< 1 Akorinto 7 >
1 Tsopano pa zinthu zomwe munandilembera nʼkwabwino kuti munthu asakwatire.
2 Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake.
3 Mwamuna akwaniritse udindo wake wa pa banja kwa mkazi wake, ndipo chimodzimodzi mkazi kwa mwamuna wake.
4 Thupi la mkazi wokwatiwa si la iye mwini yekha koma ndi la mwamuna wakenso. Momwemonso, thupi la mwamuna si la iye mwini yekha koma ndi la mkazi wakenso.
5 Musamakanizane, pokhapokha mutagwirizana awiri kuti mwakanthawi mudzipereke kumapemphero. Kenaka mukhalirenso pamodzi kuopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cholephera kudziretsa.
6 Ndikunena zimenezi mokulolani chabe osati mokulamulani.
7 Ine ndikanakonda anthu akanakhala ngati ine. Koma poti munthu aliyense ali ndi mphatso yakeyake yochokera kwa Mulungu, wina mphatso yake, wina yakenso.
8 Tsono kwa osakwatira onse, ndi akazi amasiye ndikuti, ndi bwino kwa iwo kukhala osakwatira monga mmene ndilili inemu.
9 Koma ngati sangathe kudziretsa, akwatire, popeza ndi bwino kukwatira kusiyana ndi kudzizunza ndi chilakolako.
10 Kwa amene ali pa banja ndikupatsani lamulo ili (osati langa koma la Ambuye): Mkazi asalekane ndi mwamuna wake.
11 Koma ngati atatero, asakwatiwenso, apo ayi, abwerere kwa mwamuna wakeyo. Ndipo mwamuna asaleke mkazi wake.
12 Kwa ena onse ndikunena izi (ineyo osati Ambuye); ngati mʼbale wina ali ndi mkazi wosakhulupirira ndipo mkaziyo walola kukhala pa banja ndi mʼbaleyo, ameneyo asamuleke.
13 Ngati mayi wina ali ndi mwamuna wosakhulupirira ndipo mwamunayo walola kukhala pa banja ndi mayiyo, ameneyo asamuleke.
14 Pakuti mwamuna wosakhulupirirayo amayeretsedwa chifukwa cha mkazi wakeyo, ndipo mkazi wosakhulupirira amayeretsedwa chifukwa cha mwamuna wokhulupirirayo. Kupanda apo ana anu akanakhala odetsedwa, koma mmene zililimu ndi oyeretsedwa.
15 Koma ngati wosakhulupirira achoka, mulekeni achoke. Zikatero ndiye kuti mwamuna kapena mkazi wokhulupirirayo sali womangikanso. Mulungu anatiyitana kuti tikhale mu mtendere.
16 Kodi iwe, mkazi, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mwamuna wako? Kapena iwe, mwamuna, ungadziwe bwanji kuti mwina nʼkupulumutsa mkazi wako?
17 Koma aliyense akhale moyo umene Ambuye anamupatsa, umene Mulungu anamuyitanira. Ili ndiye lamulo limene ndalikhazikitsa mʼmipingo yonse.
18 Ngati pamene munthu amayitanidwa anali atachita mdulidwe, asavutike nʼkubisa za mdulidwe wakewo. Ngatinso pamene munthu amayitanidwa nʼkuti asanachite mdulidwe, asachite mdulidwe.
19 Mdulidwe si kanthu, kusachita mdulidwe si kanthunso. Chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu.
20 Aliyense akhale monga analili pamene Mulungu anamuyitana.
21 Kodi munali kapolo pamene Mulungu anakuyitanani? Musavutike nazo zimenezi. Koma ngati mutapeza mwayi woti mulandire ufulu, ugwiritseni ntchito mwayiwo.
22 Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu.
23 Munagulidwa ndi mtengowapatali, choncho musakhalenso akapolo a anthu.
24 Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analili pamene Mulungu anamuyitana.
25 Tsopano za anamwali: Ine ndilibe lamulo lochokera kwa Ambuye, koma ndipereka maganizo anga monga ngati munthu amene mwachifundo cha Ambuye ndine wodalirika.
26 Chifukwa cha masautso a masiku ano, ndikuganiza kuti nʼkwabwino kuti munthu akhale monga mmene alili.
27 Kodi ndinu wokwatira? Musalekane. Kodi ndinu wosakwatira? Musafunefune mkazi.
28 Komabe ngati mukwatira simunachimwe; ndipo ngati namwali akwatiwa sanachimwenso. Koma amene walowa mʼbanja adzakumana ndi zovuta zambiri mʼmoyo uno, ndipo sindikufuna kuti inu mukumane ndi zovutazi.
29 Abale, chimene ndikutanthauza nʼchakuti nthawi yatha. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale ngati sanakwatire.
30 Amene akulira akhale monga ngati sakulira. Amene akukondwa akhale ngati sakukondwa. Amene akugula zinthu akhale ngati alibe zinthuzo.
31 Amene akugwiritsa ntchito zinthu za dziko lapansi lino, akhale ngati sizikuwakhudza. Pakuti dziko lapansi lino mmene lilirimu, likupita.
32 Ine ndikufuna kuti mumasuke ku nkhawa zanu. Munthu wosakwatira amangolabadira za Ambuye, mmene angakondweretsere Ambuyewo.
33 Koma wa pa banja amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mkazi wake,
34 ndipo chifukwa ichi amatanganidwa kwambiri. Mkazi wosakwatiwa kapena namwali, amalabadira za Ambuye. Cholinga chake ndi kudzipereka kwa Ambuye mʼthupi ndi mu uzimu momwe. Koma mkazi wokwatiwa amalabadira za dziko lapansi lino, mmene angakondweretsere mwamuna wake.
35 Ndikunena izi kufuna kuthandiza inu nomwe osati kukupanikizani. Ine ndikufuna mukhale moyenera mosadzigawa pa kudzipereka kwanu kwa Ambuye.
36 Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi.
37 Koma ngati wina motsimikiza mtima wake, popanda womukakamiza, koma akuchita mwa chifuniro chake, ndipo watsimikiza mtima kuti samukwatira namwaliyo, munthuyu akuchitanso chokhoza.
38 Choncho amene akukwatira namwali amene ali naye pa ubwenzi, akuchita bwino, koma amene sangakwatire namwaliyo akuchita bwino koposa.
39 Mkazi amamangika ndi lamulo la ukwati nthawi zonse pamene mwamuna wake ali ndi moyo. Koma mwamuna wake akamwalira, ali ndi ufulu kukwatiwa ndi wina aliyense amene akumufuna, koma mwamunayo akhale wa mwa Ambuye.
40 Mʼmaganizo anga, mkaziyo adzakhala wokondwa koposa ngati atangokhala wosakwatiwa. Ndipo ndikuganiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu.