< 1 Akorinto 13 >

1 Ngakhale nditamayankhula mʼmalilime a anthu ndi a angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chinganga chaphokoso kapena ngati chitsulo chosokosera.
martyasvargIyANAM bhAShA bhAShamANo. ahaM yadi premahIno bhaveyaM tarhi vAdakatAlasvarUpo ninAdakAribherIsvarUpashcha bhavAmi|
2 Ngati ndili ndi mphatso ya uneneri, nʼkumazindikira zinsinsi ndi kudziwa zonse, ndipo ngati ndili ndi chikhulupiriro chosuntha mapiri, koma wopanda chikondi, ine sindili kanthu.
apara ncha yadyaham IshvarIyAdeshADhyaH syAM sarvvANi guptavAkyAni sarvvavidyA ncha jAnIyAM pUrNavishvAsaH san shailAn sthAnAntarIkarttuM shaknuyA ncha kintu yadi premahIno bhaveyaM tarhyagaNanIya eva bhavAmi|
3 Ngati ndipereka zanga zonse kwa osauka ndi kupereka thupi langa kuti alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ine sindipindula kanthu.
aparaM yadyaham annadAnena sarvvasvaM tyajeyaM dAhanAya svasharIraM samarpayeya ncha kintu yadi premahIno bhaveyaM tarhi tatsarvvaM madarthaM niShphalaM bhavati|
4 Chikondi nʼcholeza mtima, chikondi nʼchokoma mtima, chilibe nsanje, sichidzikuza, sichidzitamandira.
prema chirasahiShNu hitaiShi cha, prema nirdveSham ashaThaM nirgarvva ncha|
5 Chikondi chilibe mwano, sichodzikonda, sichipsa mtima msanga, sichisunga mangawa.
aparaM tat kutsitaM nAcharati, AtmacheShTAM na kurute sahasA na krudhyati parAniShTaM na chintayati,
6 Chikondi sichikondwera ndi zoyipa koma chimakondwera ndi choonadi.
adharmme na tuShyati satya eva santuShyati|
7 Chimatchinjiriza nthawi zonse, chimakhulupirika nthawi zonse, chimakhala ndi chiyembekezo nthawi zonse, chimapirira nthawi zonse.
tat sarvvaM titikShate sarvvatra vishvasiti sarvvatra bhadraM pratIkShate sarvvaM sahate cha|
8 Chikondi ndi chosatha. Koma mphatso ya uneneri idzatha, pamene pali kuyankhula malilime adzatha, pamene pali chidziwitso chidzatha.
premno lopaH kadApi na bhaviShyati, IshvarIyAdeshakathanaM lopsyate parabhAShAbhAShaNaM nivarttiShyate j nAnamapi lopaM yAsyati|
9 Pakuti timadziwa zinthu pangʼono chabe ndipo timanenera pangʼono chabe.
yato. asmAkaM j nAnaM khaNDamAtram IshvarIyAdeshakathanamapi khaNDamAtraM|
10 Koma changwiro chikadzaoneka ndipo chopereweracho chidzatha.
kintvasmAsu siddhatAM gateShu tAni khaNDamAtrANi lopaM yAsyante|
11 Pamene ndinali mwana ndinkayankhula ngati mwana, ndinkaganiza ngati mwana, ndinkalingalira ngati mwana. Koma nditakula, zonse zachibwana ndinazisiya.
bAlyakAle. ahaM bAla ivAbhAShe bAla ivAchintaya ncha kintu yauvane jAte tatsarvvaM bAlyAcharaNaM parityaktavAn|
12 Pakuti tsopano tiona zinthu mosaoneka bwino ngati mʼgalasi loonera; kenaka tidzaziona maso ndi maso. Tsopano ndidziwa mosakwanira koma kenaka ndidzadziwa mokwanira, monga mmene Mulungu akundidziwira ine.
idAnIm abhramadhyenAspaShTaM darshanam asmAbhi rlabhyate kintu tadA sAkShAt darshanaM lapsyate| adhunA mama j nAnam alpiShThaM kintu tadAhaM yathAvagamyastathaivAvagato bhaviShyAmi|
13 Ndipo tsopano zatsala zinthu zitatu: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.
idAnIM pratyayaH pratyAshA prema cha trINyetAni tiShThanti teShAM madhye cha prema shreShThaM|

< 1 Akorinto 13 >