< 2 Mbiri 33 >

1 Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 55.
[默納舍崇拜偶像]默納舍登極時年十二歲,在耶路撒冷作王凡五十五年。
2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira machitidwe a mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli.
他行了上主視為惡的事,仿傚上主從以色列子民前驅逐的異民所行的可恥之事。
3 Iyeyo anamanganso malo opembedzerapo mafano amene Hezekiya abambo ake anawaphwasula; anamanganso maguwa ansembe a Baala ndi kupanga mafano a Asera. Iye amagwadira zolengedwa zonse zamlengalenga ndi kumazipembedza.
他重建了他父親希則克雅所拆毀的高丘,又為巴耳建立了祭壇,製造阿舍辣,叩拜奉事天上的萬象。
4 Manase anamanga maguwa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Ine ndidzakhala mu Yerusalemu mpaka muyaya.”
雖然上主曾指著聖殿說過:「我要將我的名永遠立在耶路撒冷,」他仍在上主殿內建立了一些祭壇;
5 Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova anamangamo maguwa ansembe a zolengedwa zonse zamlengalenga.
且在上主殿的兩庭院內,為天上萬象建立了一些祭壇;
6 Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo.
使自己的兒子在本希農山谷中經火,行占卜,邪術,立招魂師和術士;不斷行上主視為惡的事,惹上主發怒。
7 Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya.
他又在天主殿內立了他所彫製的偶像;雖然論及這殿天主曾對達味和他的兒子撒羅滿說過:「我要在這殿內,和在我由以色列各支派所選出的耶路撒冷城,立我的名,直到永遠。
8 Ine sindidzachotsanso phazi la Aisraeli kuchoka mʼdziko limene ndawapatsa makolo ako, ngatitu iwowa adzasamalira kuchita chilichonse chimene ndinawalamulira za malamulo onse, malangizo ndi miyambo imene inapatsidwa kudzera mwa Mose.”
只要以色列人遵行我藉梅瑟所吩咐他們的一切法律、典章和律例,我不再使他們的腳,離開我賜予你們祖先的土地。」
9 Koma Manase anasocheretsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, kotero anachita zoyipa zambiri kupambana mitundu imene Yehova anayiwononga pamaso pa Aisraeli.
但默納舍誘惑猶大和耶路撒冷的居民行惡,甚至上主由以色列子民前所消滅的那些民族。[默納舍受罰改過]
10 Yehova anayankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanasamaleko.
為此,上主曾警告莫舍納和他的百姓,但是他們不肯聽從。
11 Kotero Yehova anawatumizira atsogoleri a ankhondo a ku Asiriya amene anagwira Manase ukapolo, anayika ngowe mʼmphuno mwake, namumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
因此,上主使亞述王的將官前來攻打他們,用鉤子勾住默納舍,用鎖鏈鎖住,解送到巴比倫。
12 Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake.
默納舍在這患難中,呼求了上主他的天主,在他祖先的天主前,大發謙卑,
13 Ndipo atapemphera, Yehova anakhudzidwa ndi kupempha kwakeko ndipo anamvera madandawulo ake. Kotero anamubweretsanso ku Yerusalemu ndi ku ufumu wake. Ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu.
哀懇上主,上主便俯允了他的祈求,垂聽了他的哀禱,使他歸回耶路撒冷,恢復了他的王位;默納舍這才知道只有上主是天主。[掃除偶像]
14 Zitapita izi iye anamanga khoma la kunja kwa Mzinda wa Davide kumadzulo kwa kasupe wa Gihoni ku chigwa mpaka polowera ku Chipata cha Nsomba kuzungulira phiri la Ofeli. Iyeyo anakweza kwambiri khomalo. Anayikanso atsogoleri a nkhondo ku mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda.
此後,默納舍在達味城外另築了一道城牆,西邊由谷內的基紅起,直到魚門,將敖斐耳圍起,且將城牆加建的很高;在猶大各堅城內派有將帥駐守。
15 Iye anachotsa milungu yonse yachilendo ndi fano mʼNyumba ya Yehova komanso maguwa ansembe onse amene anamanga pa phiri la Nyumba ya Mulungu ndi mu Yerusalemu, nazitayira kunja kwa mzinda.
又從上主殿內除去了外神和偶像,將他在上主殿的山上和耶路撒冷所建立的祭壇,都一律拆毀,拋在城外,
16 Kenaka anabwezeretsa guwa lansembe la Yehova ndi kupereka zopereka zachiyanjano ndiponso zopereka zamatamando ndipo anawuza Yuda kuti atumikire Yehova Mulungu wa Israeli.
重修了上主的祭壇,在上面獻和平祭和感恩祭,命令猶大人只奉事上主以色列的天主。
17 Komabe anthu anapitiriza kupereka nsembe ku malo achipembedzo, koma kwa Yehova, Mulungu wawo yekha.
但是民眾仍然在高丘獻祭,不過只巷上主天主獻祭。[默納舍逝世]
18 Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Manase, kuphatikiza mapemphero ake kwa Mulungu wake ndi mawu amene alosi anayankhula kwa iye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli, zalembedwa mʼmabuku a mafumu a Israeli.
默納舍其餘的事蹟,以及他巷天主所發的禱詞,並諸先見者奉上主,以色列天主的名對他所說的話,都記載在以色列列王實錄上。
19 Pemphero lake ndi momwe Mulungu anakhudzidwira ndi kupempha kwakeko, pamodzinso ndi machimo ake onse ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso malo onse amene anamanga, malo azipembedzo ndi mafano a Asera ndi mafano asanadzichepetse, zonse zalembedwa mʼmbiri ya alosi.
他如何祈禱和上主如何應允,他未自卑以前的一切罪惡和不忠,以及他在何處建立高丘,立阿舍辣和彫刻的偶像等事,都記載在諸先見者的言行錄上。
20 Manase anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yake yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
默納舍與他的祖先同眠,葬在他王宮的花園裏;他的兒子阿孟繼位為王。[阿孟登極]
21 Amoni anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka ziwiri.
阿孟登極時年二十二歲,在耶路撒冷作王二年。
22 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase abambo ake. Amoni analambira ndi kupereka nsembe kwa mafano onse amene anapanga Manase.
他行了上主視為惡的事,全如同他父親默納舍;向他父親默納舍所彫刻的一切偶像獻祭膜拜,
23 Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake.
從沒有像他父親默納舍在上主面前自謙自卑過;阿孟只知罪上加罪。
24 Akuluakulu a Amoni anamuchita chiwembu ndipo anamupha mʼnyumba yake yaufumu.
為此,他的臣僕共謀造反,在宮中將他殺死。
25 Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anakonzera chiwembu mfumu Amoni, ndipo anayika mwana wake Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwake.
當地的人民卻將所有反叛阿孟王的人都殺了,立他的兒子約史雅繼位為王。

< 2 Mbiri 33 >