< 1 Samueli 18 >

1 Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha.
大衛對掃羅說完了話,約拿單的心與大衛的心深相契合。約拿單愛大衛,如同愛自己的性命。
2 Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake.
那日掃羅留住大衛,不容他再回父家。
3 Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera.
約拿單愛大衛如同愛自己的性命,就與他結盟。
4 Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba.
約拿單從身上脫下外袍,給了大衛,又將戰衣、刀、弓、腰帶都給了他。
5 Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli.
掃羅無論差遣大衛往何處去,他都做事精明。掃羅就立他作戰士長,眾百姓和掃羅的臣僕無不喜悅。
6 Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira.
大衛打死了那非利士人,同眾人回來的時候,婦女們從以色列各城裏出來,歡歡喜喜,打鼓擊磬,歌唱跳舞,迎接掃羅王。
7 Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati: “Sauli wapha 1,000, Koma Davide wapha miyandamiyanda.”
眾婦女舞蹈唱和,說:「掃羅殺死千千,大衛殺死萬萬。」
8 Koma Sauli anapsa mtima kwambiri ndipo mawu amenewa anamuyipira. Iye anati, “Iwo amuwerengera Davide miyandamiyanda, koma ine 1,000 okha. Nanga chatsalanso nʼchiyani kuti atenge? Si ufumu basi?”
掃羅甚發怒,不喜悅這話,就說:「將萬萬歸大衛,千千歸我,只剩下王位沒有給他了。」
9 Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide.
從這日起,掃羅就怒視大衛。
10 Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake.
次日,從上帝那裏來的惡魔大大降在掃羅身上,他就在家中胡言亂語。大衛照常彈琴,掃羅手裏拿着槍。
11 Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse.
掃羅把槍一掄,心裏說,我要將大衛刺透,釘在牆上。大衛躲避他兩次。
12 Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli.
掃羅懼怕大衛;因為耶和華離開自己,與大衛同在。
13 Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa.
所以掃羅使大衛離開自己,立他為千夫長,他就領兵出入。
14 Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye.
大衛做事無不精明,耶和華也與他同在。
15 Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri.
掃羅見大衛做事精明,就甚怕他。
16 Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo.
但以色列和猶大眾人都愛大衛,因為他領他們出入。
17 Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!”
掃羅對大衛說:「我將大女兒米拉給你為妻,只要你為我奮勇,為耶和華爭戰。」掃羅心裏說:「我不好親手害他,要藉非利士人的手害他。」
18 Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?”
大衛對掃羅說:「我是誰,我是甚麼出身,我父家在以色列中是何等的家,豈敢作王的女婿呢?」
19 Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire.
掃羅的女兒米拉到了當給大衛的時候,掃羅卻給了米何拉人亞得列為妻。
20 Koma Mikala mwana wamkazi wa Sauli anamukonda Davide ndipo Sauli atamva za zimenezi, anakondwera.
掃羅的次女米甲愛大衛。有人告訴掃羅,掃羅就喜悅。
21 Sauli ankaganiza kuti, “Ndimupatse amukwatire kuti akhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo adzaphedwe ndi Afilisti.” Choncho Sauli anawuza Davide kachiwiri, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.”
掃羅心裏說:「我將這女兒給大衛,作他的網羅,好藉非利士人的手害他。」所以掃羅對大衛說:「你今日可以第二次作我的女婿。」
22 Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’”
掃羅吩咐臣僕說:「你們暗中對大衛說:『王喜悅你,王的臣僕也都喜愛你,所以你當作王的女婿。』」
23 Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.”
掃羅的臣僕就照這話說給大衛聽。大衛說:「你們以為作王的女婿是一件小事嗎?我是貧窮卑微的人。」
24 Nduna za Sauli zinamuwuza zonse zimene anayankha Davide.
掃羅的臣僕回奏說,大衛所說的如此如此。
25 Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti.
掃羅說:「你們要對大衛這樣說:『王不要甚麼聘禮,只要一百非利士人的陽皮,好在王的仇敵身上報仇。』」掃羅的意思要使大衛喪在非利士人的手裏。
26 Nduna za Saulizo zitamuwuza Davide zimenezi, anakondwera kuti akhale mpongozi wa mfumu. Koma nthawi imene anapatsidwa isanathe,
掃羅的臣僕將這話告訴大衛,大衛就歡喜作王的女婿。日期還沒有到,
27 Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire.
大衛和跟隨他的人起身前往,殺了二百非利士人,將陽皮滿數交給王,為要作王的女婿。於是掃羅將女兒米甲給大衛為妻。
28 Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide,
掃羅見耶和華與大衛同在,又知道女兒米甲愛大衛,
29 iye anapitirirabe kumuopa Davide ndi kumadana naye moyo wake wonse.
就更怕大衛,常作大衛的仇敵。
30 Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri.
每逢非利士軍長出來打仗,大衛比掃羅的臣僕做事精明,因此他的名被人尊重。

< 1 Samueli 18 >