< 2 Mbiri 4 >

1 Solomoni anapanga guwa lamkuwa limene mulitali mwake linali mamita asanu ndi anayi, mulifupi mwakenso mamita asanu ndi anayi ndipo msinkhu wake unali mamita anayi ndi theka.
He made a bronze altar twenty cubits long, twenty cubits wide, and ten cubits high.
2 Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.
He also made the Sea of cast metal. It was circular in shape, measuring ten cubits from rim to rim, five cubits in height, and thirty cubits in circumference.
3 Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo zithunzi zangʼombe zazimuna mozungulira, zithunzi khumi pa theka la mita. Ngʼombezo zimajambulidwa mʼmizere iwiri ndipo anazipangira kumodzi ndi mbiyayo.
Below the rim, figures of oxen encircled it, ten per cubit all the way around the Sea, cast in two rows as a part of the Sea.
4 Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati.
The Sea stood on twelve oxen, three facing north, three facing west, three facing south, and three facing east. The Sea rested on them, with all their hindquarters toward the center.
5 Mbiyayo inali yochindikala ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 60,000.
It was a handbreadth thick, and its rim was fashioned like the brim of a cup, like a lily blossom. It could hold three thousand baths.
6 Kenaka anapanga mabeseni khumi otsukira zinthu ndipo asanu amawayika mbali ya kummwera, asanu mbali ya kumpoto. Mʼmenemo amatsukiramo zinthu zimene zimagwiritsidwa ntchito pa nsembe zopsereza koma mbiyamo ndi mʼmene ankasambiramo ansembe.
He also made ten basins for washing and placed five on the south side and five on the north. The parts of the burnt offering were rinsed in them, but the priests used the Sea for washing.
7 Solomoni anapanga zoyikapo nyale khumi zagolide monga momwe kunalembedwera ndipo anaziyika mʼNyumba ya Mulungu, zisanu mbali ya kummwera, ndi zisanu mbali ya kumpoto.
He made ten gold lampstands according to their specifications and placed them in the temple, five on the south side and five on the north.
8 Iye anapanga matebulo khumi ndipo anawayika mʼNyumba ya Mulungu, asanu mbali ya kummwera ndi asanu mbali ya kumpoto. Iye anapanganso mabeseni agolide okwanira 100.
Additionally, he made ten tables and placed them in the temple, five on the south side and five on the north. He also made a hundred gold bowls.
9 Iye anapanga bwalo la ansembe, bwalo lalikulu ndi zitseko za bwalolo ndipo anakuta zitsekozo ndi mkuwa.
He made the courtyard of the priests and the large court with its doors, and he overlaid the doors with bronze.
10 Anayika mbiya ija mbali yakummwera pamene mbali ya kummawa ndi kummwera zimakumana.
He put the Sea on the south side, at the southeast corner.
11 Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi. Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Mulungu imene ankagwirira Mfumu Solomoni:
Additionally, Huram made the pots, shovels, and sprinkling bowls. So Huram finished the work that he had undertaken for King Solomon in the house of God:
12 Nsanamira ziwiri; mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo; maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;
the two pillars; the two bowl-shaped capitals atop the pillars; the two sets of network covering both bowls of the capitals atop the pillars;
13 makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);
the four hundred pomegranates for the two sets of network (two rows of pomegranates for each network covering both the bowl-shaped capitals atop the pillars);
14 miyendo pamodzi ndi mabeseni ake;
the stands; the basins on the stands;
15 mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo.
the Sea; the twelve oxen underneath the Sea;
16 Miphika, mafosholo, mafoloko otengera nyama ndi ziwiya zina zonse. Zipangizo zonse zimene Hiramu Abi anapangira Mfumu Solomoni za mʼNyumba ya Yehova zinali zamkuwa wonyezimira.
and the pots, shovels, meat forks, and all the other articles. All these objects that Huram-abi made for King Solomon for the house of the LORD were of polished bronze.
17 Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani.
The king had them cast in clay molds in the plain of the Jordan between Succoth and Zeredah.
18 Zinthu zonse zimene Solomoni anapanga zinali zochuluka kwambiri kotero kuti kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.
Solomon made all these articles in such great abundance that the weight of the bronze could not be determined.
19 Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Mulungu: guwa lansembe lagolide; matebulo pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;
Solomon also made all the furnishings for the house of God: the golden altar; the tables on which was placed the Bread of the Presence;
20 zoyikapo nyale zagolide ndi nyale zake zagolide weniweni, kuti ziziyaka mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika monga analembera,
the lampstands of pure gold and their lamps, to burn in front of the inner sanctuary as prescribed;
21 maluwa agolide, nyale ndi mbaniro. (Zinali zagolide mmodzi);
the flowers, lamps, and tongs of gold—of purest gold;
22 zozimitsira nyale zagolide weniweni, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zitseko zagolide za Nyumba ya Mulungu, chitseko cha ku Malo Opatulika Kwambiri ndi zitseko za ku chipinda chachikulu.
the wick trimmers, sprinkling bowls, ladles, and censers of purest gold; and the gold doors of the temple: the inner doors to the Most Holy Place as well as the doors of the main hall.

< 2 Mbiri 4 >