< 2 Mbiri 36 >
1 Tsono anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namuyika kukhala mfumu mu Yerusalemu mʼmalo mwa abambo ake.
Alors le peuple du pays prit Joachaz, fils de Josias, et l'établit roi à la place de son père, à Jérusalem.
2 Yowahazi anali wa zaka 23 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu.
Joachaz avait vingt-trois ans lorsqu'il devint roi, et il régna trois mois à Jérusalem.
3 Mfumu ya Igupto inamuchotsa pa udindo wa ufumu mu Yerusalemu ndipo inakhometsa msonkho dziko la Yuda wa makilogalamu 3,400 asiliva ndi agolide.
Le roi d'Égypte le démit de ses fonctions à Jérusalem, et imposa au pays une amende de cent talents d'argent et d'un talent d'or.
4 Mfumu ya Igupto inakhazika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehowahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasintha dzina la Eliyakimu kukhala Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yowahazi mʼbale wake wa Eliyakimu ndi kupita naye ku Igupto.
Le roi d'Égypte établit son frère Éliakim roi sur Juda et Jérusalem, et changea son nom en Jehoïakim. Néco prit Joachaz, son frère, et le transporta en Égypte.
5 Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.
Jojakim avait vingt-cinq ans lorsqu'il devint roi, et il régna onze ans à Jérusalem. Il fit ce qui est mal aux yeux de l'Éternel, son Dieu.
6 Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anachita naye nkhondo ndipo anamumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kumutenga kupita naye ku Babuloni.
Nebucadnetsar, roi de Babylone, monta contre lui et le lia par des fers pour le conduire à Babylone.
7 Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.
Nebucadnetsar emporta aussi à Babylone quelques-uns des ustensiles de la maison de l'Éternel, et il les mit dans son temple à Babylone.
8 Zochitika zina za pa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zonyansa zimene anachita ndi zonse zinapezeka kuti zinali zomutsutsa zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Le reste des actions de Jojakim, les abominations qu'il a commises et ce qu'on a trouvé en lui, tout cela est écrit dans le livre des rois d'Israël et de Juda; et Jojakin, son fils, régna à sa place.
9 Yehoyakini anali ndi zaka 21 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu ndi masiku khumi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Jojakin avait huit ans lorsqu'il devint roi, et il régna trois mois et dix jours à Jérusalem. Il fit ce qui est mal aux yeux de l'Éternel.
10 Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.
Au retour de l'année, le roi Nebucadnetsar l'envoya et l'emmena à Babylone, avec les objets de valeur de la maison de l'Éternel, et il établit Sédécias, son frère, roi de Juda et de Jérusalem.
11 Zedekiya anali ndi zaka 21 pamene ankakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11.
Sédécias avait vingt et un ans lorsqu'il devint roi, et il régna onze ans à Jérusalem.
12 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake ndipo sanadzichepetse yekha pamaso pa mneneri Yeremiya amene ankayankhula mawu a Yehova.
Il fit ce qui est mal aux yeux de l'Éternel, son Dieu. Il ne s'humilia pas devant Jérémie, le prophète, qui parlait de la bouche de l'Éternel.
13 Iye anawukiranso mfumu Nebukadinezara amene anamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Iyeyo anali wosamva ndipo anawumitsa mtima wake. Sanatembenukire kwa Yehova Mulungu wa Israeli.
Il se révolta aussi contre le roi Nabuchodonosor, qui l'avait fait jurer par Dieu; mais il raidit son cou et endurcit son cœur pour ne pas se tourner vers l'Éternel, le Dieu d'Israël.
14 Kuwonjezera apo, atsogoleri onse a ansembe ndi anthu ena anapitirapitira kukhala osakhulupirika, kutsatira machitidwe onse onyansa a mitundu ina ndi kudetsa Nyumba ya Yehova Mulungu wawo, imene anayipatula mu Yerusalemu.
De plus, tous les chefs des prêtres et du peuple se rendirent très coupables de toutes les abominations des nations, et ils souillèrent la maison de l'Éternel, qu'il avait sanctifiée à Jérusalem.
