< 1 Petro 2 >
1 Choncho, lekani zoyipa zonse, chinyengo chilichonse, chiphamaso, nsanje ndi kusinjirira kulikonse.
그러므로 모든 악독과 모든 궤휼과 외식과 시기와 모든 비방하는 말을 버리고
2 Monga makanda obadwa kumene amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wauzimu, kuti mukule ndi kukufikitsani ku chipulumutso chanu,
갓난 아이들같이 순전하고 신령한 젖을 사모하라 이는 이로 말미암아 너희로 구원에 이르도록 자라게 하려 함이라
3 pakuti tsopano mwalawadi kuti Ambuye ndi wabwino.
너희가 주의 인자하심을 맛보았으면 그리하라
4 Pamene mukubwera kwa Iye, amene ndi Mwala wa moyo, umene anthu anawukana, koma Mulungu anawusankha kuti ndi wa mtengowapatali,
사람에게는 버린 바가 되었으나 하나님께는 택하심을 입은 보배로운 산 돌이신 예수에게 나아와
5 inunso, mukhale ngati miyala ya moyo yoti Mulungu amangire nyumba yake yauzimu kuti mukhale ansembe opatulika, opereka nsembe zauzimu zovomerezeka ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.
너희도 산 돌같이 신령한 집으로 세워지고 예수 그리스도로 말미암아 하나님이 기쁘게 받으실 신령한 제사를 드릴 거룩한 제사장이 될찌니라
6 Pakuti mʼMalemba mwalembedwa kuti, “Taonani, ndikuyika mwala wa maziko mu Ziyoni, wosankhika ndi wamtengowapatali. Amene akhulupirira Iye sadzachititsidwa manyazi.”
경에 기록하였으되 보라 내가 택한 보배롭고 요긴한 모퉁이 돌을 시온에 두노니 저를 믿는 자는 부끄러움을 당치 아니하리라 하였으니
7 Tsono kwa inu okhulupirira, mwalawo ndi wamtengowapatali. Koma kwa amene sakhulupirira, “Mwala umene amisiri anawukana wasanduka mwala wa maziko,
그러므로 믿는 너희에게는 보배이나 믿지 아니하는 자에게는 건축자들의 버린 그 돌이 모퉁이의 머릿돌이 되고
8 ndi “Mwala wopunthwitsa anthu ndiponso thanthwe limene limagwetsa anthu.” Iwo amapunthwa chifukwa samvera uthenga, pakuti ichi ndiye chinali chifuniro cha Mulungu pa iwo.
또한 부딪히는 돌과 거치는 반석이 되었다 하니라 저희가 말씀을 순종치 아니하므로 넘어지나니 이는 저희를 이렇게 정하신 것이라
9 Koma inu ndinu anthu osankhidwa ndi Mulungu, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu ake enieni a Mulungu, munasankhidwa kuti mulalikire za ntchito zamphamvu za Iye amene anakuyitanani kuti mutuluke mu mdima ndi kulowa mʼkuwunika kwake kodabwitsa.
오직 너희는 택하신 족속이요 왕같은 제사장들이요 거룩한 나라요 그의 소유된 백성이니 이는 너희를 어두운데서 불러 내어 그의 기이한 빛에 들어가게 하신 자의 아름다운 덕을 선전하게 하려 하심이라
10 Kale simunali anthu ake, koma tsopano ndinu anthu a Mulungu. Kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
너희가 전에는 백성이 아니더니 이제는 하나님의 백성이요 전에는 긍휼을 얻지 못하였더니 이제는 긍휼을 얻은 자니라
11 Okondedwa, ndikukupemphani, ngati alendo pansi pano, pewani zilakolako za uchimo, zimene zimachita nkhondo ndi moyo wanu.
