< 1 Petro 5 >

1 Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe.
Starješine dakle među vama opominjem, ja sustarješina i svjedok Kristovih patnja, a zato i zajedničar slave koja se ima očitovati:
2 Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira.
pasite povjereno vam stado Božje, nadgledajte ga - ne prisilno, nego dragovoljno, po Božju; ne radi prljava dobitka, nego oduševljeno;
3 Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo.
i ne kao gospodari Baštine nego kao uzori stada.
4 Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
Pa kad se pojavi Natpastir, primit ćete neuveli vijenac slave.
5 Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa, “Mulungu amatsutsana nawo odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”
Tako i vi, mladići, podložite se starješinama; svi se jedni prema drugima pripašite poniznošću jer Bog se oholima protivi, a poniznima daruje milost.
6 Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni.
Ponizite se dakle pod snažnom rukom Božjom da vas uzvisi u pravo vrijeme.
7 Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.
Svu svoju brigu povjerite njemu jer on se brine za vas.
8 Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze.
Otrijeznite se! Bdijte! Protivnik vaš, đavao, kao ričući lav obilazi tražeći koga da proždre.
9 Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.
Oprite mu se stameni u vjeri znajući da takve iste patnje podnose vaša braća po svijetu.
10 Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. (aiōnios g166)
A Bog svake milosti, koji vas pozva na vječnu slavu u Kristu, on će vas, pošto malo potrpite, usavršiti, učvrstiti, ojačati, utvrditi. (aiōnios g166)
11 Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni. (aiōn g165)
Njemu vlast u vijeke vjekova! Amen. (aiōn g165)
12 Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu.
Pišem vam ukratko, po Silvanu, koga smatram bratom vjernim, da vas ohrabrim i posvjedočim kako je ovo istinska milost Božja. Nje se držite!
13 Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni.
Pozdravlja vas suizabranica u Babilonu i Marko, sin moj.
14 Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.
Pozdravite jedni druge cjelovom ljubavi! Mir svima vama koji ste u Kristu!

< 1 Petro 5 >