15 Yehova, Mulungu wa makolo awo, ankatumiza mawu kwa iwo kudzera kwa amithenga ake kawirikawiri, chifukwa ankawamvera chisoni anthu ake ndi malo ake okhalapo.
Yahvé, le Dieu de leurs pères, leur a envoyé ses messagers, se levant de bonne heure et envoyant, car il avait pitié de son peuple et de sa demeure.
16 Koma iwo ananyoza amithenga a Mulungu, anapeputsa mawu awo ndipo ankaseka aneneri ake mpaka anawutsa mkwiyo wa Yehova pa anthu ake ndipo panalibenso mankhwala owachiritsa.
Mais ils se sont moqués des messagers de Dieu, ont méprisé ses paroles et se sont moqués de ses prophètes, jusqu'à ce que la colère de Yahvé s'élève contre son peuple, jusqu'à ce qu'il n'y ait plus de remède.
17 Yehova anabweretsa mfumu ya anthu a ku Babuloni, imene inapha anyamata awo ndi lupanga ku malo opatulika, ndipo sanasiye kaya mnyamata kapena mtsikana, wamkulu kapena wokalamba. Mulungu anapereka onsewo kwa Nebukadinezara.
C'est pourquoi il fit venir sur eux le roi des Chaldéens, qui tua leurs jeunes gens par l'épée dans la maison de leur sanctuaire, et n'eut aucune compassion pour le jeune homme ou la vierge, le vieillard ou l'infirme. Il les livra tous entre ses mains.
18 Iye ananyamula kupita nazo ku Babuloni zipangizo zonse za mʼNyumba ya Yehova Mulungu wawo, zazikulu ndi zazingʼono zomwe, ndi chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso chuma cha mfumu ndi akuluakulu ake.
Tous les ustensiles de la maison de Dieu, grands et petits, les trésors de la maison de l'Éternel, les trésors du roi et de ses princes, tout cela, il le transporta à Babylone.
19 Iwo anayatsa moto Nyumba ya Mulungu, ndipo anagwetsa makoma a Yerusalemu. Anatentha moto nyumba zonse zaufumu ndipo anawononga chilichonse chimene chinali chofunika.
Ils brûlèrent la maison de Dieu, démolirent la muraille de Jérusalem, incendièrent tous ses palais et détruisirent tous ses objets précieux.
20 Iye anagwira ukapolo anthu otsala amene anapulumuka ku lupanga ndi kupita nawo ku Babuloni, ndipo anakhala antchito ake ndi ana ake mpaka pamene ufumu wa Peresiya unakhazikitsidwa.
Il emmena à Babylone ceux qui avaient échappé à l'épée, et ils le servirent, lui et ses fils, jusqu'au règne du royaume de Perse,
21 Dziko linakondwera ndi masabata ake. Pa nthawi yonse ya chipasuko chake nthaka inapuma, mpaka zaka 70 zinakwana pokwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya.
pour accomplir la parole de Yahvé par la bouche de Jérémie, jusqu'à ce que le pays ait joui de ses sabbats. Tant qu'il fut en désolation, il observa le sabbat, pour accomplir soixante-dix ans.
22 Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:
La première année de Cyrus, roi de Perse, afin que la parole de Yahvé par la bouche de Jérémie s'accomplisse, Yahvé stimula l'esprit de Cyrus, roi de Perse, de sorte qu'il fit une proclamation dans tout son royaume et l'écrivit, en disant:
23 Chimene mfumu Koresi ya Peresiya ikunena ndi ichi: “Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa ine mafumu onse a dziko lapansi ndipo wandisankha kuti ndimumangire Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ku Yuda. Aliyense wa anthu ake pakati panu, Yehova Mulungu wake akhale naye, ndipo apite.”
« Cyrus, roi de Perse, dit: 'Yahvé, le Dieu du ciel, m'a donné tous les royaumes de la terre; et il m'a ordonné de lui bâtir une maison à Jérusalem, qui est en Judée. Si quelqu'un parmi vous fait partie de son peuple, que Yahvé son Dieu soit avec lui, et qu'il monte. »