< 1 Yohane 3 >
1 Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye.
2 Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili.
3 Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera.
4 Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo.
5 Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo.
6 Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa.
7 Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama.
8 Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi.
9 Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.
10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake.
11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake.
12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama.
13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu.
14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa.
15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha. (aiōnios )
16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu.
17 Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu?
18 Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi.
19 Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu,
20 nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse.
21 Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu.
22 Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa.
23 Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira.
24 Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.