< 1 Yohane 4 >
1 Anzanga okondedwa, musakhulupirire mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ikuchokera kwa Mulungu, chifukwa aneneri onama ambiri afalikira mʼdziko lapansi.
Ἀγαπητοί, μὴ παντὶ πνεύματι πιστεύετε, ἀλλὰ δοκιμάζετε τὰ πνεύματα, εἰ ἐκ τοῦ θεοῦ ἐστιν, ὅτι πολλοὶ ψευδοπροφῆται ἐξεληλύθασιν εἰς τὸν κόσμον.
2 Mungathe kuzindikira Mzimu wa Mulungu motere: Mzimu uliwonse umene umavomereza kuti Yesu Khristu anabwera mʼthupi, ndi wochokera kwa Mulungu,
ἐν τούτῳ γινώσκετε τὸ πνεῦμα τοῦ θεοῦ· πᾶν πνεῦμα ὃ ὁμολογεῖ Ἰησοῦν χριστὸν ἐν σαρκὶ ἐληλυθότα, ἐκ τοῦ θεοῦ ἐστιν.
3 koma mzimu uliwonse umene suvomereza Yesu, siwochokera kwa Mulungu. Uwu ndi mzimu wa wokana Khristu umene munawumva kuti ukubwera ndipo ngakhale tsopano wabwera kale mʼdziko lapansi.
καὶ πᾶν πνεῦμα ὃ μὴ ὁμολογεῖ τὸν Ἰησοῦν ἐκ τοῦ θεοῦ οὐκ ἔστιν· καὶ τοῦτό ἐστιν τὸ τοῦ ἀντιχρίστου, ὃ ἀκηκόατε ὅτι ἔρχεται, καὶ νῦν ἐν τῷ κόσμῳ ἐστὶν ἤδη.
4 Inu ana okondedwa, ndinu ochokera kwa Mulungu ndipo mwawagonjetsa aneneri onyengawa, chifukwa Iye amene ali mwa inu ndi wamkulu kuposa amene ali mʼdziko lapansi.
ὑμεῖς ἐκ τοῦ θεοῦ ἐστε, τεκνία, καὶ νενικήκατε αὐτούς, ὅτι μείζων ἐστὶν ὁ ἐν ὑμῖν ἢ ὁ ἐν τῷ κόσμῳ.
5 Aneneri onyengawa ndi ochokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake amayankhula za dziko lapansi, ndipo dziko lapansi limawamvera.
αὐτοὶ ἐκ τοῦ κόσμου εἰσίν· διὰ τοῦτο ἐκ τοῦ κόσμου λαλοῦσιν, καὶ ὁ κόσμος αὐτῶν ἀκούει.
6 Ife ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo aliyense amene amadziwa Mulungu amamvera zimene timayankhula. Koma aliyense amene sachokera kwa Mulungu samvera zimene timayankhula. Mmenemu ndiye mmene timasiyanitsira pakati pa mzimu wachoonadi ndi Mzimu wachinyengo.
ἡμεῖς ἐκ τοῦ θεοῦ ἐσμεν· ὁ γινώσκων τὸν θεὸν ἀκούει ἡμῶν· ὃς οὐκ ἔστιν ἐκ τοῦ θεοῦ οὐκ ἀκούει ἡμῶν. ἐκ τούτου γινώσκομεν τὸ πνεῦμα τῆς ἀληθείας καὶ τὸ πνεῦμα τῆς πλάνης.
7 Anzanga okondedwa, tiyeni tikondane wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimachokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi ndi mwana wa Mulungu ndipo amadziwa Mulungu.
Ἀγαπητοί, ἀγαπῶμεν ἀλλήλους, ὅτι ἡ ἀγάπη ἐκ τοῦ θεοῦ ἐστιν, καὶ πᾶς ὁ ἀγαπῶν ἐκ τοῦ θεοῦ γεγέννηται καὶ γινώσκει τὸν θεόν·
8 Aliyense amene alibe chikondi sadziwa Mulungu, chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
ὁ μὴ ἀγαπῶν οὐκ ἔγνω τὸν θεόν, ὅτι ὁ θεὸς ἀγάπη ἐστίν.
9 Mmene Mulungu anaonetsera chikondi chake pakati pathu ndi umu: Iye anatumiza Mwana wake mmodzi yekha ku dziko lapansi kuti mwa Iyeyo tikhale ndi moyo.
ἐν τούτῳ ἐφανερώθη ἡ ἀγάπη τοῦ θεοῦ ἐν ἡμῖν, ὅτι τὸν υἱὸν αὐτοῦ τὸν μονογενῆ ἀπέσταλκεν ὁ θεὸς εἰς τὸν κόσμον, ἵνα ζήσωμεν δι᾽ αὐτοῦ.
10 Chikondi ndi ichi: osati kuti ife ndife amene tinamukonda Mulungu, koma kuti Iyeyo ndiye amene anatikonda ndipo anatumiza Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
ἐν τούτῳ ἐστὶν ἡ ἀγάπη, οὐχ ὅτι ἡμεῖς ἠγαπήσαμεν τὸν θεόν, ἀλλ᾽ ὅτι αὐτὸς ἠγάπησεν ἡμᾶς, καὶ ἀπέστειλεν τὸν υἱὸν αὐτοῦ ἱλασμὸν περὶ τῶν ἁμαρτιῶν ἡμῶν.
