< 1 Akorinto 8 >
1 Tsopano za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano: Ife tidziwa kuti tonse tili ndi chidziwitso. Komatu chidziwitso chokha chimadzitukumula, koma chikondi ndicho chimapindulitsa.
2 Munthu amene amaganiza kuti amadziwa kanthu, ndiye kuti sakudziwa monga mmene amayenera kudziwira.
3 Koma munthu amene amakonda Mulungu amadziwika ndi Mulunguyo.
4 Choncho kunena za chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano; ife tikudziwa kuti mafano si kanthu nʼpangʼonongʼono pomwe pa dziko lapansi, ndiponso kuti palibe Mulungu wina koma mmodzi yekha.
5 Popeza kuti ngakhale pali yotchedwa milungu, kaya ndi kumwamba kapena pa dziko lapansi (poti ilipodi milungu yambirimbiri ndi ambuye ambirimbiri),
6 koma kwa ife pali Mulungu mmodzi yekha, Atate, zinthu zonse zinachokera mwa Iye ndipo ndife ake. Komanso pali Ambuye mmodzi Yesu Khristu kumene zinthu zonse zinachokera ndipo mwa Iye ife tili ndi moyo.
7 Koma saliyense amadziwa zimenezi. Alipo ena ozolowera mafano kwambiri mwakuti akadya chakudya chotere amaganiza kuti chakudyacho chinaperekedwa nsembe kwa mafano. Ndiye poti chikumbumtima chawo nʼchofowoka chimadetsedwadi.
8 Koma chakudya sichitisendeza kufupi ndi Mulungu. Tikapanda kudya si vuto, tikadya sitisinthikanso.
9 Komabe samalani kuti ufulu wanu ochita zinthu usafike pokhumudwitsa ofowoka.
10 Pakuti ngati aliyense wachikumbumtima chofowoka akakuonani achidziwitsonu mukudya mʼnyumba yopembedzera mafano, kodi iyeyo sichidzamulimbitsa mtima kuti azidya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano?
11 Kotero kuti chifukwa cha chidziwitso chanu mʼbale wofowokayu amene chifukwa cha iye, Khristu anafa, wawonongeka chifukwa cha chidziwitso chanu.
12 Mukamachimwira abale anu motere ndikuwawonongera chikumbumtima chawo chofowokacho, mukuchimwira Khristu.
13 Nʼchifukwa chake ngati zimene ine ndimadya zichititsa mʼbale wanga kugwa mu tchimo, sindidzadyanso chakudyacho kuti mʼbaleyo ndisamuchimwitse. (aiōn )