< 1 Samueli 7 >

1 Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.
ויבאו אנשי קרית יערים ויעלו את ארון יהוה ויבאו אתו אל בית אבינדב בגבעה ואת אלעזר בנו קדשו לשמר את ארון יהוה׃
2 Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize.
ויהי מיום שבת הארון בקרית יערים וירבו הימים ויהיו עשרים שנה וינהו כל בית ישראל אחרי יהוה׃
3 Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.”
ויאמר שמואל אל כל בית ישראל לאמר אם בכל לבבכם אתם שבים אל יהוה הסירו את אלהי הנכר מתוככם והעשתרות והכינו לבבכם אל יהוה ועבדהו לבדו ויצל אתכם מיד פלשתים׃
4 Choncho Aisraeli anachotsa milungu yawo ya Baala ndi Asitoreti ndi kutumikira Yehova yekha.
ויסירו בני ישראל את הבעלים ואת העשתרת ויעבדו את יהוה לבדו׃
5 Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.”
ויאמר שמואל קבצו את כל ישראל המצפתה ואתפלל בעדכם אל יהוה׃
6 Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa.
ויקבצו המצפתה וישאבו מים וישפכו לפני יהוה ויצומו ביום ההוא ויאמרו שם חטאנו ליהוה וישפט שמואל את בני ישראל במצפה׃
7 Afilisti anamva kuti Aisraeli asonkhana ku Mizipa, choncho akalonga awo anabwera kudzawathira nkhondo. Ndipo Aisraeli atamva anachita mantha chifukwa cha Afilisti.
וישמעו פלשתים כי התקבצו בני ישראל המצפתה ויעלו סרני פלשתים אל ישראל וישמעו בני ישראל ויראו מפני פלשתים׃
8 Choncho anati kwa Samueli, “Musasiye kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti atipulumutse mʼdzanja la Afilistiwa.”
ויאמרו בני ישראל אל שמואל אל תחרש ממנו מזעק אל יהוה אלהינו וישענו מיד פלשתים׃
9 Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha.
ויקח שמואל טלה חלב אחד ויעלה עולה כליל ליהוה ויזעק שמואל אל יהוה בעד ישראל ויענהו יהוה׃
10 Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa.
ויהי שמואל מעלה העולה ופלשתים נגשו למלחמה בישראל וירעם יהוה בקול גדול ביום ההוא על פלשתים ויהמם וינגפו לפני ישראל׃
11 Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari.
ויצאו אנשי ישראל מן המצפה וירדפו את פלשתים ויכום עד מתחת לבית כר׃
12 Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.”
ויקח שמואל אבן אחת וישם בין המצפה ובין השן ויקרא את שמה אבן העזר ויאמר עד הנה עזרנו יהוה׃
13 Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli. Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli.
ויכנעו הפלשתים ולא יספו עוד לבוא בגבול ישראל ותהי יד יהוה בפלשתים כל ימי שמואל׃
14 Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori.
ותשבנה הערים אשר לקחו פלשתים מאת ישראל לישראל מעקרון ועד גת ואת גבולן הציל ישראל מיד פלשתים ויהי שלום בין ישראל ובין האמרי׃
15 Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse.
וישפט שמואל את ישראל כל ימי חייו׃
16 Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa.
והלך מדי שנה בשנה וסבב בית אל והגלגל והמצפה ושפט את ישראל את כל המקומות האלה׃
17 Koma pambuyo pake ankabwerera ku Rama, kumene kunali nyumba yake. Ankaweruza Aisraeli kumeneko. Ndipo iye anamanga guwa lansembe la Yehova kumeneko.
ותשבתו הרמתה כי שם ביתו ושם שפט את ישראל ויבן שם מזבח ליהוה׃

< 1 Samueli 7 >