11 Anzanga okondedwa, popeza Mulungu anatikonda chotere, ifenso tiyenera kukondana wina ndi mnzake.
ἀγαπητοί, εἰ οὕτως ὁ θεὸς ἠγάπησεν ἡμᾶς, καὶ ἡμεῖς ὀφείλομεν ἀλλήλους ἀγαπᾶν·
12 Palibe amene anaonapo Mulungu, koma tikakondana wina ndi mnzake, ndiye kuti Mulungu amakhala mwa ife ndipo chikondi chake chafika pachimake penipeni mwa ife.
θεὸν οὐδεὶς πώποτε τεθέαται· ἐὰν ἀγαπῶμεν ἀλλήλους, ὁ θεὸς ἐν ἡμῖν μένει, καὶ ἡ ἀγάπη αὐτοῦ τετελειωμένη ἐν ἡμῖν ἐστίν.
13 Ife tikudziwa kuti timakhala mwa Iye ndipo Iyeyo amakhala mwa ife chifukwa anatipatsa Mzimu wake.
ἐν τούτῳ γινώσκομεν ὅτι ἐν αὐτῷ μένομεν καὶ αὐτὸς ἐν ἡμῖν, ὅτι ἐκ τοῦ πνεύματος αὐτοῦ δέδωκεν ἡμῖν.
14 Ndipo taona ndipo tikuchitira umboni, kuti Atate anatuma Mwana wake kuti akhale Mpulumutsi wa dziko lapansi.
καὶ ἡμεῖς τεθεάμεθα καὶ μαρτυροῦμεν ὅτι ὁ πατὴρ ἀπέσταλκεν τὸν υἱὸν σωτῆρα τοῦ κόσμου.
15 Ngati aliyense avomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye ndipo iyeyo amakhala mwa Mulungu.
ὃς ἂν ὁμολογήσῃ ὅτι Ἰησοῦς ἐστιν ὁ υἱὸς τοῦ θεοῦ, ὁ θεὸς ἐν αὐτῷ μένει καὶ αὐτὸς ἐν τῷ θεῷ.
16 Tikudziwa ndipo timadalira chikondi chimene Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi. Aliyense amene amakhala moyo wachikondi, ali mwa Mulungu ndipo Mulungu amakhala mwa iye.
καὶ ἡμεῖς ἐγνώκαμεν καὶ πεπιστεύκαμεν τὴν ἀγάπην ἣν ἔχει ὁ θεὸς ἐν ἡμῖν. ὁ θεὸς ἀγάπη ἐστίν, καὶ ὁ μένων ἐν τῇ ἀγάπῃ, ἐν τῷ θεῷ μένει, καὶ ὁ θεὸς ἐν αὐτῷ.
17 Chikondi chafika pachimake penipeni pakati pathu, kotero kuti pa tsiku lachiweruzo tidzakhala olimba mtima chifukwa mʼdziko lapansi moyo wathu uli ngati wa Khristu.
Ἐν τούτῳ τετελείωται ἡ ἀγάπη μεθ᾽ ἡμῶν, ἵνα παῤῥησίαν ἔχωμεν ἐν τῇ ἡμέρᾳ τῆς κρίσεως, ὅτι καθὼς ἐκεῖνός ἐστιν καὶ ἡμεῖς ἐσμεν ἐν τῷ κόσμῳ τούτῳ.
18 Mulibe mantha mʼchikondi. Koma chikondi ndi changwiro chimachotsa mantha, chifukwa mantha amabwera chifukwa choopa chilango. Munthu amene ali ndi mantha, chikondi chake sichangwiro.
φόβος οὐκ ἔστιν ἐν τῇ ἀγάπῃ, ἀλλὰ ἡ τελεία ἀγάπη ἔξω βάλλει τὸν φόβον, ὅτι ὁ φόβος κόλασιν ἔχει· ὁ δὲ φοβούμενος οὐ τετελείωται ἐν τῇ ἀγάπῃ.
19 Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye anayamba kutikonda.
ἡμεῖς ἀγαπῶμεν, ὅτι αὐτὸς πρῶτος ἠγάπησεν ἡμᾶς.
20 Ngati wina anena kuti, “Ine ndimakonda Mulungu,” koma namadana ndi mʼbale wake ndi wabodza ameneyo. Pakuti aliyense amene sakonda mʼbale wake, amene akumuona, sangathenso kukonda Mulungu amene sanamuone.
ἐάν τις εἴπῃ ὅτι Ἀγαπῶ τὸν θεόν, καὶ τὸν ἀδελφὸν αὐτοῦ μισῇ, ψεύστης ἐστίν· ὁ γὰρ μὴ ἀγαπῶν τὸν ἀδελφὸν αὐτοῦ ὃν ἑώρακεν, τὸν θεὸν ὃν οὐχ ἑώρακεν οὐ δύναται ἀγαπᾶν·
21 Ndipo Iye anatipatsa lamulo lakuti: Aliyense amene amakonda Mulungu ayenera kukondanso mʼbale wake.
καὶ ταύτην τὴν ἐντολὴν ἔχομεν ἀπ᾽ αὐτοῦ, ἵνα ὁ ἀγαπῶν τὸν θεὸν ἀγαπᾷ καὶ τὸν ἀδελφὸν αὐτοῦ.