< 2 Mbiri 14 >
1 Tsono Abiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Asa mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake ndipo pa masiku ake, dziko linakhala pa mtendere kwa zaka khumi.
2 Asa anachita zabwino ndi zolungama pamaso pa Yehova Mulungu wake.
3 Iye anachotsa maguwa achilendo ndi malo opembedzerapo mafano, anaphwanya zipilala za miyala yachipembedzo ndi kugwetsa mafano a Asera.
4 Asa analamula Yuda kuti afunefune Yehova Mulungu wa makolo awo ndi kumvera malamulo ndi zolamulira zake.
5 Iye anachotsa malo opembedzera mafano ndi maguwa ofukizira lubani mu mzinda uliwonse wa mu Yuda, ndipo mu ufumu wake munali mtendere pa nthawi ya ulamuliro wake.
6 Asa anamanga mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda pakuti dziko linali pa mtendere. Panalibe amene anachita naye nkhondo mʼzaka zimenezo, pakuti Yehova anamupatsa mpumulo.
7 Iye anati kwa Yuda “Tiyeni timange mizinda iyi ndipo timange makoma ndi nsanja, zitseko ndi zotchinga. Dzikoli likanali lathu chifukwa tafuna Yehova Mulungu wathu; tinamufuna Iye ndipo watipatsa mpumulo mbali zonse.” Kotero iwo anamanga ndi kukhala pa ulemerero.
8 Asa anali ndi ankhondo 300,000 ochokera ku Yuda, okhala ndi zishango zikuluzikulu ndi mikondo, ndiponso ankhondo 280,000 ochokera ku Benjamini, okhala ndi zishango ndi mauta. Onsewa anali ankhondo amphamvu ndi olimba mtima.
9 Zera wa ku Kusi anapita kukamenyana nawo ali ndi gulu lalikulu kwambiri la asilikali ndi magaleta 300 ndipo anafika mpaka ku Maresa.
10 Asa anapita kukakumana naye ndipo anakhala pa mizere yawo ya nkhondo mʼchigwa cha Zefata pafupi ndi Maresa.
11 Kenaka Asa anafuwulira Yehova Mulungu wake ndipo anati “Yehova palibe wina wofanana nanu kuti angathandize anthu opanda mphamvu pakati pa amphamvu. Tithandizeni Inu Yehova Mulungu wathu pakuti ife timadalira Inu ndipo mʼdzina lanu ife tabwera kudzalimbana ndi gulu la ankhondo lalikulu kwambiri ngati ili. Inu Yehova ndinu Mulungu wathu, musalole kuti munthu akupambaneni.”
12 Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Ayuda. Akusi anathawa,
13 ndipo Asa ndi ankhondo ake anawathamangitsa mpaka ku Gerari. Gulu lonse lalikulu lija la Akusi linaphedwa. Sanapezeke mmodzi wamoyo pakati pawo. Iwo anakanthidwa pamaso pa Yehova ndi asilikali ake. Anthu a ku Yuda anatenga katundu wambiri olanda ku nkhondo.
14 Iwo anawononga midzi yonse yozungulira Gerari pakuti mantha aakulu wochokera kwa Yehova anagwera anthuwo. Analanda katundu wa midzi yonse, popeza kunali katundu wambiri kumeneko.
15 Anakathiranso nkhondo misasa ya anthu oweta ziweto ndipo anatenga nkhosa zambiri, mbuzi ndi ngamira. Atatero anabwerera ku Yerusalemu.