< 1 Timoteyo 5 >
1 Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako.
Πρεσβυτέρῳ μὴ ἐπιπλήξῃς ἀλλὰ παρακάλει ὡς πατέρα, νεωτέρους ὡς ἀδελφούς,
2 Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.
πρεσβυτέρας ὡς μητέρας, νεωτέρας ὡς ἀδελφὰς ἐν πάσῃ ἁγνείᾳ.
3 Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha.
χήρας τίμα τὰς ὄντως χήρας.
4 Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu.
εἰ δέ τις χήρα τέκνα ἢ ἔκγονα ἔχει, μανθανέτωσαν πρῶτον τὸν ἴδιον οἶκον εὐσεβεῖν καὶ ἀμοιβὰς ἀποδιδόναι τοῖς προγόνοις· τοῦτο γάρ ἐστιν (καλὸν καὶ *K*) ἀπόδεκτον ἐνώπιον τοῦ θεοῦ.
5 Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza.
Ἡ δὲ ὄντως χήρα καὶ μεμονωμένη ἤλπικεν ἐπὶ (τὸν *ko*) θεὸν καὶ προσμένει ταῖς δεήσεσιν καὶ ταῖς προσευχαῖς νυκτὸς καὶ ἡμέρας·
6 Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo.
ἡ δὲ σπαταλῶσα ζῶσα τέθνηκεν.
7 Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa.
καὶ ταῦτα παράγγελλε, ἵνα ἀνεπίλημπτοι ὦσιν.
8 Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.
Εἰ δέ τις τῶν ἰδίων καὶ μάλιστα (τῶν *k*) οἰκείων οὐ (προνοεῖ, *N(k)O*) τὴν πίστιν ἤρνηται καὶ ἔστιν ἀπίστου χείρων.
9 Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha.
χήρα καταλεγέσθω μὴ ἔλαττον ἐτῶν ἑξήκοντα γεγονυῖα ἑνὸς ἀνδρὸς γυνή,
10 Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.
ἐν ἔργοις καλοῖς μαρτυρουμένη, εἰ ἐτεκνοτρόφησεν, εἰ ἐξενοδόχησεν, εἰ ἁγίων πόδας ἔνιψεν, εἰ θλιβομένοις ἐπήρκεσεν, εἰ παντὶ ἔργῳ ἀγαθῷ ἐπηκολούθησεν.
11 Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso.
νεωτέρας δὲ χήρας παραιτοῦ· ὅταν γὰρ καταστρηνιάσωσιν τοῦ Χριστοῦ, γαμεῖν θέλουσιν
12 Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba.
ἔχουσαι κρίμα, ὅτι τὴν πρώτην πίστιν ἠθέτησαν·
13 Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba.
ἅμα δὲ καὶ ἀργαὶ μανθάνουσιν περιερχόμεναι τὰς οἰκίας. οὐ μόνον δὲ ἀργαί, ἀλλὰ καὶ φλύαροι καὶ περίεργοι, λαλοῦσαι τὰ μὴ δέοντα.
14 Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza
Βούλομαι οὖν νεωτέρας γαμεῖν, τεκνογονεῖν, οἰκοδεσποτεῖν, μηδεμίαν ἀφορμὴν διδόναι τῷ ἀντικειμένῳ λοιδορίας χάριν·
15 Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana.
ἤδη γάρ τινες ἐξετράπησαν ὀπίσω τοῦ σατανᾶ.
16 Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha.
εἴ τις (πιστὸς ἢ *K*) πιστὴ ἔχει χήρας, (ἐπαρκείτω *NK(o)*) αὐταῖς καὶ μὴ βαρείσθω ἡ ἐκκλησία, ἵνα ταῖς ὄντως χήραις ἐπαρκέσῃ.
17 Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa.
Οἱ καλῶς προεστῶτες πρεσβύτεροι διπλῆς τιμῆς ἀξιούσθωσαν μάλιστα οἱ κοπιῶντες ἐν λόγῳ καὶ διδασκαλίᾳ·
18 Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.”
λέγει γὰρ ἡ γραφή· βοῦν ἀλοῶντα οὐ φιμώσεις· καὶ ἄξιος ὁ ἐργάτης τοῦ μισθοῦ αὐτοῦ.
19 Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu.
κατὰ πρεσβυτέρου κατηγορίαν μὴ παραδέχου ἐκτὸς εἰ μὴ ἐπὶ δύο ἢ τριῶν μαρτύρων.
20 Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo.
τοὺς (δὲ *o*) ἁμαρτάνοντας ἐνώπιον πάντων ἔλεγχε, ἵνα καὶ οἱ λοιποὶ φόβον ἔχωσιν.
21 Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.
Διαμαρτύρομαι ἐνώπιον τοῦ θεοῦ καὶ (κυρίου *K*) Χριστοῦ Ἰησοῦ καὶ τῶν ἐκλεκτῶν ἀγγέλων, ἵνα ταῦτα φυλάξῃς χωρὶς προκρίματος μηδὲν ποιῶν κατὰ πρόσκλισιν.
22 Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako.
χεῖρας ταχέως μηδενὶ ἐπιτίθει μηδὲ κοινώνει ἁμαρτίαις ἀλλοτρίαις, σεαυτὸν ἁγνὸν τήρει.
23 Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.
μηκέτι ὑδροπότει, ἀλλ᾽ οἴνῳ ὀλίγῳ χρῶ διὰ τὸν στόμαχον (σου *K*) καὶ τὰς πυκνάς σου ἀσθενείας.
24 Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo.
τινῶν ἀνθρώπων αἱ ἁμαρτίαι πρόδηλοί εἰσιν προάγουσαι εἰς κρίσιν· τισὶν δὲ καὶ ἐπακολουθοῦσιν.
25 Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingatheke kubisika.
ὡσαύτως καὶ τὰ ἔργα τὰ καλὰ πρόδηλα (ἐστίν *k*) καὶ τὰ ἄλλως ἔχοντα κρυβῆναι οὐ (δύνανται. *N(k)O*)