< 1 Mafumu 3 >
1 Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu.
Confirmatum est igitur regnum in manu Salomonis, et affinitate conjunctus est Pharaoni regi Ægypti: accepit namque filiam ejus, et adduxit in civitatem David, donec compleret ædificans domum suam, et domum Domini, et murum Jerusalem per circuitum.
2 Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba.
Attamen populus immolabat in excelsis: non enim ædificatum erat templum nomini Domini usque in diem illum.
3 Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.
Dilexit autem Salomon Dominum, ambulans in præceptis David patris sui, excepto quod in excelsis immolabat, et accendebat thymiama.
4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe.
Abiit itaque in Gabaon, ut immolaret ibi: illud quippe erat excelsum maximum: mille hostias in holocaustum obtulit Salomon super altare illud in Gabaon.
5 Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
Apparuit autem Dominus Salomoni per somnium nocte, dicens: Postula quod vis ut dem tibi.
6 Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.
Et ait Salomon: Tu fecisti cum servo tuo David patre meo misericordiam magnam, sicut ambulavit in conspectu tuo in veritate et justitia, et recto corde tecum: custodisti ei misericordiam tuam grandem, et dedisti ei filium sedentem super thronum ejus, sicut est hodie.
7 “Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi.
Et nunc Domine Deus, tu regnare fecisti servum tuum pro David patre meo: ego autem sum puer parvulus, et ignorans egressum et introitum meum.
8 Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga.
Et servus tuus in medio est populi quem elegisti, populi infiniti, qui numerari et supputari non potest præ multitudine.
9 Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
Dabis ergo servo tuo cor docile, ut populum tuum judicare possit, et discernere inter bonum et malum. Quis enim poterit judicare populum istum, populum tuum hunc multum?
10 Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi.
Placuit ergo sermo coram Domino, quod Salomon postulasset hujuscemodi rem.
11 Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo,
Et dixit Dominus Salomoni: Quia postulasti verbum hoc, et non petisti tibi dies multos, nec divitias, aut animas inimicorum tuorum, sed postulasti tibi sapientiam ad discernendum judicium:
12 Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako.
ecce feci tibi secundum sermones tuos, et dedi tibi cor sapiens et intelligens, in tantum ut nullus ante te similis tui fuerit, nec post te surrecturus sit.
13 Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe.
Sed et hæc quæ non postulasti, dedi tibi: divitias scilicet, et gloriam, ut nemo fuerit similis tui in regibus cunctis retro diebus.
14 Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.”
Si autem ambulaveris in viis meis, et custodieris præcepta mea et mandata mea, sicut ambulavit pater tuus, longos faciam dies tuos.
15 Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto. Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse.
Igitur evigilavit Salomon, et intellexit quod esset somnium: cumque venisset Jerusalem, stetit coram arca fœderis Domini, et obtulit holocausta, et fecit victimas pacificas, et grande convivium universis famulis suis.
16 Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake.
Tunc venerunt duæ mulieres meretrices ad regem, steteruntque coram eo:
17 Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu.
quarum una ait: Obsecro, mi domine: ego et mulier hæc habitabamus in domo una, et peperi apud eam in cubiculo.
18 Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.
Tertia autem die postquam ego peperi, peperit et hæc: et eramus simul, nullusque alius nobiscum in domo, exceptis nobis duabus.
19 “Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera.
Mortuus est autem filius mulieris hujus nocte: dormiens quippe oppressit eum.
20 Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga.
Et consurgens intempestæ noctis silentio, tulit filium meum de latere meo, ancillæ tuæ dormientis, et collocavit in sinu suo: suum autem filium, qui erat mortuus, posuit in sinu meo.
21 Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”
Cumque surrexissem mane ut darem lac filio meo, apparuit mortuus: quem diligentius intuens clara luce, deprehendi non esse meum quem genueram.
22 Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.” Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
Responditque altera mulier: Non est ita ut dicis, sed filius tuus mortuus est, meus autem vivit. E contrario illa dicebat: Mentiris: filius quippe meus vivit, et filius tuus mortuus est. Atque in hunc modum contendebant coram rege.
23 Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’”
Tunc rex ait: Hæc dicit: Filius meus vivit, et filius tuus mortuus est: et ista respondit: Non, sed filius tuus mortuus est, meus autem vivit.
24 Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu.
Dixit ergo rex: Afferte mihi gladium. Cumque attulissent gladium coram rege,
25 Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”
Dividite, inquit, infantem vivum in duas partes, et date dimidiam partem uni, et dimidiam partem alteri.
26 Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!” Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”
Dixit autem mulier, cujus filius erat vivus, ad regem (commota sunt quippe viscera ejus super filio suo): Obsecro, domine, date illi infantem vivum, et nolite interficere eum. E contrario illa dicebat: Nec mihi nec tibi sit, sed dividatur.
27 Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”
Respondit rex, et ait: Date huic infantem vivum, et non occidatur: hæc est enim mater ejus.
28 Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.
Audivit itaque omnis Israël judicium quod judicasset rex, et timuerunt regem, videntes sapientiam Dei esse in eo ad faciendum judicium.