salomonis in Ophir, tuleruntque inde quadringenta quinquaginta talenta auri, et attulerunt ad regem Salomonem.

< 2 Mbiri 8 >