< 1 Mafumu 13 >

1 Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani.
때에 하나님의 사람이 여호와의 말씀으로 인하여 유다에서부터 벧엘에 이르니 마침 여로보암이 단 곁에 서서 분향하는지라
2 Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’”
하나님의 사람이 단을 향하여 여호와의 말씀으로 외쳐 가로되 단아 단아 여호와께서 말씀하시기를 다윗의 집에 요시야라 이름하는 아들을 낳으리니 저가 네 위에 분향하는 산당 제사장을 네 위에 제사할 것이요 또 사람의 뼈를 네 위에 사르리라 하셨느니라 하고
3 Tsiku lomwelo munthu wa Mulungu uja anapereka chizindikiro ichi: “Chizindikiro chimene Yehova wanena ndi ichi: Taonani guwali lidzangʼambika pakati ndipo phulusa lili pamenepo lidzamwazika.”
그 날에 저가 예조를 들어 가로되 이는 여호와의 말씀하신 예조라 단이 갈라지며 그 위에 있는 재가 쏟아지리라 하매
4 Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza.
여로보암 왕이 하나님의 사람의 벧엘에 있는 단을 향하여 외쳐 말함을 들을 때에 단에서 손을 펴며 저를 잡으라 하더라 저를 향하여 편 손이 말라 다시 거두지 못하며
5 Nthawi yomweyo guwa lija linangʼambika pakati ndipo phulusa lake linamwazika molingana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapereka potsata mawu a Yehova.
하나님의 사람의 여호와의 말씀으로 보인 예조대로 단이 갈라지며 재가 단에서 쏟아진지라
6 Pamenepo mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Undipempherere kwa Yehova Mulungu wako kuti andikomere mtima ndipo undipempherere kuti dzanja langa lichire.” Choncho munthu wa Mulungu anapempha kwa Yehova, ndipo dzanja la mfumu linachiritsidwa nʼkukhala ngati momwe linalili kale.
왕이 하나님의 사람에게 말하여 가로되 청컨대 너는 나를 위하여 네 하나님 여호와께 은혜를 구하여 내 손으로 다시 성하게 기도하라 하나님의 사람이 여호와께 은혜를 구하니 왕의 손이 다시 성하여 전과 같이 되니라
7 Mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya, ndipo ndidzakupatsa mphatso.”
왕이 하나님의 사람에게 이르되 나와 함께 집에 가서 몸을 쉬라 내가 네게 예물을 주리라
8 Koma munthu wa Mulunguyo anayankha mfumu kuti, “Ngakhale mutandipatsa theka la chuma chanu, sindingapite nanu, kapena kudya chakudya, kapenanso kumwa madzi kuno.
하나님의 사람이 왕께 대답하되 왕께서 왕의 집 절반으로 내게 준다 할지라도 나는 왕과 함께 들어가지도 아니하고 이곳에서는 떡도 먹지 아니하고 물도 마시지 아니하리니
9 Pakuti Yehova anandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kapena kubwerera podzera njira imene unayendamo kale.’”
이는 곧 여호와의 말씀이 내게 명하여 이르시기를 떡도 먹지 말며 물도 마시지 말고 왔던 길로 도로 가지도 말라 하셨음이니이다 하고
10 Choncho munthu wa Mulunguyo anadzera njira ina ndipo sanatsate njira imene anayendamo pobwera ku Beteliko.
이에 다른 길로 가고 자기가 벧엘에 오던 길로 좇아 돌아가지 아니하니라
11 Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu.
벧엘에 한 늙은 선지자가 살더니 그 아들들이 와서 이 날에 하나님의 사람이 벧엘에서 행한 모든 일을 저에게 고하고 또 그가 왕에게 고한 말씀도 저희가 그 아비에게 고한지라
12 Abambo awo aja anawafunsa kuti, “Kodi wadzera njira iti?” Ana akewo anamufotokozera njira imene munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo anadzera.
