< 2 Mbiri 17 >
1 Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake ndipo anadzilimbitsa pofuna kulimbana ndi Israeli.
Josaphat, son fils, régna à sa place et se fortifia contre Israël.
2 Iye anayika magulu a asilikali mʼmizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, ndipo anamanga maboma mu Yuda ndi mʼmizinda yonse ya Efereimu imene Asa abambo ake analanda.
Il plaça des forces dans toutes les villes fortes de Juda, et il établit des garnisons dans le pays de Juda et dans les villes d'Ephraïm, dont Asa, son père, s'était emparé.
3 Yehova anali ndi Yehosafati chifukwa mʼzaka zoyambirira anatsatira makhalidwe a Davide abambo ake. Iye sanafunsire kwa Abaala.
Yahvé fut avec Josaphat, parce qu'il marcha dans les premières voies de David, son père, et qu'il ne chercha pas les Baals,
4 Koma anafunafuna Mulungu wa abambo ake ndipo anatsatira malamulo ake osati zochita za Israeli.
mais qu'il chercha le Dieu de son père, et qu'il marcha dans ses commandements, et non dans les voies d'Israël.
5 Yehova anakhazikitsa kolimba ufumuwo mʼmanja mwake ndipo Ayuda onse anabweretsa mphatso kwa Yehosafati, kotero kuti anali ndi chuma ndi ulemu wambiri.
C'est pourquoi Yahvé affermit le royaume entre ses mains. Tout Juda apportait un tribut à Josaphat, et il eut des richesses et des honneurs en abondance.
6 Mtima wake anawupereka kutsatira Yehova, kuwonjezera apo, anachotsa malo onse achipembedzo ndi mafano a Asera mu Yuda.
Son cœur s'élevait dans les voies de l'Éternel. Il fit disparaître de Juda les hauts lieux et les mâts d'ashère.
7 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wake, iye anatuma akuluakulu ake Beni-Haili, Obadiya, Zekariya, Netaneli ndi Mikaya kukaphunzitsa mʼmizinda ya Yuda.
La troisième année de son règne, il envoya ses chefs, Ben Haïl, Abdias, Zacharie, Nethaneel et Michée, enseigner dans les villes de Juda,
8 Pamodzi ndi iwo panali Alevi ena: Semaya, Netaniya, Zebadiya, Asaheli, Semiramoti, Yonatani, Adoniya, Tobiya ndi Tobu-Adoniya ndiponso ansembe Elisama ndi Yehoramu.
et avec eux des Lévites, Schemaeja, Nethania, Zebadia, Asaël, Schemiramoth, Jehonathan, Adonija, Tobija et Tobadonija, les Lévites, et avec eux Élischama et Joram, les prêtres.
9 Iwo anaphunzitsa mu Yuda monse atatenga Buku la Malamulo a Yehova iwo anayenda mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndipo anaphunzitsa anthu.
Ils enseignaient en Juda, ayant avec eux le livre de la loi de Yahvé. Ils parcoururent toutes les villes de Juda et enseignèrent parmi le peuple.
10 Kuopsa kwa Yehova kunali pa maufumu onse a mayiko oyandikana ndi Yuda, kotero kuti sanachite nkhondo ndi Yehosafati.
La crainte de Yahvé s'abattit sur tous les royaumes des pays qui entouraient Juda, de sorte qu'ils ne firent pas la guerre à Josaphat.
11 Afilisti ena anabweretsa kwa Yehosafati mphatso ndi siliva ngati msonkho, ndipo Aarabu anabweretsa ziweto: nkhosa zazimuna 7,700 ndi mbuzi 7,700.
Des Philistins apportèrent à Josaphat des présents et de l'argent en guise de tribut. Les Arabes lui apportèrent aussi des troupeaux: sept mille sept cents béliers et sept mille sept cents chèvres mâles.
12 Mphamvu za Yehosafati zinkakulirakulira. Iye anamanga malo otetezedwa ndi mizinda yosungiramo chuma mu Yuda
Josaphat devint extrêmement grand, et il bâtit en Juda des forteresses et des villes de commerce.
13 ndipo anali ndi katundu wambiri mʼmizinda ya Yuda. Iye anayikanso asilikali odziwa bwino nkhondo mu Yerusalemu.
Il eut de nombreux ouvrages dans les villes de Juda, et des hommes de guerre, des vaillants hommes, à Jérusalem.
14 Chiwerengero chawo potsata mabanja awo chinali chotere: kuchokera ku Yuda, atsogoleri a magulu 1,000; mtsogoleri Adina, anali ndi anthu 300,000 odziwa nkhondo;
Voici leur dénombrement, selon les maisons de leurs pères: De Juda, les chefs de milliers: Adna, chef, et avec lui trois cent mille vaillants hommes;
15 otsatana naye, mtsogoleri Yehohanani, anali ndi anthu 280,000;
à côté de lui, Jochanan, chef, et avec lui deux cent quatre-vingt mille hommes;
16 otsatana naye, Amasiya mwana wa Zikiri amene anadzipereka yekha kutumikira Yehova, anali ndi anthu 200,000.
à côté de lui, Amasia, fils de Zicri, qui s'offrit volontairement à l'Éternel, et avec lui deux cent mille vaillants hommes.
17 Kuchokera ku Benjamini: Eliada, msilikali wolimba mtima, anali ndi anthu 200,000 amene anali ndi mauta ndi zishango;
De Benjamin: Eliada, vaillant homme, et avec lui deux cent mille hommes armés de l'arc et du bouclier;
18 otsatana naye, Yehozabadi, anali ndi anthu 180,000 okonzekera nkhondo.
et à côté de lui Jehozabad, et avec lui cent quatre-vingt mille hommes prêts à faire la guerre.
19 Awa ndi anthu amene ankatumikira mfumu osawerengera amene anawayika mʼmizinda yotetezedwa mʼdziko lonse la Yuda.
Tels étaient ceux qui servaient le roi, sans compter ceux que le roi plaça dans les villes fortes de tout Juda.