< 1 Mafumu 7 >

1 Solomoni anamanga nyumba yake yaufumu kwa zaka 13.
And Solomon built a house for himself in thirteen years.
2 Iye anamanga nyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni yomwe mulitali mwake inali mamita 44, mulifupi mwake mamita 22, msinkhu wake mamita 13 ndi theka; ndipo inakhazikika pa mizere inayi ya mapanda a mkungudza yokhala ndi mitanda ya mkungudza yotanthalika pa mapandawo.
And he built the house with the wood of Libanus; its length [was] a hundred cubits, and its breadth [was] fifty cubits, and its height [was] of thirty cubits, and [it was made] with three rows of cedar pillars, and the pillars had side-pieces of cedar.
3 Pamwamba pa mitandapo panali matabwa a mkungudza amene anaphimba zipinda zimene zinamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira 15.
And he formed the house with chambers above on the sides of the pillars, and the number of the pillars [was each] row forty and five,
4 Mazenera a nyumbayo anali mmwamba mʼmizere itatu, zenera kuyangʼanana ndi zenera linzake.
and [there were] three chambers, and space against space in three rows.
5 Zitseko zonse ndi mazenera omwe, maferemu ake anali ofanana mbali zonse. Mulitali mwake ndi mulifupi mwake, ndipo zenera linkapenyana ndi zenera linzake pa mizere itatu.
And all the doors and spaces formed like chambers [were] square, and from door to door [was a correspondence] in three rows.
6 Iye anapanga Chipinda cha Nsanamira. Mulitali mwake munali mamita 22, mulifupi mwake munali mamita 13 ndi theka. Patsogolo pake panali khonde ndi nsanamira zokhala ndi denga.
And [he made] the porch of the pillars, [they were] fifty [cubits] long and fifty broad, the porch joining them in front; and the [other] pillars and the thick beam [were] in front of the house by the porches.
7 Anamanga chipinda cha mpando waufumu, Chipinda cha Chilungamo, modzaweruziramo milandu ndipo anayikutira ndi matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka ku denga.
And [there was] the Porch of seats where he would judge, the porch of judgment.
8 Ndipo nyumba yake yodzakhalamo anayimanga kumbuyo kwa chipindacho. Nyumbayo anayimanga mofanana ndi Chipindacho. Solomoni anamanga nyumba inanso yofanana ndi chipindachi, kumangira mkazi wake mwana wa Farao.
And their house where he would dwell, [had] one court communicating with these according to this work; and [he built] the house for the daughter of Pharao whom Solomon had taken, according to this porch.
9 Nyumba zonsezi, kuyambira kunja mpaka ku bwalo lalikulu ndiponso kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, zinapangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene anayisema potengera miyeso yake yoyenera ndipo anayisalaza ndi macheka mʼkati ndi kunja komwe.
All these [were] of costly stones, sculptured at intervals within even from the foundation even to the top, and outward to the great court,
10 Maziko ake anali a miyala yabwino kwambiri, kutalika kwa miyala ina kunali mamita atatu ndi theka, inanso mamita anayi.
founded with large costly stones, stones of ten cubits and eight cubits [long].
11 Pamwamba pake panali pa miyala yabwino kwambiri, yosemedwa potengera miyeso yake. Pamwamba pa miyalayo panali matabwa a mkungudza.
And above with costly stones, according to the measure of hewn stones, and with cedars.
12 Bwalo lalikulu lozungulira nyumbayi linali ndi khoma la mizere itatu ya miyala yosemedwa ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. Bwalo la mʼkati la Nyumba ya Yehova ndiponso khonde lake anazimanga mofanana.
[There were] three rows of hewn [stones] round about the great hall, and a row of sculptured cedar.
13 Mfumu Solomoni anatuma anthu ku Turo ndipo anakabwera ndi Hiramu,
And king Solomon sent, and took Chiram out of Tyre,
14 mwana wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali ndipo abambo ake anali a ku Turo, mʼmisiri wa mkuwa. Hiramu anali munthu wa luso lalikulu ndiponso wodziwa kupanga zinthu za mkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomoni ndi kugwira ntchito zonse zimene anamupatsa.
the son of a widow woman; and he [was] of the tribe of Nephthalim, and his father [was] a Tyrian; a worker in brass, and accomplished in art and skill and knowledge to work every work in brass: and he was brought in to king Solomon, and he wrought all the works.
15 Iye anawumba nsanamira ziwiri za mkuwa, nsanamira iliyonse msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu ndipo thunthu lake akazunguliza chingwe, linali mamita asanu ndi theka.
And he cast the two pillars for the porch of the house: eighteen cubits [was] the height of [each] pillar, and a circumference of fourteen cubits encompassed it, even the thickness of the pillar: the flutings [were] four fingers [wide], and thus [was] the other pillar [formed].
16 Anapanganso mitu iwiri ya mkuwa ndi kuyiika pamwamba pa nsanamira zija; mutu uliwonse unali wotalika kupitirirapo mamita awiri.
