< 1 Atesalonika 3 >
1 Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene.
C'est pourquoi, ne pouvant plus attendre, nous avons mieux aimé rester seuls à Athènes,
2 Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu,
et vous envoyer Timothée, notre frère, serviteur de Dieu et ministre de l'Évangile du Christ, pour vous affermir et vous encourager dans votre foi,
3 ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi.
afin qu'aucun de vous ne soit ébranlé par de telles afflictions; car, vous le savez vous-mêmes, c'est à cela que nous sommes destinés.
4 Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi.
Et lorsque nous étions auprès de vous, nous vous avons dit d'avance que nous aurions des afflictions à souffrir, comme cela est arrivé, et vous le savez bien.
5 Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula.
Ne pouvant donc attendre plus longtemps, j'envoyai Timothée pour être informé de l'état de votre foi, craignant que le Tentateur ne vous eût tentés et que notre travail ne fût devenu inutile.
6 Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo.
Mais Timothée, qui vient d'arriver ici de chez vous, nous a donné de bonnes nouvelles de votre foi et de votre charité. Il nous a dit le bon souvenir que vous gardez toujours de nous, et le désir que vous avez de nous voir, comme nous désirons aussi vous voir nous-mêmes.
7 Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa.
Ainsi, frères, au milieu de toutes nos peines et de toutes nos afflictions, vous avez été pour nous, par votre foi, un sujet de consolation.
8 Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye.
Car nous vivons maintenant, puisque vous demeurez fermes dans le Seigneur.
9 Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu?
Et comment pourrions-nous assez rendre grâces à Dieu à votre sujet, pour toute la joie dont nous sommes comblés à cause de vous, en la présence de notre Dieu?
10 Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu.
Nous lui demandons nuit et jour, très instamment, de nous permettre de vous revoir, et d'ajouter ce qui manque encore à votre foi.
11 Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko.
Que Dieu lui-même, notre Père, et Jésus, notre Seigneur, dirigent nos pas vers vous!
12 Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu.
Et que le Seigneur fasse croître et abonder votre charité les uns pour les autres et à l'égard de tous, comme il en est de nous-mêmes à votre égard,
13 Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse.
afin que vos coeurs soient affermis, et qu'ils soient irrépréhensibles dans la sainteté devant Dieu, notre Père, lorsque notre Seigneur Jésus viendra avec tous ses saints!