< 2 Mbiri 32 >
1 Zitatha zonse zimene Hezekiya anachita mokhulupirika, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kuthira nkhondo dziko la Yuda. Iye anazinga mizinda yotetezedwa ya Yuda, kuganiza kuti ayigonjetsa.
2 Pamene Hezekiya anaona kuti Senakeribu wabwera ndipo wakonzeka kuchita nkhondo ndi Yerusalemu,
3 iye anakambirana ndi akuluakulu ake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo za kutseka akasupe ochoka ku kasupe amene anali kunja kwa mzinda, ndipo iwo anamuthandiza.
4 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana, ndipo anatseka akasupe onse pamodzi ndi mtsinje umene umayenda mʼkati mwa nthakamo. Iwo ankanena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mafumu a Asiriya akabwera kuno adzapeze madzi ambiri?”
5 Kenaka iye anagwira ntchito molimbika kukonza madera ogumuka a khoma ndi kumangapo msanja. Anamanganso mpanda wina kunja kwa mpanda winawo ndipo anamanga zolimbitsa Milo ku mzinda wa Davide.
6 Iye anasankha atsogoleri a ankhondo olamulira anthu ndipo anawasonkhanitsa pamaso pake pa bwalo la chipata cha mzinda ndi kuwalimbikitsa ndi mawu awa:
7 “Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite mantha kapena kutaya mtima chifukwa cha mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lalikulu lankhondo limene ali nalo, pakuti ife tili ndi mphamvu yayikulu kuposa imene ili ndi iye.
8 Iye ali ndi mphamvu ya anthu basi, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kutithandiza ndi kuchita nkhondo zathu.” Ndipo anthu anapeza chilimbikitso kuchokera pa zimene Hezekiya mfumu ya Yuda ananena.
9 Nthawi ina, pamene Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo anali atazinga Lakisi, iye anatumiza atsogoleri ake ankhondo ku Yerusalemu ndi uthenga uwu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a ku Yuda amene anali kumeneko:
10 “Senakeribu mfumu ya ku Asiriya akuti: Kodi inu mukukhulupirira chiyani, kuti mukukhalabe mu Yerusalemu mutazingidwa?
11 Pamene Hezekiya akunena kuti ‘Yehova Mulungu wathu adzatipulumutsa kuchoka mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya,’ iye akukusocheretsani, kuti mufe ndi njala ndi ludzu.
12 Kodi si Hezekiya amene anachotsa malo opembedzerapo Mulungu ameneyu ndi maguwa ansembe ndi kunena kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe limodzi ndi kupserezapo nsembe?’
13 “Kodi inu simukudziwa zimene ine ndi makolo anga tachita kwa anthu a mitundu ina? Kodi milungu ya mitundu imeneyi inatha kupulumutsa dziko lawo kuchoka mʼdzanja langa?
14 Kodi ndi milungu iti mwa milungu ya mitundu ina ya anthuwo, imene makolo anga anayiwononga kotheratu, inatha kupulumutsa anthu ake mʼdzanja langa? Nanga tsono Mulungu wanuyo adzakupulumutsani mʼdzanja langa motani?
15 Choncho inu musalole kuti Hezekiya akunamizeni ndi kukusocheretsani motere. Musamukhulupirire, pakuti palibe mulungu wa mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse umene unatha kupulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa kapena mʼdzanja la makolo anga. Nanga bwanji Mulungu wanuyo, sadzatha kukupulumutsani kuchoka mʼdzanja langa!”
16 Atsogoleri a ankhondo a Senakeribu anapitiriza kuyankhula zotsutsana ndi Yehova Mulungu ndi mtumiki wake Hezekiya.
17 Mfumunso inalemba makalata onyoza Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo inanena zotsutsana naye izi: “Monga momwe milungu ya anthu a mayiko ena sinathe kuwapulumutsa kuchoka mʼdzanja langa, chonchonso Mulungu wa Hezekiya sadzapulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa.”
18 Kenaka iwo anafuwula mu Chihebri kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuwaopseza ndi kuwachititsa mantha ndi cholinga choti alande mzindawo.
19 Iwo anayankhula za Mulungu wa Yerusalemu monga anayankhulira za milungu ya anthu ena a pa dziko lapansi, ntchito ya manja a anthu.
20 Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi anafuwulira kumwamba mʼpemphero chifukwa cha zimenezi.
21 Ndipo Yehova anatumiza mngelo amene anadzapha anthu onse odziwa nkhondo ndi atsogoleri ndiponso oyangʼanira misasa ya mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu anabwerera kwawo wamanyazi. Ndipo atalowa mʼnyumba ya mulungu wake, ena mwa ana ake anamupha ndi lupanga.
22 Kotero Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu a ku Yerusalemu kuchoka mʼdzanja la Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi mʼdzanja la anthu ena. Yehova anawateteza ku mbali zonse.
23 Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse.
24 Pa nthawi imeneyo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Iye anapemphera kwa Yehova, amene anamuyankha ndi kumupatsa chizindikiro chodabwitsa.
25 Koma Hezekiya anali ndi mtima wonyada ndipo sanachite molingana ndi kukoma mtima kumene Mulungu anamuonetsera. Choncho mkwiyo wa Yehova unali pa iye ndi pa Yuda ndi Yerusalemu.
26 Koma kenaka Hezekiya analapa za kunyada kwakeko, monga anachitanso anthu a mu Yerusalemu. Choncho mkwiyo wa Yehova sunafike pa iwo pa nthawi ya Hezekiya.
27 Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali.
28 Iye anamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta a olivi, ndiponso anamanga nyumba zodyeramo ngʼombe zosiyanasiyana, ndi makola a nkhosa.
29 Iyeyo anamanga midzi ndipo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, pakuti Mulungu anamupatsa chuma chambiri.
30 Ndi Hezekiya amene anatseka ku mtunda kwa kasupe wa Gihoni, ndi kumuwongolera kuti madzi ake apite mbali ya kumadzulo kwa Mzinda wa Davide. Iye ankachita bwino pa ntchito iliyonse imene ankagwira.
31 Koma pamene nthumwi zotumizidwa ndi atsogoleri a ku Babuloni zinabwera kudzamufunsa za chizindikiro chozizwitsa chimene chinachitika mʼdzikomo, Mulungu anamusiya yekha, kumuyesa kuti adziwe zonse zimene zinali mu mtima mwake.
32 Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Hezekiya ndi ntchito za kudzipereka kwake zalembedwa mʼmasomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli.
33 Hezekiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pa phiri pamene pali manda a zidzukulu za Davide. Ayuda onse ndi anthu a mu Yerusalemu anamulemekeza atamwalira. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.