< 2 Mbiri 30 >
1 Hezekiya anatumiza uthenga mʼdziko lonse la Israeli ndi ku Yuda ndiponso analemba makalata ku Efereimu ndi Manase, oyitana anthu kuti abwere ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli.
Et Ézéchias envoya dans tout Israël et Juda et adressa aussi des rescrits à Éphraïm et Manassé pour qu'ils vinssent au Temple de l'Éternel à Jérusalem faire une Pâque à l'Éternel, Dieu d'Israël.
2 Mfumu ndi akuluakulu ake pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu anagwirizana kuti akondwerere Paska pa mwezi wachiwiri.
Et le roi et ses princes et toute l'Assemblée de Jérusalem furent d'avis de faire la Pâque au second mois.
3 Iwo sanathe kukondwerera pa nthawi yake chifukwa si ansembe ambiri amene anadziyeretsa ndiponso anthu anali asanasonkhane mu Yerusalemu.
Car ils ne pouvaient la faire à ce moment, les Prêtres ne s'étant pas encore mis en état de sainteté en nombre suffisant, et la nation n'étant pas réunie dans Jérusalem.
4 Chikonzerochi chinaoneka kuti chinali chabwino kwa mfumu pamodzi ndi anthu onse.
Et l'avis eut l'agrément du roi et de toute l'Assemblée.
5 Iwo anagwirizana zoti alengeze mu Israeli monse kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani, kuyitana anthu kuti abwere ku Yerusalemu ndi kudzakondwerera Paska wa Yehova, Mulungu wa Israeli. Si ambiri amene ankachita chikondwererochi monga momwe kunalembedwera.
Et ils statuèrent qu'on ferait publier dans tout Israël, de Béerséba à Dan, qu'on eût à venir faire une Pâque à l'Éternel, Dieu d'Israël, à Jérusalem, car ils ne l'avaient pas célébrée en nombre conformément à l'Écriture.
6 Molamulidwa ndi mfumu, amithenga anapita mu Israeli yense ndi Yuda ndi makalata ochokera kwa mfumu ndi kwa akuluakulu ake, olembedwa kuti, “Aisraeli bwererani kwa Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Israeli, kuti abwerere kwa inu amene mwatsala, amene mwapulumuka mʼdzanja la mafumu a ku Asiriya.
Et les coureurs allèrent avec les rescrits émanant du roi et de ses princes dans tout Israël et Juda, et d'après l'ordre du roi ils dirent: Enfants d'Israël, revenez à l'Éternel, Dieu d'Abraham, d'Isaac et d'Israël, afin qu'il revienne à votre reste échappé aux mains des rois d'Assyrie.
7 Musakhale ngati makolo anu ndi abale anu, amene anali osakhulupirika kwa Yehova Mulungu wa makolo awo kotero kuti anawachititsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha, monga mukuoneramu.
Et n'imitez pas vos pères et vos frères qui ont été infidèles à l'Éternel, Dieu de leurs pères, et qu'il a livrés à la désolation, comme vous le voyez!
8 Musawumitse khosi monga anachitira makolo anu, Gonjerani Yehova. Bwerani ku malo opatulika, amene anawapatula kwamuyaya. Tumikirani Yehova Mulungu wanu kuti mkwiyo wake ukuchokereni.
Maintenant ne roidissez pas votre col comme vos pères, donnez la main à l'Éternel et venez à son Sanctuaire qu'il a sanctifié pour l'éternité, et soumettez-vous à l'Éternel, votre Dieu, pour que se détourne de vous l'ardeur de sa colère.
9 Ngati inu mubwerera kwa Yehova, pamenepo abale anu ndi ana anu adzachitiridwa chifundo ndi amene anawagwira ukapolo ndipo adzabwereranso ku dziko lino pakuti Yehova, Mulungu wanu ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Iye sadzakufulatirani ngati inuyo mubwerera kwa Iye.”
Car si vous revenez à l'Éternel, vos frères et vos fils seront l'objet de la compassion de leurs ravisseurs, et pourront revenir dans ce pays; car l'Éternel, votre Dieu, est clément et miséricordieux, et Il ne détournera pas son visage de vous, si vous vous retournez vers Lui.
10 Amithenga aja anapita mzinda ndi mzinda wa ku Efereimu ndi Manase mpaka ku Zebuloni, koma anthu anawanyoza ndi kuwachita chipongwe.
Et les coureurs passèrent de ville en ville dans le pays d'Ephraïm et de Manassé et jusqu'à Zabulon; mais l'on se rit d'eux et l'on se moqua d'eux.
11 Komabe anthu ena a ku Aseri, Manase ndi Zebuloni anadzichepetsa ndipo anapita ku Yerusalemu.
Cependant il y eut des hommes de Asser et de Manassé et de Zabulon qui s'humilièrent et vinrent à Jérusalem.
12 Dzanja la Mulungu linalinso pa anthu a ku Yuda, kuwapatsa mtima umodzi wochita zimene mfumu ndi akuluakulu ake analamula potsata mawu a Yehova.
Juda aussi sentit la main de Dieu qui leur donna un même cœur pour exécuter l'ordre du roi et des princes conforme à la parole de l'Éternel.
13 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana mu Yerusalemu kudzachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti pa mwezi wachiwiri.
Et il se réunit à Jérusalem un peuple nombreux pour faire la fête des azymes au second mois, assemblée immense.
14 Anachotsa mu Yerusalemu maguwa ofukizira lubani ndipo anakawaponya mʼchigwa cha Kidroni.
Et ils se mirent en devoir de faire disparaître les autels qui étaient dans Jérusalem, et toutes les tables à encenser, et ils les jetèrent dans le torrent du Cédron.
