< 1 Akorinto 10 >
1 Pakuti sindikufuna kuti inu mukhale osadziwa zenizeni, abale, kuti makolo athu anatsogozedwa ndi mtambo ndikuti onse anawoloka nyanja.
2 Ndipo onse anabatizidwa mwa Mose mu mtambo ndi mʼnyanja.
3 Onse anadya chakudya chimodzi chauzimu
4 ndipo anamwa chakumwa chimodzi chauzimu; popeza anamwa kuchokera mʼthanthwe lomwe anayenda nalo, ndipo thanthwe limeneli linali Khristu.
5 Ngakhale zinali choncho, Mulungu sanakondwere ndi ambiri a iwo, motero ambiri mwa iwo anafera mʼchipululu.
6 Tsono zinthu izi zinachitika kuti zikhale chitsanzo, kuti ife tisayike mitima yathu pa zinthu zoyipa monga anachitira makolo athuwo.
7 Musakhale anthu opembedza mafano, monga analili ena mwa iwo. Pakuti zalembedwa kuti, “Anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo.”
8 Tisachite chigololo monga ena mwa iwo anachitira ndipo tsiku limodzi anafapo anthu 23,000.
9 Tisamuyese Khristu, monga ena mwa iwo anachitira ndipo anaphedwa ndi njoka.
10 Ndipo osamawiringula, monga ena mwa iwo anachitira naphedwa ndi mngelo wowononga.
11 Zinthu izi zinawachitikira kuti zikhale chitsanzo ndipo zinalembedwa kuti zikhale chenjezo kwa ife, amene tiyandikira nthawi ya kutha kwa zonse. (aiōn )
12 Choncho, ngati mukuganiza kuti mwayima mwamphamvu, samalani mungagwe!
13 Palibe mayesero amene mwakumana nawo oposa amene anthu ena onse anakumana nawo. Mulungu ngokhulupirika; sadzalola kuti inu muyesedwe koposa muyeso umene mutha kupirira. Koma pamene mwayesedwa, Iyenso adzakupatsani njira yopambanira mayeserowo.
14 Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano.
15 Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi.
16 Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu?
17 Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.
18 Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo?
19 Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse?
20 Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo.
21 Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda.
22 Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?
23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza.
24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu.
26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”
27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu.
28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima.
29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina?
30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?
31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu.
33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.