And he made two molten chapiters to put on the heads of the pillars: five cubits [was] the height of one chapiter, and five cubits [was] the height of the other chapiter.
17 Pa mitu ya pa nsanamirazo anakolekapo maunyolo awiri olukanalukana ndi oyangayanga. Mutu uliwonse unali ndi maunyolo oterewa asanu ndi awiri.
And he made two ornaments of net-work to cover the chapiters of the pillars; even a net for one chapiter, and a net for the other chapiter.
18 Anapanga mizere iwiri ya zinthu zonga makangadza mozungulira pamwamba pa maunyolo kukongoletsa mitu ya nsanamirazo. Anachita chimodzimodzi ndi mutu uliwonse.
And hanging work, two rows of brazen pomegranates, formed with net-work, hanging work, row upon row: and thus he framed [the ornaments] for the second chapiter. And he set up the pillars of the porch of the temple: and he set up the one pillar, and called its name Jachum: and he set up the second pillar, and called its name Boloz.
19 Mitu imene inali pamwamba pa nsanamira mʼkhonde inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Kutalika kwake kunali pafupifupi mamita awiri.
And on the heads of the pillars he made lily-work against the porch, of four cubits,
20 Pa mitu yonse iwiri ya pamwamba pa nsanamira, pamwamba pa chigawo chonga mʼphika pafupi ndi cholukidwa ngati ukonde, panali makangadza 200 okhala mozungulira mʼmizere.
and a chamber over both the pillars, and above the sides an addition [equal to] the chamber in width.
21 Anayimika nsanamirazo pa khonde la Nyumba ya Mulungu. Nsanamira ya kumpoto anayitcha Yakini ndipo ya kummwera anayitcha Bowazi.
22 Mitu ya pamwamba pa nsanamirazo inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Motero anamaliza ntchito ya nsanamirazo.
23 Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.
And he made the sea, ten cubits from one rim to the other, the same was completely circular round about: its height [was] five cubits, and its circumference thirty-three cubits.
24 Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo tizikho kuzungulira thunthu lonse la mbiyayo, tizikho khumi pa theka la mita. Tizikhoto tinali mʼmizere iwiri ndipo anatipangira kumodzi ndi mbiyayo.
And stays underneath its rim round about compassed it ten cubits round;
25 Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati.
And [there were] twelve oxen under the sea: three looking to the north, and three looking to the west, and three looking to the south, and three looking to the east: and all their hinder parts [were] inward, and the sea [was] above upon them.
26 Mbiyayo inali yonenepa ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 40,000.
and its rim [was] as the work of the rim of a cup, a lily-flower, and the thickness of it [was] a span.
27 Iye anapanganso maphaka khumi a mkuwa. Phaka lililonse mulitali mwake linali pafupifupi mamita awiri, mulifupi mwake linali pafupifupi mamita awiri, ndipo msinkhu wake unali kupitirirapo mita imodzi.
And he made ten brazen bases: five cubits [was] the length of one base, and four cubits the breadth of it, and its height [was] six cubits.
28 Maphakawo anapangidwa motere: Anali ndi matabwa a mʼmbali amene ankalowa mʼmaferemu.
And this work of the bases [was] formed with a border the them, and [there was] a border between the ledges.
29 Pakati pa matabwa a mʼmbali ndi maferemu panali zithunzi za mikango, ngʼombe zazimuna ndi akerubi. Pa maferemuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ngʼombe zazimunazo anajambulapo nkhata za maluwa.
And upon their borders between the projection [were] lions, and oxen, and cherubs: and on the projections, even so above, and also below [were] the places of lions and oxen, hanging work.
30 Phaka lililonse linali ndi mikombero ya mkuwa inayi ndi mitandanso ya mkuwa, ndipo phaka lililonse linali ndi zogwiriziza mbale zosambira pa ngodya zake zinayi, zopangidwa limodzi ndi nkhata za maluwa mbali zake zonse.
And [there were] four brazen wheels to one base; and [there were] brazen bases, and their four sides [answering to them], side pieces under the bases.
31 Mʼkati mwa phakalo munali malo otsekuka amene anali ndi feremu yozungulira ndipo anali ozama theka la mita. Malo otsekukawa anali wozungulira, ndipo pamodzi ndi tsinde lake anali otalika masentimita 44. Kuzungulira pa malo otsekukawa panajambulidwa zokometsera. Matabwa oyimikira phakali anali ofanana mbali zonse, osati ozungulira.
And [there were] axles in the wheels under the base.
32 Pansi pa matabwawo panali mikombero inayi, ndipo mitanda ya mikomberoyo inalumikizidwa ku phakalo. Msinkhu wa mkombero uliwonse unali masentimita 66.
And the height of one wheel [was] a cubit and a half.
33 Mikomberoyo inapangidwa ngati mikombero ya galeta; mitanda yake, marimu ake, sipokosi zake ndiponso mahabu ake, zonsezi zinali za chitsulo.