그 아비가 저희에게 이르되 그가 어느 길로 가더냐 하니 그 아들들이 유다에서부터 온 하나님의 사람의 간 길을 보았음이라
13 Ndipo abambo aja anati kwa ana akewo, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo atamangirira chishalo pa bulu, nkhalambayo inakwera buluyo
저가 그 아들들에게 이르되 나를 위하여 나귀에 안장을 지우라 저희가 나귀에 안장을 지우니 저가 타고
14 ndipo inalondola munthu wa Mulunguyo. Inamupeza atakhala pansi pa mtengo wa thundu ndipo inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene anabwera kuchokera ku Yuda?” Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndineyo.”
하나님의 사람의 뒤를 좇아 가서 상수리나무 아래 앉은 것을 보고 이르되 그대가 유다에서 온 하나님의 사람이뇨 대답하되 그러하다
15 Choncho mneneri wokalambayo anati kwa iye, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya.”
저가 그 사람에게 이르되 나와 함께 집으로 가서 떡을 먹으라
16 Munthu wa Mulungu uja anati, “Sindingabwerere nanu kapena kudya chakudya kapenanso kumwa madzi kuno.
대답하되 나는 그대와 함께 돌아가지도 못하겠고 그대와 함께 들어가지도 못하겠으며 내가 이 곳에서 그대와 함께 떡도 먹지 아니하고 물도 마시지 아니하리니
17 Pakuti ndawuzidwa ndi Yehova kuti, ‘Usadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko kapenanso kubwerera poyenda njira imene unayendamo popita.’”
이는 여호와의 말씀이 내게 이르시기를 네가 거기서 떡도 먹지 말고 물도 마시지 말며 또 네가 오던 길로 돌아가지도 말라 하셨음이로라
18 Mneneri wokalambayo anayankha kuti, “Inenso ndine mneneri ngati iwe. Ndipo mngelo wa Yehova anayankhula nane mawu a Yehova kuti, ‘Kamubweze abwere ku nyumba yako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’” Koma anamunamiza.
저가 그 사람에게 이르되 나도 그대와 같은 선지자라 천사가 여호와의 말씀으로 내게 이르기를 그를 네 집으로 데리고 돌아가서 그에게 떡을 먹이고 물을 마시우라 하였느니라 하니 이는 그 사람을 속임이라
19 Choncho munthu wa Mulungu uja anabwerera naye ndipo anakadya ndi kumwa madzi mʼnyumba mwake.
이에 그 사람이 저와 함께 돌아가서 그 집에서 떡을 먹으며 물을 마시니라
20 Ali pa tebulo, Yehova anayankhula ndi mneneri wokalambayo amene anamubweza munthu wa Mulunguyo.
저희가 상 앞에 앉았을 때에 여호와의 말씀이 그 사람을 데려온 선지자에게 임하니
21 Iye anafuwulira munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo kuti, “Yehova akuti, ‘Iwe wanyoza mawu a Yehova ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa.
저가 유다에서부터 온 하나님의 사람을 향하여 외쳐 가로되 여호와의 말씀에 네가 여호와의 말씀을 어기며 네 하나님 여호와가 네게 명한 명령을 지키지 아니하고
22 Iwe wabwerera ndi kudya chakudya ndiponso kumwa madzi ku malo amene Iye anakuwuza kuti usadye chakudya kapena kumwa madzi. Choncho mtembo wako sadzawuyika mʼmanda a makolo ako.’”
돌아와서 여호와가 너더러 떡도 먹지 말고 물도 마시지 말라 한 곳에서 떡을 먹고 물을 마셨으니 네 시체가 네 열조의 묘실에 들어가지 못하리라 하셨느니라 하니라
23 Munthu wa Mulungu atatha kudya ndi kumwa, mneneri amene anamubweza uja anamangirira chishalo pa bulu wa munthu wa Mulunguyo.
자기가 데리고 온 선지자가 떡을 먹고 물을 마신 후에 그를 위하여 나귀에 안장을 지우니라
24 Akupita, anakumana ndi mkango pa msewu ndipo unamupha, mtembo wake unagwera pansi pa msewu, bulu uja anayima pambali pake ndipo mkango unayima pafupi ndi mtembowo.
