< 2 Mbiri 34 >
1 Yosiya anali wa zaka zisanu ndi zitatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 31.
2 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndi kutsata makhalidwe a Davide abambo ake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.
3 Mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ulamuliro wake, iye akanalibe wamngʼono, anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide abambo ake. Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri iye anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu kuchotsa malo azipembedzo, mafano a Asera, milungu yosema ndi mafano owumbidwa.
4 Maguwa ansembe a Baala anagwetsedwa iye atalamulira. Anadula zidutswazidutswa maguwa ofukizira lubani amene anali pamwamba pake, ndipo anaphwanya mafano a Asera, milungu ndi zifaniziro zake. Anaziperapera ndipo anaziwaza pamwamba pa manda a amene ankapereka nsembe kwa mafanowo.
5 Iye anatentha mafupa a ansembe pa maguwa awo, kotero iye anayeretsa Yuda ndi Yerusalemu.
6 Ku mizinda ya Manase, Efereimu ndi Simeoni mpaka kufika ku Nafutali, ndiponso malo a mabanja owazungulira,
7 iye anagwetsa maguwa ansembe ndi mafano a Asera ndi kuphwanyaphwanya milungu yawo kukhala fumbi ndi kuduladula maguwa ofukizapo lubani mʼdziko lonse la Israeli. Atatero, anabwerera ku Yerusalemu.
8 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya, atayeretsa dziko ndi Yerusalemu, Yosiya anatuma Safani mwana wa Azariya ndi Maaseya, wolamulira mzinda pamodzi ndi Yowa mwana wa Yowahazi mlembi wolemba mbiri, kuti akonze Nyumba ya Yehova Mulungu wake.
9 Iwo anapita kwa Hilikiya, mkulu wa ansembe ndipo anamupatsa ndalama zimene zinaperekedwa mʼNyumba ya Mulungu, zimene Alevi amene anali alonda apakhomo analandira kuchokera kwa anthu a ku Manase, Efereimu ndi onse otsala a ku Israeli ndiponso anthu onse ochokera ku Yuda ndi Benjamini ndi okhala mu Yerusalemu.
10 Ndipo anazipereka mʼmanja mwa anthu amene anasankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Anthu amenewa ankalipira antchito amene ankakonzanso Nyumba ya Mulungu.
11 Iwo anaperekanso ndalama kwa amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba kuti agule miyala yosema ndi matabwa a phaso la nyumba ndi nsichi zomangira zomwe mfumu ya Yuda inalekerera kuti zigwe ndi kuwonongeka.
12 Anthuwa anagwira ntchitoyi mokhulupirika. Amene ankawayangʼanira anali Yahati ndi Obadiya, Alevi ochokera ku banja la Merari, ndi Zekariya ndi Mesulamu ochokera ku banja la Kohati. Alevi onse amene anali aluso loyimbira zida za nyimbo
13 ankayangʼanira anthu onyamula katundu, namatsogolera anthu onse amene ankagwira ntchito iliyonse yotumikira. Alevi ena anali alembi, akapitawo ndiponso alonda apamakomo.
14 Pa nthawi imene ankatulutsa ndalama zimene anabwera nazo ku Nyumba ya Yehova, wansembe Hilikiya anapeza Buku la Malamulo limene linaperekedwa kudzera mwa Mose.
15 Hilikiya anati kwa Safani, mlembi wa zochitika, “Ine ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Iye analipereka kwa Safani.
16 Ndipo Safani anapita nalo bukulo kwa mfumu ndi kumufotokozera kuti: “Akuluakulu anu akuchita zonse zimene zinapatsidwa kwa iwo.
17 Iwo alipira ndalama zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo azipereka kwa akapitawo ndi anthu antchito.”
18 Kenaka Safani, mlembi wa zochitika anawuza mfumu, “Wansembe, Hilikiya wandipatsa ine buku ili.” Ndipo Safani anawerenga bukulo pamaso pa mfumu.
19 Mfumu itamva mawu a Buku la Malamulo, inangʼamba mkanjo wake.
20 Iye analamula izi kwa Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Abidoni mwana wa Mika, Safani mlembi wa zochitika ndi Asaya mtumiki wa mfumu:
21 “Pitani ndipo mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa otsala a Israeli ndi Yuda za zimene zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu umene watsanulidwa pa ife chifukwa makolo athu sanasunge mawu a Yehova. Iwo sanachite motsatira zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili.”
22 Hilikiya pamodzi ndi anthu amene anawatuma aja, anapita kukayankhula ndi mneneri wamkazi Hulida, amene anali mkazi wa Salumu mwana wa Tokati, mwana wa Hasira, wosunga zovala zaufumu. Hulida ankakhala mu Yerusalemu, mʼdera lachiwiri la mzindawo.
23 Iye anati kwa anthuwo, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, muwuzeni munthu amene wakutumani kwa ineyo kuti,
24 ‘Yehova akunena kuti, Ine ndidzabweretsa mavuto pamalo pano ndi pa anthu ake, matemberero onse amene alembedwa mʼbukuli amene awerengedwa pamaso pa mfumu ya Yuda.
25 Chifukwa iwo anasiya Ine ndi kufukiza lubani kwa milungu ina ndi kuwutsa mkwiyo wanga ndi zonse zimene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzatsanulidwa pamalo pano ndipo sudzazimitsidwa.’
26 Uzani mfumu ya Yuda imene yakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova Mulungu wa Israeli, ‘Chimene Yehova, Mulungu wa Israeli akunena mokhudzana ndi mawu amene mwamva ndi ichi:
27 Pakuti mtima wako walapa, ndipo wadzichepetsa wekha pamaso pa Mulungu pamene unamva zimene Iye ananena motsutsa malo ano ndi anthu ake, ndipo chifukwa iwe unadzichepetsa wekha pamaso pa Ine ndi kungʼamba zovala zako ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, atero Yehova.
28 Tsono Ine ndidzakutengera kwa makolo ako, ndipo udzayikidwa mʼmanda mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene Ine ndidzabweretsa pa malo ano ndi pa iwo amene amakhala pano.’” Choncho iwo anatenga yankho lakelo ndi kubwerera kwa mfumu.
29 Ndipo mfumu inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Yuda ndi Yerusalemu.
30 Iye anapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu a Yuda, anthu a mu Yerusalemu, ansembe ndi Alevi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Iye anawerenga pamaso pawo mawu onse a Buku la Chipangano, limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova.
31 Mfumu inayimirira pa chipilala chake ndipo inachitanso pangano pamaso pa Yehova: kutsatira Yehova, ndi kusunga malamulo ake, machitidwe ake ndi malangizo ake ndi mtima wake wonse ndi moyo wake wonse, ndi kumvera mawu a pangano olembedwa mʼbukulo.
32 Tsono Yosiya anawuza aliyense amene anali mu Yerusalemu ndi Benjamini kuti azisunga panganoli. Anthu a mu Yerusalemu anachita izi motsata pangano la Mulungu, Mulungu wa makolo awo.
33 Yosiya anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse limene linali la Aisraeli ndipo anawuza onse amene anali mu Israeli kutumikira Yehova Mulungu wawo. Pa masiku onse a moyo wake, iye sanaleke kutsatira Yehova, Mulungu wa makolo awo.