And the work of the wheels [was] as the work of chariot wheels: their axles, and their felloes, and [the rest of] their work, [were] all molten.
34 Phaka lililonse linali ndi zogwirira zinayi; chogwirira chimodzi pa ngodya iliyonse, zolumikizidwa ku phakalo.
The four side pieces were at the four corners of each base; its shoulders [were formed] of the base.
35 Pamwamba pa phakalo panali mkombero wozungulira ndipo msinkhu wake unali masentimita 22. Pamwamba pa phakalo panali zogwiriziza ndi matabwa ake, zolumikizidwa ku phakalo.
And on the top of the base half a cubit [was] the size of it, [there was] a circle on the top of the base, and [there was] the top of its spaces and its borders: and it was open at the top of its spaces.
36 Paliponse pamene panali malo woti nʼkujambulapo, pa zogwiriziza ndi pa matabwa, anagobapo zithunzi za akerubi, mikango ndi mitengo ya mgwalangwa. Anajambulanso nkhata za maluwa mozungulira.
And its borders [were] cherubs, and lions, and palm-trees, upright, each [was] joined in front [and] within and round about.
37 Umu ndi mmene anapangira maphaka khumiwo. Onse anawapanga malo ofanana ndipo anali a miyeso yofanana ndiponso wooneka mofanana.
According to the same form he made all the ten bases, [even] one order and one measure to all.
38 Kenaka anapanga mabeseni akuluakulu khumi a mkuwa; beseni lililonse munkalowa madzi a malita 800, ndipo poyeza modutsa, pakamwa pake panali pafupifupi mamita awiri. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi beseni lake.
And he made ten brazen lavers, each laver containing forty baths, [and] measuring four cubits, each laver [placed] on a several base throughout the ten bases.
39 Maphaka asanu anawayika mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu, asanu enawo anawayika mbali ya kumpoto. Mbiyayo anayiyika mbali yakummwera, pa ngodya yakummwera cha kummawa kwa Nyumba ya Mulungu.
And he put five bases on the right side of the house, and five on the left side of the house: and the sea was placed on the right side of the house eastward in the direction of the south.
40 Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi. Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Yehova imene ankagwirira Mfumu Solomoni:
And Chiram made the caldrons, and the pans, and the bowls; and Chiram finished making all the works that he wrought for king Solomon in the house of the Lord:
41 nsanamira ziwiri; mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo; maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;
two pillars and the wreathen works of the pillars on the heads of the two pillars; and the two net-works to cover both the wreathen works of the flutings that were upon the pillars.
42 makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);
The four hundred pomegranates for both the net-works, two rows of pomegranates for one net-work, to cover both the wreathen works of the bases belonging to both pillars.
43 maphaka khumi pamodzi ndi mabeseni khumi pa maphakawo;
And the ten bases, and the ten lavers upon the bases.
44 mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo;
And one sea, and the twelve oxen under the sea.
45 miphika, mafosholo ndi mbale zowazira magazi. Ziwiya zonsezi za ku Nyumba ya Yehova, zimene Hiramu anapangira Mfumu Solomoni, zinali zamkuwa wonyezimira.
And the caldrons, and pans, and bowls, and all the furniture, which Chiram made for king Solomon for the house of the Lord: and [there were] eight and forty pillars of the house of the king and of the house of the Lord: all the works of the king which Chiram made were entirely of brass.
46 Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani.
47 Solomoni sanayeze ziwiya zonsezi chifukwa zinali zambiri ndipo kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.
There was no reckoning of the brass of which he made all these works, from the very great abundance, there was no end of the weight of the brass. In the country round about Jordan did he cast them, in the clay land between Socchoth and Sira.
48 Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova: guwa lansembe lagolide; tebulo lagolide pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;
And king Solomon took the furniture which [Chiram] made for the house of the Lord, the golden altar, and the golden table of shewbread.
49 zoyikapo nyale zagolide weniweni (dzanja lamanja zisanu ndipo zisanu zina ku dzanja lamanzere, mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika); maluwa agolide, nyale ndi mbaniro;
And [he put] the five candlesticks on the left, and five on the right in front of the oracle, [being] of pure gold, and the lamp-stands, and the lamps, and the snuffers of gold.
50 mbale zagolide weniweni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira; ndiponso zomangira zitseko zagolide za chipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndiponso za zitseko za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu.
And [there were made] the porches, and the nails, and the bowls, and the spoons, and the golden censers, of pure gold: and the panels of the doors of the innermost part of the house, [even] the holy of holies, and the golden doors of the temple.
51 Pamene ntchito yonse imene Mfumu Solomoni inagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka: siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Yehova.
So the work of the house of the Lord which Solomon wrought was finished; and Solomon brought in the holy things of David his father, and all the holy things of Solomon; he put the silver, and the gold, and the furniture, into the treasures of the house of the Lord.

< 1 Mafumu 7 >