< 2 Mbiri 10 >

1 Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse anapita kumeneko kuti akamulonge ufumu.
וילך רחבעם שכמה כי שכם באו כל ישראל להמליך אתו
2 Yeroboamu mwana wa Nebati atamva zimenezi (Iye anali ku Igupto, kumene anapita pothawa mfumu Solomoni) anabwerako kuchokera ku Igupto.
ויהי כשמע ירבעם בן נבט והוא במצרים אשר ברח מפני שלמה המלך--וישב ירבעם ממצרים
3 Kotero anthu anakayitana Yeroboamu ndipo iye ndi Aisraeli onse anapita kwa Rehobowamu ndi kumuwuza kuti,
וישלחו ויקראו לו ויבא ירבעם וכל ישראל וידברו אל רחבעם לאמר
4 “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”
אביך הקשה את עלנו ועתה הקל מעבודת אביך הקשה ומעלו הכבד אשר נתן עלינו--ונעבדך
5 Rehobowamu anayankha kuti, “Mukabwerenso pakapita masiku atatu.” Choncho anthuwo anachoka.
ויאמר אלהם עוד שלשת ימים--ושובו אלי וילך העם
6 Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”
ויועץ המלך רחבעם את הזקנים אשר היו עמדים לפני שלמה אביו בהיתו חי לאמר איך אתם נועצים להשיב לעם הזה דבר
7 Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.”
וידברו אליו לאמר אם תהיה לטוב להעם הזה ורציתם ודברת אלהם דברים טובים--והיו לך עבדים כל הימים
8 Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira.
ויעזב את עצת הזקנים אשר יעצהו ויועץ את הילדים אשר גדלו אתו העמדים לפניו
9 Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ndi otani? Kodi tiwayankhe chiyani anthu amene akunena kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anayika pa ife?’”
ויאמר אלהם מה אתם נועצים ונשיב דבר את העם הזה אשר דברו אלי לאמר הקל מן העל אשר נתן אביך עלינו
10 Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga.
וידברו אתו הילדים אשר גדלו אתו לאמר כה תאמר לעם אשר דברו אליך לאמר אביך הכביד את עלנו ואתה הקל מעלינו כה תאמר אלהם קטני עבה ממתני אבי
11 Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’”
ועתה אבי העמיס עליכם על כבד ואני אסיף על עלכם אבי יסר אתכם בשוטים ואני בעקרבים
12 Tsiku lachitatu Yeroboamu ndi anthu onse anabwerera kwa Rehobowamu monga ananenera mfumu kuti, “Mukabwerenso kwa ine pakapita masiku atatu.”
ויבא ירבעם וכל העם אל רחבעם ביום השלשי כאשר דבר המלך לאמר שובו אלי ביום השלשי
13 Mfumu inawayankha mwankhanza, pokana malangizo a akuluakulu aja.
ויענם המלך קשה ויעזב המלך רחבעם את עצת הזקנים
14 Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.”
וידבר אלהם כעצת הילדים לאמר אכביד את עלכם ואני אסיף עליו אבי יסר אתכם בשוטים ואני בעקרבים
15 Kotero mfumu sinamvere anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Mulungu, kukwaniritsa mawu amene Yehova ananena kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
ולא שמע המלך אל העם כי היתה נסבה מעם האלהים--למען הקים יהוה את דברו אשר דבר ביד אחיהו השלוני אל ירבעם בן נבט
16 Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide, gawo lanji mwa mwana wa Yese? Inu Aisraeli! Pitani kwanu. Iwe Davide! Yangʼana banja lako.” Kotero Aisraeli onse anapita kwawo.
וכל ישראל כי לא שמע המלך להם וישיבו העם את המלך לאמר מה לנו חלק בדויד ולא נחלה בבן ישי איש לאהליך ישראל עתה ראה ביתך דויד וילך כל ישראל לאהליו
17 Koma Rehobowamu anakhala akulamulirabe Aisraeli amene amakhala mʼmizinda ya Yuda.
ובני ישראל הישבים בערי יהודה--וימלך עליהם רחבעם
18 Mfumu Rehobowamu inatuma Hadoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli anamugenda miyala ndi kumupha. Koma mfumu Rehobowamu anakwera galeta lake ndi kuthawira ku Yerusalemu.
וישלח המלך רחבעם את הדרם אשר על המס וירגמו בו בני ישראל אבן וימת והמלך רחבעם התאמץ לעלות במרכבה לנוס ירושלם
19 Motero Israeli wakhala akuwukira banja la Davide mpaka lero lino.
ויפשעו ישראל בבית דויד עד היום הזה

< 2 Mbiri 10 >