< 2 Mbiri 7 >

1 Solomoni atamaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kutentha nsembe zopsereza ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulunguyo.
Cuando Salomón terminó de orar, bajó fuego del cielo y quemó el holocausto y los sacrificios, y la gloria del Señor llenó el Templo.
2 Ansembe sanathe kulowa mʼNyumba ya Mulungu chifukwa munadzaza ulemerero wa Yehova.
Los sacerdotes no podían entrar en el Templo del Señor porque la gloria del Señor llenaba el Templo del Señor.
3 Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti, “Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala chikhalire”
Cuando todos los israelitas vieron el fuego que descendía y la gloria del Señor en el Templo, se arrodillaron e inclinaron el rostro hacia el suelo. Adoraron y alabaron al Señor, diciendo: “¡Es bueno! Su amor confiable es eterno”.
4 Tsono mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova.
Entonces el rey y todo el pueblo ofrecieron sacrificios al Señor.
5 Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu.
El rey Salomón ofreció un sacrificio de 22.000 reses y 120.000 ovejas. De este modo, el rey y todo el pueblo dedicaron el Templo de Dios.
6 Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.
Los sacerdotes estaban de pie en sus puestos, y también los levitas, con los instrumentos musicales que el rey David había hecho para dar alabanzas, y que David había utilizado para alabar. Cantaban: “¡Porque su amor fiel es eterno!”. Frente a ellos, los sacerdotes tocaron las trompetas, y todos los israelitas se pusieron de pie.
7 Solomoni anapatula malo a pakati pa bwalo kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndipo pamenepo anapereka nsembe zopsereza ndi mafuta, zopereka za chiyanjano, chifukwa guwa lansembe lamkuwa limene anapanga panalibe malo woti nʼkuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe za ufa ndi mafuta.
Después Salomón dedicó el centro del patio frente al Templo del Señor. Allí presentó los holocaustos y la grasa de las ofrendas de amistad, ya que en el altar de bronce que había hecho no cabían todos los holocaustos, las ofrendas de grano y la grasa de las ofrendas.
8 Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero kwa masiku asanu ndi awiri pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku chigwa cha ku Igupto.
Luego, durante los siete días siguientes, Salomón celebró la fiesta con todo Israel, una gran reunión que llegó desde Lebo-hamat hasta el Wadi de Egipto.
9 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panali msonkhano, pakuti anachita mwambo wopereka guwa lansembe kwa masiku asanu ndi awiri ndi masiku enanso asanu ndi awiri achikondwerero.
El octavo día celebraron una asamblea final, pues la dedicación del altar había durado siete días, y la fiesta otros siete días.
10 Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.
El día veintitrés del mes séptimo, Salomón envió al pueblo a su casa. Todavía estaban celebrando y muy contentos por la bondad que el Señor había mostrado a David, a Salomón y a su pueblo Israel.
11 Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene zinali mu mtima mwake pa Nyumba ya Yehova ndi nyumba yake yaufumu,
Después de que Salomón hubo terminado el Templo del Señor y el palacio real, habiendo realizado con éxito todo lo que había querido hacer para el Templo del Señor y para su propio palacio,
12 Yehova anamuonekera usiku ndipo anati: “Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.
el Señor se le apareció por la noche y le dijo “He escuchado tu oración y he elegido este lugar para mí como Templo de sacrificio.
13 “Ine ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena kulamulira dzombe kuti liwononge dziko, kapena kutumiza mliri pakati pa anthu,
Si yo cerrara el cielo para que no lloviera, o mandara a la langosta a devorar la tierra, o enviara una plaga entre mi pueblo,
14 ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo.
y si mi pueblo, llamado por mi nombre, se humillara y orara y se volviera a mí, y se apartara de sus malos caminos, entonces yo oiría desde el cielo, perdonaría sus pecados y sanaría su tierra.
15 Ndipo maso anga adzatsekuka ndi makutu anga adzakhala tcheru kumva mapemphero a pamalo pano.
Ahora mis ojos estarán abiertos y mis oídos prestarán atención a las oraciones que se ofrezcan en este lugar,
16 Ine ndasankha ndipo ndapatula Nyumba yangayi kotero kuti ndidzakhala mʼmenemo kwamuyaya. Maso ndi mtima wanga zidzakhala pano nthawi zonse.
porque he elegido y consagrado este Templo para que se me honre allí para siempre. Siempre velaré por él y lo cuidaré, porque me importa mucho.
17 “Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula, ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga,
“En cuanto a ti, si sigues mis caminos como lo hizo tu padre David, haciendo todo lo que te he dicho que hagas, y si guardas mis leyes y reglamentos,
18 Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu, monga ndinachitira pangano ndi abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu wolamulira Israeli.’
entonces me aseguraré de que tu reinado sea seguro. Yo hice este acuerdo con tu padre David, diciéndole: ‘Siempre tendrás un descendiente que gobierne sobre Israel’.
19 “Koma ngati iwe udzapatuka ndi kutaya malangizo ndi malamulo amene ndakupatsa ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza,
Pero si te alejas e ignoras las leyes y los mandamientos que te he dado, y si vas a servir y adorar a otros dioses,
20 pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko langa limene ndinawapatsa, ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndadzipatulira. Ndipo udzakhala ngati mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse.
entonces te quitaré de la tierra que te di. Desterraré de mi presencia este Templo que he dedicado a mi honor, y lo convertiré en objeto de burla entre las naciones.
21 Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’
Este Templo que ahora es tan respetado se estropeará de tal manera que los transeúntes dirán: ‘¿Por qué el Señor ha actuado así con esta tierra y este Templo?’
22 Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova, Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’”
La respuesta será: ‘Porque han abandonado al Señor, el Dios de sus padres, que los sacó de Egipto, y se han aferrado a otros dioses, adorándolos y sirviéndolos. Por eso el Señor ha traído sobre ellos toda esta angustia’”.

< 2 Mbiri 7 >