< 1 Akorinto 11 >

1 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.
Become followers of me, as I also [am] of Christ.
2 Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani.
And I praise you, brothers, that in all things you remember me, and according as I delivered to you, you keep the deliverances,
3 Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu.
and I wish you to know that the Christ is the head of every man, and the head of a woman is the husband, and the head of Christ is God.
4 Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo.
Every man praying or prophesying, having the head covered, dishonors his head,
5 Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake.
and every woman praying or prophesying with the head uncovered, dishonors her own head, for it is one and the same thing with her being shaven,
6 Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake.
for if a woman is not covered—then let her be shorn, and if [it is] a shame for a woman to be shorn or shaven—let her be covered;
7 Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna.
for a man, indeed, ought not to cover the head, being the image and glory of God, and a woman is the glory of a man,
8 Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna.
for a man is not of a woman, but a woman [is] of a man,
9 Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.
for also was a man not created because of the woman, but a woman because of the man;
10 Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake.
because of this the woman ought to have [a token of] authority on the head, because of the messengers;
11 Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi.
but neither [is] a man apart from a woman, nor a woman apart from a man, in the LORD,
12 Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu.
for as the woman [is] of the man, so also the man [is] through the woman, and all the things [are] of God.
13 Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu?
Judge in your own selves: is it seemly for a woman to pray to God uncovered?
14 Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali,
Does not even nature itself teach you, that if a man indeed has long hair, it is a dishonor to him?
15 koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu.
And a woman, if she has long hair, it is a glory to her, because the hair has been given to her instead of a covering;
16 Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa.
and if anyone thinks to be contentious, we have no such custom, neither the assemblies of God.
17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino.
And declaring this, I give no praise, because you do not come together for the better, but for the worse;
18 Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona.
for first, indeed, coming together in an assembly, I hear of divisions being among you, and I partly believe [it],
19 Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu.
for it is also necessary for sects to be among you, that those approved may become visible among you;
20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye.
you, then, coming together at the same place—it is not to eat the LORD’s Dinner;
21 Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera.
for each takes his own dinner before in the eating, and one is hungry, and another is drunk;
22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni.
why, do you not have houses to eat and to drink in? Or do you despise the Assembly of God, and shame those not having? What may I say to you? Will I praise you in this? I do not praise!
23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi.
For I received from the LORD that which I also delivered to you, that the Lord Jesus in the night in which He was delivered up, took bread,
24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.”
and having given thanks, He broke, and said, “Take, eat, this is My body that is being broken for you; do this—to the remembrance of Me.”
25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.”
In like manner also the cup after the supping, saying, “This cup is the New Covenant in My blood; do this, as often as you may drink [it]—to the remembrance of Me”;
26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso.
for as often as you may eat this bread, and may drink this cup, you show forth the death of the LORD—until He may come;
27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye.
so that whoever may eat this bread or may drink the cup of the LORD unworthily, he will be guilty of the body and blood of the LORD:
28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi.
and let a man be proving himself, and so let him eat of the bread, and let him drink of the cup;
29 Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe.
for he who is eating and drinking unworthily, he eats and drinks judgment to himself—not discerning the body of the LORD.
30 Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo.
Because of this many [are] weak and sickly among you, and many sleep;
31 Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso.
for if we were discerning ourselves, we would not be being judged,
32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.
and being judged by the LORD, we are disciplined, that we may not be condemned with the world;
33 Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane.
so then, my brothers, coming together to eat, wait for one another;
34 Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo. Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.
and if anyone is hungry, let him eat at home, that you may not come together to judgment; and the rest, whenever I may come, I will arrange.

< 1 Akorinto 11 >