< 1 Akorinto 2 >
1 Pamene ndinabwera kwa inu, abale, sindinabwere ndi luntha lodziwa kuyankhula kapena nzeru zapamwamba pamene ndinachitira umboni chinsinsi cha Mulungu.
Og jeg, Brødre! da jeg kom til eder, kom jeg ikke og forkyndte eder Guds Vidnesbyrd med Stormægtighed i Tale eller i Visdom;
2 Pakuti ndinatsimikiza pamene ndinali ndi inu kuti ndisadziwe kanthu kena kupatula Yesu Khristu wopachikidwayo.
thi jeg agtede ikke at vide noget iblandt eder uden Jesus Kristus og ham korsfæstet;
3 Ndinabwera kwa inu wofowoka ndi wamantha, ndiponso wonjenjemera kwambiri.
og jeg færdedes hos eder i Svaghed og i Frygt og megen Bæven,
4 Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu,
og min Tale og min Prædiken var ikke med Visdoms overtalende Ord, men med Aands og Krafts Bevisning,
5 kuti chikhulupiriro chanu chisatsamire pa nzeru ya anthu koma pa mphamvu za Mulungu.
for at eders Tro ikke skulde bero paa Menneskers Visdom, men paa Guds Kraft.
6 Komabe ife timayankhula uthenga wa nzeru kwa okhwima, koma osati ndi nzeru ya mʼbado uno kapena ya olamula a mʼbado uno, amene mphamvu yawo ikutha. (aiōn )
Dog, Visdom tale vi iblandt de fuldkomne, men en Visdom, der ikke stammer fra denne Verden, ikke heller fra denne Verdens Herskere, som blive til intet; (aiōn )
7 Ayi, ife timayankhula za nzeru yobisika ya Mulungu, nzeru imene inabisidwa ndipo imene Mulungu anatikonzera mu ulemerero wathu isanayambe nthawi. (aiōn )
men vi tale Visdom fra Gud, den hemmelige, den, som var skjult, som Gud før Verdens Begyndelse forudbestemte til vor Herlighed, (aiōn )
8 Palibe olamulira aliyense wa mʼbado uno amene anamumvetsetsa popeza anakamumvetsetsa sakanamupachika Ambuye wa ulemerero. (aiōn )
hvilken ingen af denne Verdens Herskere har erkendt; thi havde de erkendt den, havde de ikke korsfæstet Herlighedens Herre; (aiōn )
9 Komabe monga zalembedwa kuti, “Palibe diso linaona, palibe khutu linamva, palibe amene anaganizira, zimene Mulungu anakonzera amene amukonda”
men, som der er skrevet: „Hvad intet Øje har set, og intet Øre har hørt, og ikke er opkommet i noget Menneskes Hjerte, hvad Gud har beredt dem, som elske ham.‟
10 koma Mulungu waululira ife mwa Mzimu wake. Mzimu amafufuza zinthu zonse, ndi zozama za Mulungu zomwe.
Men os aabenbarede Gud det ved Aanden; thi Aanden ransager alle Ting, ogsaa Guds Dybder.
11 Kodi ndani mwa anthu angadziwe maganizo a munthu wina, kupatula mzimu wa munthuyo wokhala mʼkati mwake? Chimodzimodzinso palibe amene adziwa maganizo a Mulungu kupatula Mzimu wa Mulunguyo.
Thi hvilket Menneske ved, hvad der er i Mennesket, uden Menneskets Aand, som er i ham? Saaledes har heller ingen erkendt, hvad der er i Gud, uden Guds Aand.
12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere.
Men vi have ikke faaet Verdens Aand, men Aanden fra Gud, for at vi kunne vide, hvad der er os skænket af Gud;
13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu.
og dette tale vi ogsaa, ikke med Ord, lærte af menneskelig Visdom, men med Ord, lærte af Aanden, idet vi tolke aandelige Ting med aandelige Ord.
14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu.
Men det sjælelige Menneske tager ikke imod de Ting, som høre Guds Aand til; thi de ere ham en Daarskab, og han kan ikke erkende dem, thi de bedømmes aandeligt.
15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense.
Men den aandelige bedømmer alle Ting, selv derimod bedømmes han af ingen.
16 Pakuti “Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye, kuti akhoza kumulangiza Iye.” Koma tili nawo mtima wa Khristu.
Thi hvem har kendt Herrens Sind, saa han skulde kunne undervise ham? Men vi have Kristi Sind.