< 2 Mbiri 18 >
1 Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu.
Now Josaphat was rich and very glorious, and was joined by affinity to Achab.
2 Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi
And he went down to him after some years to Samaria: and Achab at his coming killed sheep and oxen in abundance for him and the people that came with him: and he persuaded him to go up to Ramoth Galaad.
3 Ahabu mfumu ya Israeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti, “Kodi mudzapita nane kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi?” Yehosafati anayankha kuti, “Ine ndili ngati inu nomwe, ndi anthu anga ngati anthu anu. Ife tikhala nanu limodzi pa nkhondoyi.”
And Achab king of Israel said to Josaphat king of Juda: Come with me to Ramoth Galaad. And he answered him: Thou art as I am, and my people as thy people, and we will be with thee in the war.
4 Koma Yehosafati anatinso kwa mfumu ya Israeli, “Choyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
And Josaphat said to the king of Israel: Inquire, I beseech thee, at present the word of the Lord.
5 Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?” Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.”
So the king of Israel gathered together of the prophets four hundred men, and he said to them: Shall we go to Ramoth Galaad to fight, or shall we forbear? But they said: Go up, and God will deliver it into the king’s hand.
6 Koma Yehosafati anafunsanso kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene ife tingafunsireko?”
And Josaphat said: Is there not here a prophet of the Lord, that we may inquire also of him?
7 Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.” Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.”
And the king of Israel said to Josaphat: There is one man, of whom we may ask the will of the Lord: but I hate him, for he never prophesieth good to me, but always evil: and it is Micheas the son of Jemla. And Josaphat said: Speak not thus, O king.
8 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa akuluakulu ake ndipo inati, “Kamutengeni Mikaya mwana wa Imula, abwere msanga.”
And the king of Israel called one of the eunuchs, and said to him: Call quickly Micheas the son of Jemla.
9 Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.
Now the king of Israel, and Josaphat king of Juda, both sat on their thrones, clothed in royal robes, and they sat in the open court by the gate of Samaria, and all the prophets prophesied before them.
10 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’”
And Sedecias the son of Chanaana made him horns of iron, and said: Thus saith the Lord: With these shalt thou push Syria, till thou destroy it.
11 Aneneri ena onse amanenera chimodzimodzi kuti, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo kapambaneni, pakuti Mulungu adzamupereka mʼdzanja la mfumu.”
And all the prophets prophesied in like manner, and said: Go up to Ramoth Galaad, and thou shalt prosper, and the Lord will deliver them into the king’s hand.
12 Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”
And the messenger that went to call Micheas, said to him: Behold the words of all the prophets with one mouth declare good to the king: I beseech thee therefore let not thy word disagree with them, and speak thou also good success.
13 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndidzanena zimene Mulungu wanga andiwuze.”
And Micheas answered him: As the Lord liveth, whatsoever my God shall say to me, that will I speak.
14 Iye atafika mfumu inamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite ku nkhondo kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?” Iye anayankha kuti, “Kathireni nkhondo ndipo kapambaneni, pakuti mzindawo udzaperekedwa mʼdzanja lanu.”
So he came to the king: and the king said to him: Micheas, shall we go to Ramoth Galaad to fight, or forbear? And he answered him: Go up, for all shall succeed prosperously, and the enemies shall be delivered into your hands.
15 Mfumu inati kwa iye, “Kodi ndikuwuze kangati kuti ulumbire kuti usandiwuze chilichonse koma zoonadi mʼdzina la Yehova?”
And the king said: I adjure thee again and again to say nothing but the truth to me, in the name of the Lord.
16 Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’”
Then he said: I saw all Israel scattered in the mountains, like sheep without a shepherd: and the Lord said: These have no masters: let every man return to his own house in peace.
17 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti sandinenera zabwino koma zoyipa zokhazokha?”
And the king of Israel said to Josaphat: Did I not tell thee that this man would not prophesy me any good, but evil?
18 Mikaya anapitiriza ndi kunena kuti, “Imvani tsono mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu ndi gulu lonse lakumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi lamanzere.
Then he said: Hear ye therefore the word of the Lord: I saw the Lord sitting on his throne, and all the army of heaven standing by him on the right hand and on the left.
19 Ndipo Yehova anati, ‘Ndani amene adzamunyengerere Ahabu mfumu ya Israeli kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi ndi kukafera komweko?’ “Wina ananena zina, winanso ananena zina.”