이에 그 사람이 가더니 사자가 길에서 저를 만나 죽이매 그 시체가 길에 버린 바 되니 나귀는 그 곁에 섰고 사자도 그 시체 곁에 섰더라
25 Ndipo taonani, anthu ena amene ankapita mu msewumo anaona mtembowo uli pansi potero, mkango utayima pa mbali pa mtembo uja ndipo anapita nakafotokozera anthu mu mzinda umene mumakhala mneneri wokalamba uja.
지나가는 사람들이 길에 버린 시체와 그 시체 곁에 선 사자를 보고 그 늙은 선지자가 사는 성읍에 와서 말한지라
26 Mneneri amene anamubweza mnzake ku njira uja atamva zimenezi, anati, “Ameneyo ndi munthu wa Mulungu amene wanyoza mawu a Yehova. Yehova wamupereka kwa mkango umene wamukhadzula ndi kumupha, monga momwe Yehova anamuchenjezera.”
그 사람을 길에서 데리고 돌아간 선지자가 듣고 말하되 이는 여호와의 말씀을 어긴 하나님의 사람이로다 여호와께서 그에게 하신 말씀과 같이 여호와께서 그를 사자에게 붙이시매 사자가 그를 찢어 죽였도다 하고
27 Mneneri wokalambayo anati kwa ana ake, “Mundimangire chishalo pa bulu,” ndipo anaterodi.
이에 그 아들들에게 말하여 가로되 나를 위하여 나귀에 안장을 지우라 저희가 안장을 지우매
28 Ndipo anapita, nakapezadi mtembo utagwera pansi mu msewu, bulu pamodzi ndi mkango atayima pambali pake. Koma mkangowo sunadye mtembowo kapena kukhadzula buluyo.
저가 가서 본즉 그 시체가 길에 버린 바 되었고 나귀와 사자는 그 시체 곁에 섰는데 사자가 시체를 먹지도 아니하였고 나귀를 찢지도 아니하였더라
29 Choncho mneneri wokalambayo anatenga mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nawuyika pa bulu, ndipo anabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuyika mtembowo mʼmanda.
늙은 선지자가 하나님의 사람의 시체를 떠들어 나귀에 실어가지고 돌아와 자기 성읍으로 들어가서 슬피 울며 장사하되
30 Tsono anayika mtembowo mʼmanda amene mneneri wokalamba uja anadzikonzera, ndipo anamulira pomanena kuti, “Mʼbale wanga ine! Mʼbale wanga ine!”
곧 그 시체를 자기의 묘실에 두고 그를 위하여 슬피 울며 가로되 오호라 나의 형제여 하니라
31 Atamuyika mʼmanda, iye anati kwa ana ake, “Ine ndikafa, mudzandiyike mʼmanda amene munthu wa Mulungu wayikidwa. Mudzayike mafupa anga pambali pa mafupa ake.
그 사람을 장사한 후에 저가 그 아들들에게 말하여 가로되 내가 죽거든 하나님의 사람을 장사한 묘실에 나를 장사하되 내 뼈를 그의 뼈 곁에 두라
32 Pakuti uthenga umene Yehova anamuyankhulitsa, wotsutsana ndi guwa lansembe la ku Beteli ndi nyumba zonse za chipembedzo za mʼmizinda ya ku Samariya, zidzachitika ndithu.”
그가 여호와의 말씀으로 벧엘에 있는 단을 향하고 또 사마리아 성읍들에 있는 모든 산당을 향하여 외쳐 말한 것이 반드시 이룰 것임이니라
33 Ngakhale izi zinachitika, Yeroboamu sanasiye njira zake zoyipa, koma anasankhanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo ake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna kukhala wansembe iye anamupatula kukhala wansembe.
여로보암이 이 일 후에도 그 악한 길에서 떠나 돌이키지 아니하고 다시 보통 백성으로 산당의 제사장을 삼되 누구든지 자원하면 그 사람으로 산당의 제사장을 삼았으므로
34 Limeneli ndiye linali tchimo la nyumba ya Yeroboamu limene linabweretsa kugwa kwake ndiponso chiwonongeko mʼdzikomo.
이 일이 여로보암 집에 죄가 되어 그 집이 지면에서 끊어져 멸망케 되니라

< 1 Mafumu 13 >