< 1 Mafumu 10 >
1 Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima.
示巴女王聽見所羅門因耶和華之名所得的名聲,就來要用難解的話試問所羅門。
2 Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake.
跟隨她到耶路撒冷的人甚多,又有駱駝馱着香料、寶石,和許多金子。她來見了所羅門王,就把心裏所有的對所羅門都說出來。
3 Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo.
所羅門王將她所問的都答上了,沒有一句不明白、不能答的。
4 Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga,
示巴女王見所羅門大有智慧,和他所建造的宮室,
5 chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
席上的珍饈美味,群臣分列而坐,僕人兩旁侍立,以及他們的衣服裝飾和酒政的衣服裝飾,又見他上耶和華殿的臺階,就詫異得神不守舍;
6 Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona.
對王說:「我在本國裏所聽見論到你的事和你的智慧實在是真的!
7 Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva.
我先不信那些話,及至我來親眼見了才知道人所告訴我的還不到一半。你的智慧和你的福分越過我所聽見的風聲。
8 Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu!
你的臣子、你的僕人常侍立在你面前聽你智慧的話是有福的!
9 Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
耶和華-你的上帝是應當稱頌的!他喜悅你,使你坐以色列的國位;因為他永遠愛以色列,所以立你作王,使你秉公行義。」
10 Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.
於是,示巴女王將一百二十他連得金子和寶石,與極多的香料,送給所羅門王。她送給王的香料,以後奉來的不再有這樣多。 (
11 (Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola.
希蘭的船隻從俄斐運了金子來,又從俄斐運了許多檀香木和寶石來。
12 Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).
王用檀香木為耶和華殿和王宮做欄杆,又為歌唱的人做琴瑟。以後再沒有這樣的檀香木進國來,也沒有人看見過,直到如今。)
13 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.
示巴女王一切所要所求的,所羅門王都送給她,另外照自己的厚意餽送她。於是女王和她臣僕轉回本國去了。
14 Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000,
所羅門每年所得的金子共有六百六十六他連得。
15 osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.
另外還有商人和雜族的諸王,與國中的省長所進的金子。
16 Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka.
所羅門王用錘出來的金子打成擋牌二百面,每面用金子六百舍客勒;
17 Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.
又用錘出來的金子打成盾牌三百面,每面用金子三彌那,都放在黎巴嫩林宮裏。
18 Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri.
王用象牙製造一個寶座,用精金包裹。
19 Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse.
寶座有六層臺階,座的後背是圓的,兩旁有扶手,靠近扶手有兩個獅子站立。
20 Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse.
六層臺階上有十二個獅子站立,每層有兩個:左邊一個,右邊一個;在列國中沒有這樣做的。
21 Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni.
所羅門王一切的飲器都是金子的。黎巴嫩林宮裏的一切器皿都是精金的。所羅門年間,銀子算不了甚麼。
22 Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.
因為王有他施船隻與希蘭的船隻一同航海,三年一次,裝載金銀、象牙、猿猴、孔雀回來。
23 Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi.
所羅門王的財寶與智慧勝過天下的列王。
24 Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake.
普天下的王都求見所羅門,要聽上帝賜給他智慧的話。
25 Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu.
他們各帶貢物,就是金器、銀器、衣服、軍械、香料、騾馬,每年有一定之例。
26 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu.
所羅門聚集戰車馬兵,有戰車一千四百輛,馬兵一萬二千名,安置在屯車的城邑和耶路撒冷,就是王那裏。
27 Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri.
王在耶路撒冷使銀子多如石頭,香柏木多如高原的桑樹。
28 Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe.
所羅門的馬是從埃及帶來的,是王的商人一群一群按着定價買來的。
29 Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.
從埃及買來的車,每輛價銀六百舍客勒,馬每匹一百五十舍客勒。赫人諸王和亞蘭諸王所買的車馬,也是按這價值經他們手買來的。