And the Lord said: Who shall deceive Achab king of Israel, that he may go up and fall in Ramoth Galaad? And when one spoke in this manner, and another otherwise:
20 Pomaliza mzimu wina unatuluka ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, “Ine ndikamunyengerera!” Yehova anafunsa kuti, “Ukagwiritsa ntchito njira yanji?”
There came forth a spirit, and stood before the Lord, and said: I will deceive him. And the Lord said to him: By what means wilt thou deceive him?
21 Mzimuwo unati, “Ine ndidzapita ndi kukhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse!” Yehova anati, “‘Iwe ukamunyengadi iyeyo. Pita kachite zimenezo.’
And he answered: I will go out, and be a lying spirit in the mouth of all his prophets. And the Lord said: Thou shalt deceive, and shalt prevail: go out, and do so.
22 “Choncho Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa. Yehova waneneratu kuti inu mukaona tsoka.”
Now therefore behold the Lord hath put a spirit of lying in the mouth of all thy prophets, and the Lord hath spoken evil against thee.
23 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi ndi kumenya khofi Mikaya. Zedekiya anafunsa kuti, “Kodi mzimu wochokera kwa Yehova unadzera njira iti pamene unachoka kwa ine kupita kwa iwe?”
And Sedecias the son of Chanaana came, and struck Micheas on the cheek and said: Which way went the spirit of the Lord from me, to speak to thee?
24 Mikaya anayankha kuti, “Udzadziwa pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
And Micheas said: Thou thyself shalt see in that day, when thou shalt go in from chamber to chamber, to hide thyself.
25 Pamenepo mfumu ya Israeli inalamula kuti, “Tengani Mikaya ndipo mupite naye kwa Amoni, wolamulira mzindawo ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu,
And the king of Israel commanded, saying: Take Micheas, and carry him to Amen the governor of the city, and to Joas the son of Amelech,
26 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyike munthu uyu mʼndende ndipo musamupatse kanthu kalikonse koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwera mwamtendere.’”
And say: Thus saith the king: Put this fellow in prison, and give him bread and water in a small quantity till I return in peace.
27 Mikaya anayankhula kuti, “Ngati inu mukabwera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo anawonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”
And Micheas said: If thou return in peace, the Lord hath not spoken by me. And he said: Hear, all ye people.
28 Choncho mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi.
So the king of Israel and Josaphat king of Juda went up to Ramoth Galaad.
29 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Ine ndipita ku nkhondo modzibisa koma iwe uvale mikanjo yaufumu.” Kotero mfumu ya Israeli inadzibisa ndipo inapita ku nkhondoko.
And the king of Israel said to Josaphat: I will change my dress, and so I will go to the battle, but put thou on thy own garments. And the king of Israel having changed his dress, went to the battle.
30 Tsono mfumu ya Aramu inalamulira olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu koma mfumu ya Israeli yokha.”
Now the king of Syria had commanded the captains of his cavalry, saying: Fight ye not with small, or great, but with the king of Israel only.
31 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, iwo anaganiza kuti, “Mfumu ya Israeli ndi iyi.” Kotero anatembenuka kukamenyana naye koma Yehosafati anafuwula, ndipo Yehova anamuthandiza. Mulungu anawabweza mʼmbuyo,
So when the captains of the cavalry saw Josaphat, they said: This is the king of Israel. And they surrounded him to attack him: but he cried to the Lord, and he helped him, and turned them away from him.
32 pakuti olamulira magaleta ataona kuti sanali mfumu ya Israeli, anasiya kumuthamangitsa.
For when the captains of the cavalry saw, that he was not the king of Israel, they left him.
33 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndipo analasa mfumu ya Israeli pakati polumikizira malaya achitsulo. Mfumu inawuza oyendetsa galeta kuti, “Bwerera, undichotse pa nkhondo pano. Ndavulazidwa.”
And it happened that one of the people shot an arrow at a venture, and struck the king of Israel between the neck and the shoulders, and he said to his chariot man: Turn thy hand, and carry me out of the battle, for I am wounded.
34 Nkhondo inakula kwambiri tsiku lonse, ndipo mfumu ya Israeli inakhala tsonga mʼgaleta lake kuyangʼanana ndi Aaramu mpaka madzulo. Ndipo pamene dzuwa linkalowa inamwalira.
And the fight was ended that day: but the king of Israel stood in his chariot against the Syrians until the evening, and died at the sunset.