< 1 Samueli 10 >
1 Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi:
Or, Samuel prit une fiole d'huile, qu'il répandit sur la tête de Saül; puis il le baisa, et dit: L'Éternel ne t'a-t-il pas oint pour être le conducteur de son héritage?
2 Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’”
Aujourd'hui quand tu seras parti d'avec moi, tu trouveras, près du tombeau de Rachel, sur la frontière de Benjamin, à Tseltsach, deux hommes qui te diront: Les ânesses que tu étais allé chercher, ont été trouvées; et voici, ton père ne pense plus aux ânesses, mais il est en peine de vous, disant: Que ferai-je pour retrouver mon fils?
3 “Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo.
Et lorsque de là tu auras passé plus avant, et que tu seras venu jusqu'au chêne de Tabor, tu seras rencontré par trois hommes qui montent vers Dieu, à Béthel, et qui portent, l'un trois chevreaux, l'autre trois tourteaux de pain, et l'autre une outre de vin;
4 Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.
Et ils te demanderont comment tu te portes, et ils te donneront deux pains, que tu recevras de leur main.
5 “Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera.
Après cela, tu viendras à Guibea-Élohim, où est la garnison des Philistins; et il arrivera qu'en entrant dans la ville, tu rencontreras une troupe de prophètes, descendant du haut lieu, ayant devant eux une lyre, un tambour, une flûte et une harpe, et qui prophétiseront;
6 Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina.
Alors l'Esprit de l'Éternel te saisira, et tu prophétiseras avec eux, et tu seras changé en un autre homme.
7 Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe.
Et quand ces signes te seront arrivés, fais tout ce qui se présentera à faire; car Dieu est avec toi.
8 “Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”
Puis tu descendras devant moi, à Guilgal; et voici, je descendrai vers toi, pour offrir des holocaustes et des sacrifices de prospérités; tu attendras sept jours, jusqu'à ce que j'arrive auprès de toi, et je te déclarerai ce que tu devras faire.
9 Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo.
Or, aussitôt que Saül eut tourné le dos pour s'en aller d'avec Samuel, Dieu lui changea le cœur, et lui en donna un autre, et tous ces signes lui arrivèrent en ce jour-là.
10 Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo.
Quand ils furent arrivés à Guibea, voici, une troupe de prophètes vint au-devant de lui; et l'Esprit de Dieu le saisit, et il prophétisa au milieu d'eux.
11 Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”
Et lorsque tous ceux qui le connaissaient auparavant, virent qu'il prophétisait avec les prophètes, les gens se dirent l'un à l'autre: Qu'est-il donc arrivé au fils de Kis? Saül est-il aussi entre les prophètes?
12 Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?”
Et quelqu'un de là répondit, et dit: Et qui est leur père? C'est pourquoi cela passa en proverbe: Saül aussi est-il entre les prophètes?
13 Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri.
Puis il cessa de prophétiser, et vint au haut lieu.
14 Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?” Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”
Et un oncle de Saül dit à Saül et à son serviteur: Où êtes-vous allés? Et il répondit: Chercher les ânesses; mais voyant qu'elles ne se trouvaient point, nous sommes venus vers Samuel.
15 Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.”
Et l'oncle de Saül lui dit: Déclare-moi, je te prie, ce que vous a dit Samuel.
16 Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.
Et Saül dit à son oncle: Il nous a assuré que les ânesses étaient trouvées; mais il ne lui déclara pas le discours que Samuel avait tenu touchant la royauté.
17 Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa.
Or, Samuel convoqua le peuple, devant l'Éternel, à Mitspa;
18 Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’
Et il dit aux enfants d'Israël: Ainsi a dit l'Éternel, le Dieu d'Israël: J'ai fait monter Israël hors d'Égypte, et je vous ai délivrés de la main des Égyptiens, et de la main de tous les royaumes qui vous opprimaient;
19 Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”
Et aujourd'hui vous rejetez votre Dieu, qui vous a délivrés de tous vos maux et de toutes vos afflictions, et vous dites: Non, mais établis un roi sur nous. Présentez-vous donc maintenant devant l'Éternel, selon vos tribus, et selon vos milliers.
20 Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa.
Alors Samuel fit approcher toutes les tribus d'Israël; et la tribu de Benjamin fut désignée.
21 Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze.
Puis, il fit approcher la tribu de Benjamin, selon ses familles, et la famille de Matri fut désignée; puis Saül, fils de Kis, fut désigné, et ils le cherchèrent; mais il ne se trouva point.
22 Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?” Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”
Et ils consultèrent encore l'Éternel, en disant: Est-il encore venu un homme ici? Et l'Éternel dit: Le voilà caché dans les bagages.
23 Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa.
Et ils coururent, et le tirèrent de là, et il se présenta au milieu du peuple; et il dépassait tout le peuple, depuis les épaules en haut.
24 Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.” Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
Et Samuel dit à tout le peuple: Voyez-vous celui que l'Éternel a choisi? Il n'y en a point dans tout le peuple qui soit semblable à lui. Et tout le peuple jeta des cris de joie, et dit: Vive le roi!
25 Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.
Alors Samuel prononça devant le peuple le droit du royaume, et l'écrivit dans un livre, qu'il mit devant l'Éternel. Puis Samuel renvoya tout le peuple, chacun en sa maison.
26 Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima.
Saül aussi s'en alla en sa maison, à Guibea, et les gens de guerre, dont Dieu avait touché le cœur, allèrent avec lui.
27 Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.
Mais il y eut des hommes pervers qui dirent: Comment celui-ci nous délivrerait-il? Et ils le méprisèrent, et ne lui apportèrent point de présent; mais il fit le sourd.