< 1 Akorinto 3 >

1 Ndipo abale sindikanakuyankhulani ngati auzimu koma adziko lapansi, makanda chabe mwa Khristu.
And I, brothers, could not address you as spiritual, but as fleshly, as infants in Messiah.
2 Ndinakupatsani mkaka osati chakudya cholimba pakuti munali musanakonzeke kuchilandira. Zoonadi, simunakonzekebe.
I fed you with milk, not solid food, for you weren't yet ready. And even now you are still not ready,
3 Mukanali adziko lapansi. Pakuti pakati panu pali kaduka ndi kukangana, kodi si inu a dziko lapansi? Kodi simukuchita ngati anthu wamba?
for you are still fleshly. For insofar as there is jealousy and strife among you, are you not fleshly, and living by human standards?
4 Pamene wina anena kuti, “Ine ndimatsatira Paulo,” ndipo wina akuti, “Ine ndimatsatira Apolo,” Kodi si inu akunja?
For when one says, "I follow Paul," and another, "I follow Apollos," are you not merely human?
5 Ndiponso kodi Apolo ndi ndani? Nanga Paulo ndi ndani? Otumikira chabe, omwe kudzera mwa iwo inu munakhulupirira monga Ambuye anawagawira aliyense ntchito yake.
What then is Apollos? And what is Paul? Servants through whom you believed, and each as the Lord gave to him.
6 Ine ndinadzala mbewu, Apolo anayithirira, koma Mulungu ndiye anayikulitsa.
I planted. Apollos watered. But God made it grow.
7 Choncho kuphatikiza iye wodzala ndi iye wothirira, onse sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amakulitsa zinthu.
So then neither he who plants is anything, nor he who waters, but God who makes it grow.
8 Munthu wodzala ndi munthu wothirira ali ndi cholinga chimodzi, ndipo aliyense adzapatsidwa mphotho molingana ndi ntchito yake.
Now he who plants and he who waters are the same, but each will receive his own reward according to his own labor.
9 Pakuti ife ndife antchito anzake a Mulungu; inu ndinu munda wa Mulungu, Nyumba ya Mulungu.
For we are God's fellow workers. You are God's field, God's building.
10 Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira.
According to the grace of God which was given to me, as a wise master builder I laid a foundation, and another builds on it. But let each one be careful how he builds on it.
11 Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu.
For no one can lay any other foundation than that which has been laid, which is Jesus (the) Messiah.
12 Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu,
But if anyone builds on the foundation with gold, silver, costly stones, wood, hay, or straw;
13 ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense.
each man's work will be revealed. For the Day will declare it, because it is revealed in fire; and the fire itself will test what sort of work each man's work is.
14 Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake.
If any man's work remains which he built on it, he will receive a reward.
15 Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.
If any man's work is burned, he will suffer loss, but he himself will be saved, but as through fire.
16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Do you not know that you are a temple of God, and that God's Spirit lives in you?
17 Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.
If anyone destroys the temple of God, God will destroy him; for God's temple is holy, which you are.
18 Choncho musadzinyenge. Ngati wina wa inu akuganiza kuti ndi wanzeru pa mulingo wa mʼbado uno, ayenera kukhala “wopusa” kuti athe kukhala wanzeru. (aiōn g165)
Let no one deceive himself. If anyone thinks that he is wise among you in this age, let him become a fool, that he may become wise. (aiōn g165)
19 Pakuti nzeru ya dziko lapansi ndi yopusa pamaso pa Mulungu. Monga kwalembedwera kuti, “Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo,”
For the wisdom of this world is foolishness with God. For it is written, "He traps the wise in their craftiness."
20 ndiponso, “Ambuye amadziwa kuti maganizo a wanzeru ndi opandapake.”
And again, "The Lord knows the thoughts of the wise, that they are futile."
21 Choncho, wina asanyadire anthu chabe! Zonse ndi zanu,
Therefore let no one boast about people. For all things are yours,
22 kaya Paulo kapena Apolo kapena Kefa kapena dziko lapansi, kapena moyo, kapena imfa, kapena tsopano, kapena mʼtsogolo, zonse ndi zanu,
whether Paul, or Apollos, or Cephas, or the world, or life, or death, or things present, or things to come. All are yours,
23 ndipo inu ndinu a Khristu, ndipo Khristu ndi wa Mulungu.
and you are Messiah's, and Messiah is God's.

< 1 Akorinto 3 >