< 2 Mbiri 12 >

1 Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova.
Une fois que Roboam eut affermi sa royauté et fut devenu puissant, il abandonna la Loi de l’Eternel, suivi de tout Israël.
2 Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu.
Dans la cinquième année du règne de Roboam, Sésak, roi d’Egypte, vint attaquer Jérusalem, parce qu’on était devenu infidèle au Seigneur;
3 Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto.
il disposait de douze cents chars, de soixante mille cavaliers. Innombrable était la multitude venue avec lui d’Egypte et composée de Libyens, de Soukkiites et d’Ethiopiens.
4 Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu.
Il s’empara des villes fortes de Juda et arriva jusqu’à Jérusalem.
5 Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’”
Alors Chemaya, le prophète, vint trouver Roboam et les grands de Juda qui s’étaient retirés à Jérusalem à l’approche de Sésak, et leur dit: "Ainsi parle le Seigneur: Vous m’avez abandonné, à mon tour je vous abandonne à la merci de Sésak."
6 Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.”
Les grands d’Israël et Roboam s’humilièrent et dirent: "L’Eternel est juste!"
7 Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki.
Le Seigneur, voyant qu’ils s’humiliaient, s’adressa à Chemaya en ces termes: "Ils se sont humiliés, je ne les détruirai point; mais encore un peu, j’assurerai leur salut, et mon courroux ne fondra pas sur Jérusalem par l’entremise de Sésak.
8 Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.”
Mais quand ils lui seront asservis, ils sauront ce que c’est de me servir ou de servir les royaumes étrangers."
9 Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga.
Sésak, roi d’Egypte, marcha donc contre Jérusalem: il s’empara des trésors de la maison du Seigneur et de ceux de la maison du roi, et emporta le tout. Il enleva aussi les boucliers d’or qu’avait fait faire Salomon.
10 Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu.
Le roi Roboam les remplaça par des boucliers de cuivre, dont il confia la garde aux chefs des coureurs chargés de surveiller l’entrée du palais royal.
11 Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda.
Chaque fois que le roi se rendait à la maison du Seigneur, les coureurs venaient porter les boucliers, puis les replaçaient dans leur salle de service.
12 Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda.
Comme il s’était humilié, la colère de l’Eternel se détourna de lui et n’acheva point sa ruine. Aussi bien, Juda avait conservé de bonnes qualités.
13 Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni.
Le roi Roboam s’affermit dans Jérusalem et continua de régner. En effet, Roboam était âgé de quarante et un ans à son avènement et il régna dix-sept ans à Jérusalem, la ville que le Seigneur avait choisie entre toutes les tribus d’Israël pour y faire dominer son nom. Sa mère se nommait Naama; elle était Ammonite.
14 Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova.
Il fit le mal, car il n’avait pas appliqué son cœur à rechercher l’Eternel.
15 Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu.
L’Histoire de Roboam, du début à la fin, se trouve consignée dans le récit du prophète Schemaya et du Voyant Iddo, avec les livres de généalogie. La guerre fut permanente entre Roboam et Jéroboam.
16 Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.
Roboam s’endormit avec ses pères et fut enseveli dans la Cité de David. Il eut pour successeur son fils Abiyya.

< 2 Mbiri 12 >