15 Iwo anapha mwana wankhosa wa Paska pa tsiku la 14 la mwezi wachiwiri. Ansembe ndi Alevi anachita manyazi ndipo anadziyeretsa ndi kubweretsa nsembe zopsereza ku Nyumba ya Yehova.
Et ils immolèrent la Pâque le quatorzième jour du second mois; et les Prêtres et les Lévites avaient eu honte, et s'étaient mis en état de sainteté, et ils offrirent des holocaustes dans le Temple de l'Éternel.
16 Ndipo anakhala mʼmalo awo a nthawi zonse potsatira zolembedwa mʼmalamulo a Mose munthu wa Mulungu. Ansembe anawaza magazi amene anawapatsa Alevi.
Et ils se tenaient à leur poste, suivant leur règle, d'après la Loi de Moïse, homme de Dieu, les Prêtres faisant l'aspersion du sang qu'ils recevaient des mains des Lévites.
17 Popeza ambiri mʼgululo anali asanadziyeretse, Alevi anapha ana ankhosa a Paska a iwo amene, mwa mwambo, anali osayeretsedwa ndipo sakanatha kupereka ana ankhosa awo kwa Yehova.
Comme il y avait beaucoup de gens dans l'Assemblée qui ne s'étaient pas mis en état de sainteté, les Lévites se chargèrent d'immoler les agneaux de Pâque pour tous ceux qui n'étaient pas purs, et ils les consacraient à l'Éternel.
18 Ngakhale kuti ambiri mwa anthu ochokera ku Efereimu, Manase, Isakara ndi Zebuloni sanadziyeretse okha, komabe anadya Paska motsutsana ndi zimene zinalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, kunena kuti, “Yehova wabwino, khululukirani aliyense
En effet, une grande quantité de gens d'Éphraïm et de Manassé et d'Issaschar et de Zabulon ne s'étaient pas purifiés, mais mangeaient la Pâque contrairement à l'Écriture. Mais Ézéchias avait intercédé pour eux par cette prière: Que l'Éternel, le Dieu bon, pardonne
19 amene wayika mtima wake kufunafuna Yehova, Mulungu wa makolo ake, ngakhale ali wosayeretsedwa molingana ndi malamulo a malo opatulika.”
à tous ceux qui ont dirigé leur cœur à la recherche du Dieu, l'Éternel, Dieu de leurs pères, sans avoir toutefois pratiqué la sainte purification.
20 Ndipo Yehova anamvera Hezekiya ndipo anachiritsa anthuwo.
Et l'Éternel exauça Ézéchias et pardonna au peuple.
21 Aisraeli amene anali mu Yerusalemu anachita chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti kwa masiku asanu ndi awiri akusangalala kwambiri, pamene Alevi ndi ansembe amayimbira Yehova tsiku lililonse, akuyimbira zida zamatamando za Yehova.
Ainsi fut célébrée par les enfants d'Israël présents à Jérusalem la fête des azymes pendant sept jours en grande allégresse, et chaque jour les Lévites et les Prêtres louaient l'Éternel avec les instruments de la louange de l'Éternel.
22 Hezekiya anayankhula molimbikitsa Alevi onse amene anaonetsa kumvetsa bwino za kutumikira Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri anadya gawo lawo ndi kupereka nsembe zachiyanjano ndi kutamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo.
Et Ézéchias adressa des encouragements à tous les Lévites qui se montraient habiles dans la belle science [du culte] de l'Éternel, et ils mangèrent l'aliment festal pendant sept jours, en offrant des sacrifices pacifiques et louant l'Éternel, Dieu de leurs pères.
23 Ndipo msonkhano wonse unagwirizana zopitiriza chikondwerero kwa masiku ena asanu ndi awiri. Kotero kwa masiku ena asanu ndi awiri anachita chikondwererocho mosangalala.
Et toute l'Assemblée fut d'avis de fêter sept autres jours, et ils fêtèrent [encore] sept jours dans la joie.
24 Hezekiya mfumu ya Yuda anapereka ngʼombe zamphongo 1,000 ndi nkhosa ndi mbuzi 7,000 ku msonkhanoko ndipo akuluakulu ake anapereka ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa ndi mbuzi 10,000. Ansembe ambiri anadziyeretsa.
Car Ézéchias, roi de Juda, offrit à l'Assemblée mille taureaux et sept mille moutons, et les princes offrirent à l'Assemblée mille taureaux et dix mille moutons; et les Prêtres en masse s'étaient mis en état de sainteté.
25 Gulu lonse la ku Yuda linasangalala, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ndi onse amene anasonkhana ochokera ku Israeli, kuphatikizanso alendo amene anachokera ku Israeli ndi amene amakhala ku Yuda.
Et toute l'Assemblée de Juda et les Prêtres et les Lévites et toute l'Assemblée venue d'Israël et les étrangers venus du pays d'Israël ou établis en Juda, se réjouirent.
26 Munali chikondwerero chachikulu mu Yerusalemu, pakuti kuyambira masiku a Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli sizinachitikepo zotere mu Yerusalemu.
Et il y eut grande réjouissance à Jérusalem, car depuis l'époque de Salomon, fils de David, roi d'Israël, il n'y avait rien eu de pareil à Jérusalem.
27 Ansembe ndi Alevi anayimirira kudalitsa anthu, ndipo Mulungu anawamvera pakuti pemphero lawo linafika kumwamba, malo ake oyera.
Et les Prêtres et les Lévites se levèrent et bénirent le peuple, et leur voix fut écoutée et leur prière parvint à Sa résidence sainte dans les Cieux.