< 1 Timoteyo 6 >

1 Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu.
Koji su pod jarmom, robovi, neka svoje gospodare smatraju svake časti dostojnima da se ne bi pogrđivalo ime Božje i nauk.
2 Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu.
A oni kojima su gospodari vjernici, neka ih ne cijene manje zato što su braća, nego neka im još više služe jer ti koji primaju njihovo dobročinstvo vjernici su i ljubljena braća. To naučavaj i preporučuj!
3 Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu,
A tko drukčije naučava i ne prianja uza zdrave riječi, riječi Gospodina našega Isusa Krista, i nauk u skladu s pobožnošću,
4 ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa,
nadut je, puka neznalica, samo boluje od raspra i rječoborstava, od kojih nastaje zavist, svađa, pogrde, zla sumnjičenja,
5 ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.
razračunavanja ljudi pokvarene pameti i lišenih istine, što pobožnost smatraju dobitkom.
6 Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu.
Pa i jest dobitak velik pobožnost, zadovoljna onim što ima!
7 Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi.
Ta ništa nismo donijeli na svijet te iz njega ništa ni iznijeti ne možemo!
8 Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire.
Imamo li dakle hranu i odjeću, zadovoljimo se time.
9 Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko.
Jer oni koji se hoće bogatiti, upadaju u napast, zamku i mnoge nerazumne i štetne požude što ljude strovaljuju u zator i propast.
10 Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.
Zaista, korijen svih zala jest srebroljublje; njemu odani, mnogi odlutaše od vjere i sami sebe isprobadaše mukama mnogima.
11 Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa.
A ti se, Božji čovječe, toga kloni! Teži za pravednošću, pobožnošću, vjerom, ljubavlju, postojanošću, krotkošću!
12 Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. (aiōnios g166)
Bij dobar boj vjere, osvoji vječni život na koji si pozvan i radi kojega si dao ono lijepo svjedočanstvo pred mnogim svjedocima! (aiōnios g166)
13 Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni.
Zapovijedam pred Bogom koji svemu život daje i pred Kristom Isusom koji pred Poncijem Pilatom posvjedoči lijepo svjedočanstvo:
14 Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera.
čuvaj Zapovijed, neokaljano i besprijekorno, do Pojavka Gospodina našega Isusa Krista.
15 Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye.
Njega će u svoje vrijeme pokazati On, Blaženi i jedini Vladar, Kralj kraljeva i Gospodar gospodara,
16 Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni. (aiōnios g166)
koji jedini ima besmrtnost, prebiva u svjetlu nedostupnu, koga nitko od ljudi ne vidje niti ga vidjeti može. Njemu čast i vlast vjekovječna! Amen. (aiōnios g166)
17 Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. (aiōn g165)
Onima koji su u sadašnjem svijetu bogati zapovijedaj neka ne budu bahati i neka se ne uzdaju u nesigurno bogatstvo, nego u Boga koji nam sve bogato daje na uživanje; (aiōn g165)
18 Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo.
neka dobro čine, neka se bogate dobrim djelima, neka budu darežljivi, zajedničari -
19 Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.
prikupljajući sebi lijepu glavnicu za budućnost da osvoje onaj pravi život.
20 Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru.
Timoteju, poklad čuvaj kloneći se svjetovnoga praznoglasja i proturječja nekog nazovispoznanja,
21 Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo. Chisomo chikhale nawe.
koje su neki ispovijedali pa od vjere zastranili. Milost s vama

< 1 Timoteyo 6 >