사랑하는 자들아 나그네와 행인같은 너희를 권하노니 영혼을 거스려 싸우는 육체의 정욕을 제어하라
12 Khalani moyo wabwino pakati pa anthu osapembedza kuti ngakhale atakusinjirirani kuti mumachita zoyipa, iwowo akaona ntchito zanu zabwino, adzalemekeza Mulungu pa tsiku lomwe Iye adzatiyendere.
너희가 이방인 중에서 행실을 선하게 가져 너희를 악행한다고 비방하는 자들로 하여금 너희 선한 일을 보고 권고하시는 날에 하나님께 영광을 돌리게 하려 함이라
13 Gonjerani maulamuliro onse chifukwa cha Ambuye. Kaya ndi mfumu, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro waukulu,
인간에 세운 모든 제도를 주를 위하여 순복하되 혹은 위에 있는 왕이나
14 kaya ndi mabwanamkubwa, pakuti watumidwa ndi mfumu kuti alange onse amene amachita zoyipa ndi kuyamikira onse amene amachita zabwino.
혹은 악행하는 자를 징벌하고 선행하는 자를 포장하기 위하여 그의 보낸 방백에게 하라
15 Pakuti Mulungu akufuna kuti pochita ntchito zabwino muthetse kuyankhula mosazindikira ndi mopusa.
곧 선행으로 어리석은 사람들의 무식한 말을 막으시는 것이라
16 Mukhale monga mfulu, koma musagwiritse ntchito ufulu wanuwo ngati chophimbira zoyipa; mukhale monga atumiki a Mulungu.
자유하나 그 자유로 악을 가리우는데 쓰지 말고 오직 하나님의 종과 같이 하라
17 Chitirani ulemu aliyense, kondani abale okhulupirira, wopani Mulungu, ndipo chitirani mfumu ulemu.
뭇 사람을 공경하며 형제를 사랑하며 하나님을 두려워하며 왕을 공경하라
18 Inu akapolo, gonjerani ambuye anu ndi kuwachitira ulemu, osati kwa iwo okha amene ndi abwino ndi omvetsa zinthu, komanso kwa amene ndi ankhanza.
사환들아 범사에 두려워함으로 주인들에게 순복하되 선하고 관용하는 자들에게만 아니라 또한 까다로운 자들에게도 그리하라
19 Pakuti ndi chinthu chokoma ngati munthu apirira mu zowawa zimene sizinamuyenera chifukwa chodziwa kuti Mulungu alipo.
애매히 고난을 받아도 하나님을 생각함으로 슬픔을 참으면 이는 아름다우나
20 Kodi pali choti akuyamikireni ngati mupirira pomenyedwa chifukwa choti mwalakwa? Koma ngati mumva zowawa chifukwa chochita zabwino ndi kupirira, mwachita choyamikika pamaso pa Mulungu.
죄가 있어 매를 맞고 참으면 무슨 칭찬이 있으리요 오직 선을 행함으로 고난을 받고 참으면 이는 하나님 앞에 아름다우니라
21 Munayitanidwa kudzachita zimenezi, chifukwa Khristu anamva zowawa chifukwa cha inu, anakusiyirani chitsanzo, kuti inu mutsatire mʼmapazi ake.
이를 위하여 너희가 부르심을 입었으니 그리스도도 너희를 위하여 고난을 받으사 너희에게 본을 끼쳐 그 자취를 따라 오게 하려 하셨느니라
22 “Iye sanachite tchimo kapena kunena bodza.”
저는 죄를 범치 아니하시고 그 입에 궤사도 없으시며
23 Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sanabwezere chipongwe, pamene Iye ankamva zowawa, sanaopseze. Mʼmalo mwake, anadzipereka kwa Mulungu amene amaweruza molungama.
욕을 받으시되 대신 욕하지 아니하시고 고난을 받으시되 위협하지 아니하시고 오직 공의로 심판하시는 자에게 부탁하시며
24 Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi mabala ake munachiritsidwa.
25 Pakuti munali monga nkhosa zosochera, koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa ndi woyangʼanira miyoyo yanu.