< 1 Petro 4 >

1 Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo.
Χριστοῦ οὖν παθόντος σαρκὶ καὶ ὑμεῖς τὴν αὐτὴν ἔννοιαν ὁπλίσασθε, ὅτι ὁ παθὼν σαρκὶ πέπαυται ἁμαρτίας·
2 Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu.
εἰς τὸ μηκέτι ἀνθρώπων ἐπιθυμίαις, ἀλλὰ θελήματι θεοῦ τὸν ἐπίλοιπον ἐν σαρκὶ βιῶσαι χρόνον.
3 Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa.
ἀρκετὸς γὰρ ὁ παρεληλυθὼς χρόνος τὸ βούλημα τῶν ἐθνῶν κατειργάσθαι, πεπορευμένους ἐν ἀσελγείαις, ἐπιθυμίαις, οἰνοφλυγίαις, κώμοις, πότοις, καὶ ἀθεμίτοις εἰδωλολατρείαις·
4 Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe.
ἐν ᾧ ξενίζονται μὴ συντρεχόντων ὑμῶν εἰς τὴν αὐτὴν τῆς ἀσωτίας ἀνάχυσιν, βλασφημοῦντες,
5 Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.
οἳ ἀποδώσουσιν λόγον τῷ ἑτοίμως ἔχοντι κρῖναι ζῶντας καὶ νεκρούς.
6 Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.
εἰς τοῦτο γὰρ καὶ νεκροῖς εὐηγγελίσθη, ἵνα κριθῶσιν μὲν κατὰ ἀνθρώπους σαρκί, ζῶσιν δὲ κατὰ θεὸν πνεύματι.
7 Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera.
Πάντων δὲ τὸ τέλος ἤγγικεν· σωφρονήσατε οὖν καὶ νήψατε εἰς προσευχάς,
8 Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri.
πρὸ πάντων τὴν εἰς ἑαυτοὺς ἀγάπην ἐκτενῆ ἔχοντες, ὅτι ἀγάπη καλύπτει πλῆθος ἁμαρτιῶν.
9 Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika.
φιλόξενοι εἰς ἀλλήλους ἄνευ γογγυσμοῦ·
10 Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu.
ἕκαστος καθὼς ἔλαβεν χάρισμα, εἰς ἑαυτοὺς αὐτὸ διακονοῦντες ὡς καλοὶ οἰκονόμοι ποικίλης χάριτος θεοῦ·
11 Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni. (aiōn g165)
εἴ τις λαλεῖ, ὡς λόγια θεοῦ· εἴ τις διακονεῖ, ὡς ἐξ ἰσχύος ἧς χορηγεῖ ὁ θεός· ἵνα ἐν πᾶσιν δοξάζηται ὁ θεὸς διὰ Ἰησοῦ χριστοῦ, ᾧ ἐστιν ἡ δόξα καὶ τὸ κράτος εἰς τοὺς αἰῶνας τῶν αἰώνων. ἀμήν. (aiōn g165)
12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani.
Ἀγαπητοί, μὴ ξενίζεσθε τῇ ἐν ὑμῖν πυρώσει πρὸς πειρασμὸν ὑμῖν γινομένῃ, ὡς ξένου ὑμῖν συμβαίνοντος·
13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera.
ἀλλὰ καθὸ κοινωνεῖτε τοῖς τοῦ χριστοῦ παθήμασιν χαίρετε, ἵνα καὶ ἐν τῇ ἀποκαλύψει τῆς δόξης αὐτοῦ χαρῆτε ἀγαλλιώμενοι.
14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu.
εἰ ὀνειδίζεσθε ἐν ὀνόματι χριστοῦ, μακάριοι· ὅτι τὸ τῆς δόξης καὶ τὸ τοῦ θεοῦ πνεῦμα ἐφ᾽ ὑμᾶς ἀναπαύεται.
15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena,
μὴ γάρ τις ὑμῶν πασχέτω ὡς φονεὺς ἢ κλέπτης ἢ κακοποιὸς ἢ ὡς ἀλλοτριεπίσκοπος·
16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo.
εἰ δὲ ὡς χριστιανός, μὴ αἰσχυνέσθω, δοξαζέτω δὲ τὸν θεὸν ἐν τῷ ὀνόματι τούτῳ.
17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani?
ὅτι ὁ καιρὸς τοῦ ἄρξασθαι τὸ κρῖμα ἀπὸ τοῦ οἴκου τοῦ θεοῦ· εἰ δὲ πρῶτον ἀφ᾽ ἡμῶν, τί τὸ τέλος τῶν ἀπειθούντων τῷ τοῦ θεοῦ εὐαγγελίῳ;
18 Monga Malemba akuti, “Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke, nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”
καὶ εἰ ὁ δίκαιος μόλις σώζεται, ὁ ἀσεβὴς καὶ ἁμαρτωλὸς ποῦ φανεῖται;
19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.
ὥστε καὶ οἱ πάσχοντες κατὰ τὸ θέλημα τοῦ θεοῦ, πιστῷ κτίστῃ παρατιθέσθωσαν τὰς ψυχὰς αὐτῶν ἐν ἀγαθοποιΐᾳ.

< 1 Petro 4 >