< 1 Atesalonika 2 >
1 Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa.
2 Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe.
3 Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani.
4 Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu.
5 Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu.
6 Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu.
7 Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu. Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono,
8 moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu.
9 Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu.
10 Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira.
11 Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake,
12 kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero.
13 Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira.
14 Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda,
15 amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse
16 ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano.
17 Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni.
18 Pakuti ife tinafuna kubweranso kwa inu, makamaka ine Paulo, ndinayesa kangapo koma Satana anatiletsa.
19 Nanga chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu kapena chaufumu chimene ife tidzanyadira pamaso pa Ambuye athu Yesu Khristu pamene abwere ndi chiyani? Kodi si inu?
20 Indedi, inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe.