< 1 Timoteyo 2 >

1 Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika.
παρακαλω ουν πρωτον παντων ποιεισθαι δεησεις προσευχας εντευξεις ευχαριστιας υπερ παντων ανθρωπων
2 Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima.
υπερ βασιλεων και παντων των εν υπεροχη οντων ινα ηρεμον και ησυχιον βιον διαγωμεν εν παση ευσεβεια και σεμνοτητι
3 Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu,
τουτο γαρ καλον και αποδεκτον ενωπιον του σωτηρος ημων θεου
4 amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi.
ος παντας ανθρωπους θελει σωθηναι και εις επιγνωσιν αληθειας ελθειν
5 Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu.
εις γαρ θεος εις και μεσιτης θεου και ανθρωπων ανθρωπος χριστος ιησους
6 Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera.
ο δους εαυτον αντιλυτρον υπερ παντων το μαρτυριον καιροις ιδιοις
7 Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona.
εις ο ετεθην εγω κηρυξ και αποστολος αληθειαν λεγω εν χριστω ου ψευδομαι διδασκαλος εθνων εν πιστει και αληθεια
8 Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana.
βουλομαι ουν προσευχεσθαι τους ανδρας εν παντι τοπω επαιροντας οσιους χειρας χωρις οργης και διαλογισμου
9 Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali.
ωσαυτως και τας γυναικας εν καταστολη κοσμιω μετα αιδους και σωφροσυνης κοσμειν εαυτας μη εν πλεγμασιν η χρυσω η μαργαριταις η ιματισμω πολυτελει
10 Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu.
αλλ ο πρεπει γυναιξιν επαγγελλομεναις θεοσεβειαν δι εργων αγαθων
11 Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu.
γυνη εν ησυχια μανθανετω εν παση υποταγη
12 Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete.
γυναικι δε διδασκειν ουκ επιτρεπω ουδε αυθεντειν ανδρος αλλ ειναι εν ησυχια
13 Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava.
αδαμ γαρ πρωτος επλασθη ειτα ευα
14 Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa.
και αδαμ ουκ ηπατηθη η δε γυνη απατηθεισα εν παραβασει γεγονεν
15 Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse.
σωθησεται δε δια της τεκνογονιας εαν μεινωσιν εν πιστει και αγαπη και αγιασμω μετα σωφροσυνης

< 1 Timoteyo 2 >