< 1 Timoteyo 6 >
1 Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu.
Let as many as are servants under the yoke account their own masters worthy of all honor; that the name of God and his doctrine may not be blasphemed:
2 Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu.
and let not those who have believing masters, despise them, because they are brethren; but serve them more readily, because they are faithful and beloved by God, partakers of his grace.
3 Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu,
These things teach and exhort. If any one teach otherwise, and adhere not to the sound words of our Lord Jesus Christ, and the doctrine which is according to godliness;
4 ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa,
he is proud, knowing nothing, but is delirious about questions and strifes of words: from which cometh envy, contention, calumnies, wicked suspicions, perverse debates of men corrupted in mind,
5 ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.
and void of truth, accounting gain to be godliness: from such withdraw thyself.
6 Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu.
But godliness with contentment is great gain.
7 Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi.
For we brought nothing into the world, and it is certain that we can carry nothing out:
8 Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
having therefore food and raiment, let us be herewith content.
9 Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko.
But they, that will be rich, fall into temptation and a snare, and into many foolish and hurtful lusts, which plunge men into ruin and perdition.
10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
For the love of money is the root of all evils, which some coveting after have been led astray from the faith, and pierced themselves through with many sorrows.
11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.
But do thou, O man of God, flee these things, and follow after righteousness, piety, fidelity, love, patience, meekness.
12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. (aiōnios )
Maintain the glorious combat of faith, lay hold on eternal life, to which thou hast been called, and hast made a good profession before many witnesses. (aiōnios )
13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni.
I charge thee before God, who giveth life to all, and before Christ Jesus who witnessed a good confession before Pontius Pilate,
14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera.
that thou keep this commandment, unspotted and blameless, till the appearance of our Lord Jesus Christ;
15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye.
which He will manifest in his own times, who is the blessed and only potentate, the King of kings, and Lord of lords,
16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni. (aiōnios )
who alone hath immortality, dwelling in light inaccessible, whom no man hath seen, nor can see: to whom be honor and power everlasting. Amen. (aiōnios )
17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. (aiōn )
Charge them, that are rich in this world, not to be high-minded nor trust in uncertain riches, but in the living God, who richly affords us all things for enjoyment: charge them to do good, (aiōn )
18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo.
to be rich in good works, to be ready to distribute, willing to communicate;
19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.
treasuring up to themselves a good foundation for the future, that they may obtain eternal life.
20 Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru.
O Timothy, keep that with which thou art entrusted, avoiding profane empty babblings, and the oppositions of science falsely so called:
21 Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo. Chisomo chikhale nawe.
which some pretending to, have erred from the faith. Grace be with thee. Amen.