< 1 Samueli 19 >

1 Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide.
撒烏耳曾對兒子約納堂和臣僕提過,他願殺達味;但撒烏耳的兒子約納堂很愛達味,
2 Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko.
就警告達味說:「我父親想殺害你,現今請你明晨多加小心,躲藏在一個隱密的地方。
3 Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.”
我去陪我到你所在的田間,向我父親向你說情,看情形怎樣,然後告訴你」。
4 Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri.
於是約納堂向他父親提及達味的長處,對他說:「君王不要得罪的僕人達味,因為他沒有得罪你,並且他所行的,都是對你很有利的事。
5 Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?”
他冒著性命的危險,去殺了那培肋舍特人;上主藉他使以色列獲得了這樣大的勝利,你親自看見了,也很喜歡;為什麼你要犯罪,流無辜者的血,無緣無故殺害達味﹖」
6 Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.”
撒烏耳就聽了約納堂的話,並且發誓說:「上主永在,他必不死! 」
7 Pambuyo pake Yonatani anayitana Davide namuwuza zonsezi. Choncho Yonatani anabwera naye Davide kwa Sauli ndipo ankamutumikira Sauliyo monga kale.
約納堂便叫回達味,告訴他這一切話,並且領他到撒烏耳前;就如和先前一樣,侍立在君王左右。
8 Panabukanso nkhondo ina ndipo Davide anapita ndi kukamenyana ndi Afilisti. Iye anawakantha mwamphamvu kotero kuti Afilisti anathawa.
再次爆發了戰爭,達味又出征攻打培肋舍特人,打得他們大敗,他們都從他面前逃散了。
9 Tsiku lina mzimu woyipa uja unafikanso pa Sauli. Nthawi imeneyi nʼkuti Sauli uja ali mʼnyumba mwake, mkondo uli mʼdzanja lake ndi Davide akuyimba zeze,
惡神由上主那裏又降在撒烏耳身上;有一天,君王在家中坐著,手中拿槍,同時達味正在彈琴。
10 Sauli anafuna kumubaya Davide ndi kumukhomera kukhoma, koma Davide anapewa mkondowo kotero Sauli anakabaya pa khoma. Usiku womwewo Davide anathawa.
撒烏耳想用槍把達味釘在牆上,但達味立刻由撒烏耳面前躲開,君王把槍釘在牆上,達味就逃跑了,沒有喪命。
11 Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.”
那一夜,撒烏耳派差役去看守達味的家,要在早晨殺死他。他的妻子米加耳警告他說:「今夜你不逃命,明日你就沒有命了」。
12 Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka.
米加耳把達味從窗口縋下去,他便逃跑了,救了命。
13 Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu.
米加耳隨即把神像放在床上,用毛毯把頭蓋上,又蓋上一件衣服。
14 Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, “Davide akudwala.”
當撒烏耳派差役去捉拿達味時,米加耳說:「達味病了」。
15 Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, “Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe.”
撒烏耳再派差役去看達味說:「將達味連床帶到這裏來,我要殺死他」。
16 Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake.
差役進去,見是「神像」躺在床上,有張毛毯蓋著頭。
17 Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?” Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’”
因此,撒烏耳對米加耳說:「妳為什麼這樣欺騙我﹖放走了我的仇人,叫他逃命」。米加耳回答撒烏耳說:「他對我說:放我走,不然我要殺妳! 」
18 Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti.
達味死裏逃生,到了辣瑪,去見撒慕爾,向他報告了撒烏耳對他所行的一切;然後他便和撒慕爾去了納約特,住在那裏。
19 Sauli anamva kuti, “Davide ali ku Nayoti ku Rama.”
有人告訴撒烏耳說:「看,達味住在辣瑪的納約特」。
20 Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera.
撒烏耳又派差役去捉拿達味,但是他們看見一大群先知正在出神說妙語,撒慕爾站在他們面前作領導;這些天主的神也降在撒烏耳的差役身上,他們也出神說起妙語來。
21 Sauli atamva zimenezi anatumizanso anthu ena, koma nawonso anayamba kulosa. Anatumanso anthu ena kachitatu, koma nawonso anayamba kulosa.
有人將此事撒烏耳,他又打發別的差役去,他們也出神說開了妙語。撒烏耳第三次又打發差役去,他們也出神說開了妙語。
22 Pomaliza Sauli mwini wake ananyamuka kupita ku Rama ndipo anafika ku chitsime chachikulu cha ku Seku. Ndipo anafunsa, “Samueli ndi Davide ali kuti?” Munthu wina anamuyankha kuti, “Ali ku Nayoti ku Rama.”
撒烏耳大發憤怒,便親自去了辣瑪;當他到了色雇的大井那裏,就問說:「撒慕爾和達味在哪裏﹖」有人答說:「在辣瑪的納約特」。
23 Choncho Sauli anapita ku Nayoti ku Rama. Koma Mzimu wa Mulungu unafikanso pa iye ndipo ankalosa akuyenda mpaka anafika ku Nayoti.
他就從那裏起身往辣瑪納約特去;那時天主的神也降到他身上,所以他一邊走,一邊說妙語,一直到了辣瑪納約特。
24 Nayenso anavula zovala zake nayamba kulosa pamaso pa Samueli. Kenaka anagona wamaliseche tsiku lonse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amati, “Kodi Sauli alinso mmodzi wa aneneri?”
並且他還脫去衣服,在撒慕爾面前出神說起妙語來,赤裸裸地一天一夜躺在地上:因此有句俗語說:「不是撒烏耳也列在先知中嗎﹖」

< 1 Samueli 19 >