< 1 Mafumu 4 >
1 Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse.
And king Solomon reigned over all Israel:
2 Nduna zake zikuluzikulu zinali izi: Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;
And these were the princes which he had: Azarias the son of Sadoc the priest:
3 Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi; Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;
Elihoreph, and Ahia, the sons of Sisa, scribes: Josaphat the son of Ahilud, recorder:
4 Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo; Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;
Banaias the son of Joiada, over the army: and Sadoc and Abiathar priests.
5 Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo; Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;
Azarias the son of Nathan, over them that were about the king: Zabud, the son of Nathan the priest, the king’s friend:
6 Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu; Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.
And Ahisar governor of the house: and Adoniram the son of Abda over the tribute.
7 Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka.
And Solomon had twelve governors over all Israel, who provided victuals for the king and for his household: for every one provided necessaries, each man his month in the year.
8 Mayina awo ndi awa: Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;
And these are their names: Benhur, in mount Ephraim,
9 Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;
Bendecar, in Macces, and in Salebim, and in Bethsames, and in Elon, and in Bethanan.
10 Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);
Benhesed in Aruboth: his was Socho, and all the land of Epher.
11 Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);
Benabinadab, to whom belonged all Nephath-Dor, he had Tapheth the daughter of Solomon to wife.
12 Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;
Bana the son of Ahilud, who governed Thanac and Mageddo, and all Bethsan, which is by Sarthana beneath Jezrael, from Bethsan unto Abelmehula over against Jecmaan.
13 Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).
Bengaber in Ramoth Galaad: he had the towns of Jair the son of Manasses in Galaad, he was chief in all the country of Argob, which is in Basan, threescore great cities with walls, and brazen bolts.
14 Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;
Abinadab the son of Addo was chief in Manaim.
15 Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);
Achimaas in Nephtali: he also had Basemath the daughter of Solomon to wife.
16 Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;
Baana the son of Husi, in Aser and in Baloth.
17 Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;
Josaphat the son of Pharue, in Issachar.
18 Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;
Semei the son of Ela in Benjamin.
19 Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.
Gaber the son of Uri, in the land of Galaad, in the land of Sehon the king of the Amorrhites and of Og the king of Basan, over all that were in that land.
20 Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala.
Juda and Israel were innumerable, as the sand of the sea in multitude: eating and drinking, and rejoicing.
21 Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.
And Solomon had under him all the kingdoms from the river to the land of the Philistines, even to the border of Egypt: and they brought him presents, and served him, all the days of his life.
22 Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa,
And the provision of Solomon for each day was thirty measures of fine flour, and threescore measures of meal,
23 ngʼombe khumi zonenepa zodyetsera mʼkhola, ngʼombe za ku busa makumi awiri, ndiponso nkhosa ndi mbuzi 100, pamodzinso ndi mbawala, agwape, mphoyo ndi mbalame zoweta zonona.
Ten fat oxen and twenty out of the pastures, and a hundred rams, besides venison of harts, roes, and buffles, and fatted fowls.
24 Pakuti ankalamulira dziko lonse la kumadzulo kwa mtsinje wa Yufurate kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza, mafumu onse a kumadzulo kwa Mtsinje, ndipo anali pa mtendere ndi mayiko onse ozungulira.
For he had all the country which was beyond the river, from Thaphsa to Gazan, and all the kings of those countries: and he had peace on every side round about.
25 Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.
And Juda and Israel dwelt without any fear, every one under his vine, and under his fig tree, from Dan to Bersabee, all the days of Solomon.
26 Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta.
And Solomon had forty thousand stalls of chariot horses, and twelve thousand for the saddle.
27 Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse.
And the foresaid governors of the king fed them: and they furnished the necessaries also for king Solomon’s table, with great care in their time.
28 Ankabweretsanso ku malo ake ofunikira muyeso wawo wa barele ndi udzu wa akavalo okoka magaleta ndiponso akavalo ena.
They brought barley also and straw for the horses, and beasts, to the place where the king was, according as it was appointed them.
29 Mulungu anamupatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka ndipo nzeru zake zinali zochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.
And God gave to Solomon wisdom and understanding exceeding much, and largeness of heart as the sand that is on the sea shore.
30 Nzeru za Solomoni zinali zoposa nzeru za anthu onse a Kummawa ndiponso nzeru zonse za ku Igupto.
And the wisdom of Solomon surpassed the wisdom of all the Orientals, and of the Egyptians,
31 Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira.
And he was wiser than all men: wiser than Ethan the Ezrahite, and Heman, and Chalcol, and Dorda the sons of Mahol, and he was renowned in all nations round about.
32 Solomoni anapeka miyambi 3,000 ndi kulemba nyimbo 1,005.
Solomon also spoke three thousand parables: and his poems were a thousand and five.
33 Iye ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope khomera pa khoma. Iye ankaphunzitsanso za nyama ndi mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba.
And he treated about trees from the cedar that is in Libanus, unto the hyssop that cometh out of the wall: and he discoursed of beasts, and of fowls, and of creeping things, and of fishes.
34 Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.
And they came from all nations to hear the wisdom of Solomon, and from all the kings of the earth, who heard of his wisdom.